Maulaliki Acitsanzo
NSANJA YA MLONDA March-April
“Anthu ena sadziŵa kuti m’Baibulo muli malangizo amene angawathandize pa nchito imene amagwila. Onani zimene vesi ili limanena. [Ŵelengani Mlaliki 3:12] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kupeza cimwemwe pa nchito yanu. Kodi mungakonde kuliŵelenga?”
Galamukani! May
“Kodi muganiza kuti n’zotheka kukhala m’dziko lopanda umphawi komanso mmene anthu adzakhala ndi nyumba zabwino? [Yembekezani yankho.] Onani zimene Mulungu watilonjeza pa nkhani imeneyi. [Ŵelengani Yesaya 65:21-22.] Galamukani! iyi ifotokoza mmene Mulungu adzakwanilitsila cifunilo cake kwa anthu pa dziko ndi zimene ife tingacite kuti tidzakhalemo.”