CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 52-59
“Umutulile Yehova Nkhawa Zako”
Davide anakumana ndi mavuto ambili. Pamene Salimo 55 inali kulembedwa, iye anali atakumanapo kale ndi mavuto monga . . .
Kunyozedwa
Kuzunzidwa
Kudziimba mlandu
Mavuto a m’banja
Kudwala
Kucitilidwa zinthu mopanda cilungamo
Ngakhale kuti mavuto a Davide anaoneka ngati ndi osapililika, iye anawapililabe. Anthu amene aona kuti sangapilile mavuto, angatsatile malangizo a Davide ouzilidwa akuti: “Umutulile Yehova Nkhawa Zako.”
Tingatsatile bwanji malangizo amenewa?
55:22
Mukakumana ndi vuto kapena mukakhala ndi nkhawa, pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pamtima
Pezani thandizo kucokela m’Mau a Yehova ndi gulu lake
Citani zimene mungakwanitse kuti muthetse vuto limenelo mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo