LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/15 tsa. 1
  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Habakuku

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Habakuku
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Dalilani Yehova Kuti Mukhalebe na Moyo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Khalanibe Achelu ndi Okangalika Kuuzimu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 12/15 tsa. 1

Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Habakuku

1. N’cifukwa ciani tingamve monga mmene mneneli Habakuku anamvelela?

1 Pamene tikuona zinthu zoipa zikuonjezeka m’dzikoli, tingamve monga mmene Habakuku anamvelela. Iye anafunsa Yehova kuti: “N’cifukwa ciani mukundicititsa kuona zinthu zopweteka? N’cifukwa ciani mukupitiliza kuyang’ana khalidwe loipa?” (Hab. 1:3; 2 Tim. 3:1, 13) Kusinkhasinkha mau a Habakuku ndi citsanzo cake cabwino, kudzatithandiza kupilila pamene tikuyembekezela tsiku la ciweluzo la Yehova.—2 Pet. 3:7.

2. Kodi tingaonetse bwanji kuti tikukhala mwa cikhulupililo masiku ano?

2 Khalani mwa Cikhulupililo: M’malo mokhumudwa ndi zinthu zoipa zimene zinali kumucitikila, Habakuku anakhalabe maso mwakuuzimu ndi wacangu. (Hab. 2:1) Yehova anatsimikizila mneneliyu kuti mau Ake adzakwanilitsidwa panthawi yoyenela, ndi kuti “wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa cikhulupililo cake.” (Hab. 2:2-4) Kodi zimenezi zitanthauza ciani kwa Akristu amene akukhala m’masiku otsiliza? Cofunika kwambili ndi kukhala wotsimikizila kuti mapeto adzafika kuposa kudziŵa kuti adzafika liti. Cikhulupililo cimatithandiza kukhalabe maso ndi kuika utumiki wathu pamalo oyamba.—Aheb. 10:38, 39.

3. N’cifukwa ciani tiyenela kukhalabe osangalala potumikila Yehova?

3 Kondwelani mwa Yehova: Pamene Gogi wa kudziko la Magogi adzaukila anthu a Yehova, cikhulupililo cathu cidzayesedwa. (Ezek. 38:2, 10-12) Nthawi zonse nkhondo imabweletsa mavuto, ngakhalenso kwa anthu amene amapambana. Cakudya cingathe, katundu angaonongeke, ndipo moyo wa anthu ungakhale wovuta kwambili. Kodi tidzacita ciani panthawi yovuta ngati imeneyo? Habakuku anadziŵa kuti adzakumana ndi mavuto. Koma iye anatsimikiza mtima kukhalabe wosangalala mwa Yehova. (Hab. 3:16-19) Nafenso “cimwemwe cimene Yehova amapeleka” cidzatithandiza kupilila mayeselo a mtsogolo.—Neh. 8:10; Aheb. 12:2.

4. Ndi mwai wotani umene tili nao panthawi ino ndiponso mtsogolo?

4 Anthu amene Yehova adzapulumutsa pa tsiku lake la ciweluzo limene likubwela, adzapitilizabe kuphunzitsidwa ndi Mulungu. (Hab. 2:14) Anthu amene adzaukitsidwa naonso adzaphunzila za Yehova. Pakali pano, tiyeni tizigwilitsa nchito mpata uliwonse kuuza ena za Yehova ndi nchito zake zodabwitsa.—Sal. 34:1; 71:17.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani