LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 February tsa. 8
  • Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Olungama Palibe Cowakhumudwitsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tsatilani Yesu na Colinga Cabwino
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • “Nathamanga Panjilayo Mpaka pa Mapeto”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 February tsa. 8

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 18-19

Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena

Yesu anaseŵenzetsa mafanizo pofuna kuphunzitsa za kuopsa kwa kudzipunthwitsa kapena kupunthwitsa ena.

18:6, 7

  • Liu lakuti “copunthwitsa” limatanthauza zocita kapena mikhalidwe imene ingacititse munthu kutsatila njila yolakwika, kupunthwa kapena kugwa m’makhalidwe, kapena kugwela m’chimo.

  • Munthu amene amapunthwitsa ena cingakhale bwino kumuponya m’nyanja atamangililidwa cimwala ca mphelo m’khosi mwake

Cimwala ca mphelo cikuyendetsedwa na bulu; cimwala ca mphelo camangililidwa m’khosi mwa munthu, ndipo waponyedwa m’nyanja

Miyala ya Mphelo

18:8, 9

  • Yesu analangiza otsatila ake kuti ayenela kucotsa ngakhale cinthu cofunika ngako monga dzanja kapena diso ngati cimawapangitsa kupunthwa

  • Cingakhale bwino kucotsa ciwaloco kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu kuposa kucisunga ndi kupita ku Gehena, kutanthauza ciwonongeko cothelatu

Mu umoyo wanga, n’ciani cingakhale copunthwitsa? Nanga ningapewe bwanji kudzipunthwitsa kapena kupunthwitsa ena?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani