LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 November tsa. 3
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kupelekela Munthu Magazini Kumathandiza Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 November tsa. 3

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupanga Ulendo Wobwelelako

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu ambili amene amacita cidwi na uthenga wa ufumu, amafuna-funa coonadi pa za Mulungu. (Yes. 55:6) Kuti tiwaphunzitse mofikapo, tifunika kupitako mobweleza-bweleza. Anthu amakumana na zovuta zosiyana-siyana, conco, njila imene tingakulitsile cidwi cawo siingafanane. Komabe, kuti tikhale aluso tifunika kukonzekela bwino na kukhala na colinga pa ulendo uliwonse. Colinga cathu cacikulu ni kuyambitsa phunzilo la Baibo.

Mlongo akonzekela ulendo wobwelelako

MMENE TINGACITILE:

Alongo aŵili acita ulendo wobwelelako na kutambitsa vidiyo
  • Yesetsani kubwelelako mwamsanga, mwina m’masiku ocepa cabe.—Mat. 13:19

  • Khalani waubwenzi ndi waulemu. Khalani womasuka

  • Yambani mwa kuwapatsa moni waubwenzi. Muzichula dzina lawo. Akumbutseni cimene mwabwelela—kaya n’kudzayankha funso, kubweletsa magazini yatsopano, kuŵaonetsa webusaiti, kuŵatambitsa vidiyo, olo kuŵaonetsa mmene timacitila phunzilo la Baibo. Sinthani ulaliki wanu ngati cidwi cake capita pa nkhani ina.—Afil. 2:4

  • Thililani mbeu ya coonadi imene munabyala mu mtima mwake mwa kukambilana naye mfundo ya m’Malemba, kapena kumusiyila cofalitsa. (1 Akor. 3:6) Yesani kukhazikitsa ubwenzi naye.

  • Yalani maziko a ulendo wotsatila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani