LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 March tsa. 4
  • Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Khalanibe na Mtima Wamphumphu!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • “Yembekezela Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Yobu Anali Ndani?
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 March tsa. 4

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 1-5

Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa

Satana ayang’ana Yobu

Yobu anali kukhala m’dziko la Uzi, pa nthawi imene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo. Ngakhale kuti sanali Mwiisraeli, Yobu anali wolambila Yehova wokhulupilika. Anali ndi banja lalikulu, cuma cambili, ndipo anali munthu wacitsanzo cabwino m’dela lake. Anali mlangizi wolemekezeka ndi woweluza wopanda tsankho. Anali kuthandiza anthu aumphawi ndi ovutika. Yobu anali munthu wokhulupilika.

Yobu anaonetsa kuti Yehova ndi wofunika kwambili paumoyo wake

1:8-11, 22; 2:2-5

  • Satana anadziŵa kuti Yobu anali wokhulupilika. Sikuti iye anatsutsa zakuti Yobu anali kumvela Mulungu, koma, anakaikila zolinga za Yobu

  • Satana anakamba kuti Yobu anali kutumikila Yehova cifukwa ca dyela

  • Kuti atsutse bodza la Satana limeneli, Yehova analola kuti Satana aukile munthu wokhulupilikayu. Satana anaononga zinthu zonse zimene Yobu anali nazo

  • Yobu atakhalabe wokhulupilika, Satana anayamba kukaikila kukhulupilika kwa anthu onse

  • Yobu sanacimwe kapena kuimba Mulungu mlandu wakuti ndiye anacititsa mavuto amene anakumana nao

Yobu ataikilidwa onse a m’banja lake
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani