CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 25
“Khalanibe Maso”
Ngakhale kuti fanizo la Yesu la anamwali 10 linali kupita kwa otsatila ake odzozedwa, uthenga wake ungagwilenso nchito kwa Akhristu onse. (w15 3/15 mape. 12-16) “Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziŵa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi imwe mungalifotokoze fanizo la Yesu limeneli?
Mkwati (vesi 1)—Yesu
Anamwali ocenjela ndiponso okonzeka (vesi 2)—Akhristu odzozedwa amene ni okonzeka kukwanilitsa nchito yawo mokhulupilika, na amene amawala ngati zounikila mpaka ku mapeto (Afil. 2:15)
Mau ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)—Cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu
Anamwali opusa (vesi 8)—Akhristu odzozedwa amene adzapita kukakumana na Mkwati koma sanakhale maso ndiponso sanakhulupilike
Anamwali ocenjela anakana kupatsako anzawo mafuta (vesi 9)—Akhristu odzozedwa okhulupilika akadzaikiwa cidindo comaliza, sadzathandizanso aliyense wosakhulupilika
“Mkwati Anafika” (vesi 10)—Yesu adzabwela kudzapeleka ciweluzo pamene cisautso cacikulu catsala pang’ono kutha
Anamwali ocenjela analoŵa limodzi na mkwati m’nyumba imene munali phwando lacikwati, ndipo citseko cinatsekewa (vesi 10)—Yesu adzasonkhanitsila odzozedwa ake okhulupilika kumwamba, koma osakhulupilika sadzalandila mphoto yawo ya kumwamba