Gwilitsilani Nchito Kapepala Katsopano Konena za Webu Saiti Yathu
Kapepala kameneka kali ndi mutu wakuti, Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo? Kumbuyo kwa kapepalaka kuli mafunso atatu. Ngati mwai ulola mungapemphe mwininyumba kuti asankhe funso limene lamucititsa cidwi. Ndiyeno muonetseni pa Webusaiti yathu kuti apeze yankho pamalo olembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO. Pa Webusaiti imeneyi adzapezanso mayankho a mafunso awa: Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Ndipo lina n’lakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita zinthu ziti?
Muzinyamula tumapepala tumenetu kulikonse kuti muthandize anthu kudziŵa zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo lathu labwino mu Ufumu wa Mulungu.