Gwilitsilani Nchito Mphamvu ya Mau a Mulungu mu Ulaliki
Munthu akatilola kukamba naye za uthenga wabwino, timagwilitsila nchito bwino mwai umenewo ndipo timalola mphamvu ya Mau a Mulungu kugwila nchito mwa kuŵelenga m’Baibulo mwenimwenimo. Mfundo imeneyi inagogomezedwa caka catha pa msonkhano wapadela. Woyang’anila dela anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Gwilitsilani Nchito Mphamvu ya Mau a Mulungu mu Ulaliki.” Kodi mukumbukila mfundo zazikulu za m’nkhaniyo?
N’cifukwa ciani mau a Yehova ndi amphamvu kwambili kuposa mau athu?—2 Tim. 3:16, 17.
Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi maganizo abwino, zolinga zabwino komanso makhalidwe abwino?—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, tsa. 27, ndime 7.
Tikamaŵelengela anthu malemba mu ulaliki, kodi tingagwilitsile nchito motani Mau a Mulungu m’njila yakuti aziwalemekeza?—Onani buku la Sukulu ya Utumiki pa tsa. 148, ndime 3-4 ndi Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013 tsa. 6, ndime 8.
N’cifukwa ciani tiyenela kufotokoza ndi kukambilana ndi anthu malemba amene taŵelenga? Nanga tingacite bwanji zimenezi?—Mac. 17:2, 3. Onani Buku la Sukulu ya Utumiki tsa. 154, ndime 4 mpaka tsa. 156, ndime 5.