Webu Saiti Yathu—Igwilitsileni Nchito Kuthandiza Munthu Amene Amalankhula Cinenelo Cina
Muonetseni Webu Saiti Yathu: Muonetseni mmene angagwilitsile nchito mndandanda wa “Cinenelo ca Webu Saiti” kuti apite pa Webu Saiti ya cinenelo cake. (Zinenelo zina zili ndi mbali yocepa cabe ya Webu saiti imeneyi.)
Muonetseni Tsamba la pa Webu Saiti la m’Cinenelo Cake: Muonetseni tsamba limodzi la zofalitsa zathu, monga buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa kapena kapepala ka uthenga kakuti Mayankho Azoona. Sankhani cinenelo ca mwininyumba pa kamutu kakuti “Ŵelengani mu.”
Mupempheni Kuti Amvetsele Nkhani: Pezani nkhani imene munthu angamvetsele m’cinenelo cake ndipo iyatseni kuti aimvetsele.—Pitani pa “Publications/Books ndi Brochures” kapena pa “Publications/Magazines.”
Kulalikila Ogontha: Mukapeza munthu wogontha, muonetseni vidiyo yoonetsa munthu akuŵelenga Baibo, buku, kabuku, kapena kapepala ka uthenga m’cinenelo ca manja.—Pitani pa “Publications/Sign Language.”
[Cithunzi papeji 6]
(Kuti muone mau onse, pitani ku cofalitsa)
Iyeseni
1 Dinizani ▸ kuti mumvetsele nkhani imene mwasankha (ngati ilipo m’cinenelo canu) kapena dinizani pa “Download Options” kuti mutenge cofalitsa.
2 Sankhani cinenelo cina pa kamutu kakuti “Ŵelengani mu,” kuti mumuonetse tsamba limenelo mu cinenelo cimene mwasankha.
3 Dinizani batani la “Next” kapena linki pa “Table of Contents” kuti muŵelenge nkhani ina.