LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 tsa. 12
  • Mmene Tingaonetsele Cikondi kwa Anthu Anzathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingaonetsele Cikondi kwa Anthu Anzathu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA PONENA ZA CIKONDI
  • ZIMENE KUKONDA ANTHU ANZATHU KUMATANTHAUZA
  • Cikondi Khalidwe Lamtengo Wapatali
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Mmene Tingalimbikitsile Cikondi Cathu pa Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Musalole Kuti Cikondi Canu Cizilale
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 tsa. 12
Msamaliya wacifundo wochulidwa m’fanizo la Yesu, akupaka mafuta m’mabala a munthu amene anamenyedwa kwambili na kum’siya m’mbali mwa njila.

Cikondi cimatilimbikitsa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu

Mmene Tingaonetsele Cikondi kwa Anthu Anzathu

Popeza kuti tonsefe kholo lathu loyamba ni Adamu, ndife banja limodzi. Ngakhale kuti a m’banja amafunika kukondana na kulemekezana, masiku ano n’zovuta kuti anthu a m’banja limodzi azikondana. Ndipo izi si zimene Mulungu wathu wacikondi amafuna.

ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA PONENA ZA CIKONDI

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—LEVITIKO 19:18.

“Pitilizani kukonda adani anu.”—MATEYU 5:44.

ZIMENE KUKONDA ANTHU ANZATHU KUMATANTHAUZA

Onani mmene Mulungu amafotokozela khalidwe lacikondi m’Mawu ake pa 1 Akorinto 13:4-7:

“Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.”

Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena acita nanu zinthu moleza mtima komanso mokoma mtima, ndipo sacita nanu zinthu mwaukali mukalakwitsa zina zake?

“Cikondi sicicita nsanje.”

Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena amakukaikilani, kapena kukucitilani kaduka?

Cikondi “sicisamala zofuna zake zokha.”

Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena amalemekeza maganizo anu, ndipo saumilila maganizo awo?

Cikondi “sicisunga zifukwa.”

Ganizilani izi: Mulungu ni wokonzeka kukhululukila aliyense wolapa amene anam’lakwila. Malemba amatiuza kuti: “Iye sadzakhalila kutiimba mlandu nthawi zonse cifukwa ca zolakwa zathu, kapena kutisungila mkwiyo.” (Salimo 103:9) Timakondwela ngati munthu amene tinam’khumudwitsa watikhululukila. Conco, tiyenela kukhala okonzeka kukhululukila ena akatikhumudwitsa.—Salimo 86:5.

Cikondi “sicikondwela ndi zosalungama.”

Ganizilani izi: Zoipa zikaticitikila, sitingakonde kuti ena azikondwela pamene tivutika. Conco, sitiyenela kukondwela ngati ena akukumana na mavuto ngakhale kuti anaticitilapo zoipa.

Kuti tipeze madalitso a Mulungu, tifunika kukonda ena m’njila zimenezi, mosasamala kanthu za msinkhu, dziko, kapena cipembedzo cawo. Tingacite zimenezi mwa kuthandiza amene afunikila thandizo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani