LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 February tsa. 4
  • Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Muzilemekeza Amene Afunika Kulandila Ulemu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 February tsa. 4

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako

Yesu ali pa dziko lapansi, anagogomeza lamulo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Eks. 20:12; Mat. 15:4) Yesu anali na ufulu wolankhula cifukwa ali wacicepele, anali kumvela makolo ake. (Luka 2:51) Atakula, anaonetsetsa kuti amayi ake adzasamalilidwa bwino iye akamwalila.—Yoh. 19:26, 27.

Masiku anonso, Akhristu acicepele amene amamvela makolo awo, na kukamba nawo mwaulemu, amaonetsa kuti amawalemekeza. Lamulo lolemekeza makolo athu lilibe malile. Ngakhale makolo athu akalambe, tifunika kupitiliza kuwalemekeza mwa kumvela malangizo awo anzelu. (Miy. 23:22) Timaonetsanso kuti timalemekeza makolo athu okalamba mwa kuwathandiza akavutika maganizo komanso kuwasamalila mwa kuthupi ngati pafunika kutelo. (1 Tim. 5:8) Kaya ndise acicepele kapena acikulile, kukambilana bwino na makolo athu ndiyo njila yabwino yoonetsela kuti timawalemekeza.

TAMBANI VIDIYO YA TUKADOLI YAKUTI NINGAKAMBE NAWO BWANJI MAKOLO ANGA? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’ciani cingacititse kuti zikhale zovuta kukamba na makolo anu?

  • Kodi mungawaonetse bwanji ulemu makolo anu pokamba nawo?

    Kamnyamata kalembela makolo ake kalata, kakamba na makolo ake, kenako kachaya bola na atate ake
  • N’cifukwa ciani simuyenela kuleka kukamba na makolo anu? (Miy. 15:22)

    Makolo athandiza mwana wawo kukonzekela mmene angacitile na mavuto a m’tsogolo

    Kukambilana na makolo anu kungakuthandizeni kukhala na umoyo wopambana

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani