CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | NAHUMU 1–HABAKUKU 3
Khalanibe Achelu ndi Okangalika Kuuzimu
Hab. 1:5, 6
Kwa Ayuda, zakuti Ababulo adzaononga dziko lawo mwina zinaoneka zosatheka. Tikutelo cifukwa Ayuda anali kuthandizidwa na Aiguputo, ndipo Aiguputowo anali na mphamvu kuposa Akasidi. Komanso, Ayuda ambili anali kuona kuti n’zosatheka kuti Yehova alole Yerusalemu na kacisi wake kuwonongedwa. Ngakhale n’conco, ulosi unali kudzakwalitsika ndithu, ndipo Habakuku anafunika kuyembekezelabe pokhala wachelu ndiponso wokangalika kuuzimu.
N’ciani cimanitsimikizila kuti mapeto a dzikoli ali pafupi?
Ningakhale bwanji wachelu komanso wokangalika kuuzimu?