CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 12-13
Fanizo la Tiligu ndi Namsongole
Yesu anaseŵenzetsa fanizo la tiligu ndi namsongole pofuna kuonetsa mmene adzatengela gulu lonse la Akhristu odzozedwa pakati pa anthu, ndi kuti Akhristuwo adzayamba kudzozedwa kuyambila mu 33 C.E.
‘Munthu anafesa mbewu zabwino m’munda mwake’
Wofesa: Yesu Khristu
Mbewu zabwino zifesedwa: Ophunzila a Yesu adzozedwa na mzimu woyela
Munda: Anthu onse pa dziko lapansi
“Anthu ali m’tulo, kunabwela mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole”
Mdani: Mdyelekezi
Anthu ali m’tulo: Imfa ya atumwi
“Zilekeni zonse zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola”
Tiligu: Akhristu odzozedwa
Namsongole: Akhristu onama
“Coyamba sonkhanitsani namsongole . . . ; Mukatha mupite kukasonkhanitsa tiligu”
Akapolo/okolola: Angelo
Kusonkhanitsidwa kwa Namsongole: Kucotsewa kwa Akhristu onama pakati pa Akhristu odzozedwa
Kusonkhanitsila m’nkhokwe: Akhristu odzozedwa asonkhanitsidwa mumpingo umene unakhazikitsidwanso
Pamene nyengo yokolola inayamba, n’ciani cinasiyanitsa Akhristu oona na Akhristu onama?
Kodi kumvetsetsa fanizo ili kunganipindulitse bwanji ine panekha?