LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 January tsa. 6
  • Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA:
  • MMENE TINGACITILE
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 January tsa. 6

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki​—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA:

Tifuna kuthilila mbeu za coonadi zimene timabyala. (1 Akor. 3:6) Tikapeza munthu wacidwi, zimakhala bwino kusiya funso limene tingayankhe paulendo wotsatila. Izi zidzathandiza mwini nyumba kuti akulitse cidwi, ndipo zidzatithandizanso kukonzekela bwino ulendo wobwelelako. Tikabwelelako, tingamuuze kuti tabwela kudzayankha funso limene tinasiya.

MMENE TINGACITILE

Wa mboni akukonzekela ulendo wobwelelako, akamba ndi mwininyumba, kenako alemba zinthu zokhudza mwininyumbayo
  • Mukamakonzekela ulaliki wanu wa ku nyumba ndi nyumba, muzikonzekelanso funso limene mungadzasiye kuti mudzayankhe ulendo wotsatila. Mwina mungakonze funso limene lili m’cofalitsa cimene mukugaŵila. Mwinanso mungakonze funso lili m’cofalitsa cimene timaphunzitsilamo Baibulo comwe mufuna kudzagawila paulendo wotsatila.

  • Mukamaliza kukambilana ndi munthu wacidwi, muuzeni kuti mufuna kudzabwelanso, ndipo mufunseni funso limene mwakonza kuti mudzakambilane ulendo wotsatila. Tengani adilesi kapena nambala yake ya foni.

  • Mukamuuza tsiku ndi nthawi imene mudzabwelelako, muyenela kukwanilitsa lonjezo lanu.—Mat. 5:37

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani