UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulitsani Makhalidwe Aumulungu—Cikhulupililo
CIFUKWA CAKE N’COFUNIKA:
Cikhulupililo n’cofunika kuti tikondweletse Mulungu.—Aheb. 11:6
Cikhulupililo m’malonjezo a Mulungu cimatithandiza kupilila mayeselo.—1 Pet. 1:6, 7
Kusoŵa cikhulupililo kumatsogolela ku chimo.—Aheb. 3:12, 13
MMENE TINGAKULITSILE CIKHULUPILILO:
Pemphelani kwa Mulungu kuti akuwonjezeleni cikhulupililo.—Luka 11:9, 13; Agal. 5:22
Muziŵelenga Mau a Mulungu na kuwasinkha-sinkha.—Aroma 10:17; 1 Tim. 4:15
Nthawi na nthawi, muziyanjana ndi anthu amene ali na cikhulupililo.—Aroma 1:11, 12
Ningalimbitse bwanji cikhulupililo canga ndi ca a m’banja langa?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZICITA ZINTHU ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA WOKHULUPILIKA—KHALANI NA CIKHULUPILILO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi “cikhulupililo copanda cinyengo” n’cotani? (1 Tim. 1:5)
Ni zisonkhezelo zoipa ziti zimene tiyenela kupewa kuti tikhale na cikhulupililo colimba?
N’cifukwa ciani cikhulupililo cidzafunikila ngako pa cisautso cacikulu? (Aheb. 10:39)