UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pewani Misampha Poceza ndi Anthu pa Intaneti
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Mofanana na zida zambili, mawebusaiti ocezelapo pa intaneti angakhale othandiza kapena owononga. Akhristu ena asankha kusaseŵenzetsa mawebusaiti ocezelapo. Ena amawaseŵenzetsa kuti aziceza na acibululu komanso anzawo. Komabe, Mdyerekezi amafuna kuti tiziseŵenzetsa mawebusaiti amenewa molakwika, zimene zingawononge mbili yathu na ubwenzi wathu na Yehova. Monga Yesu, tingaseŵenzetse mfundo za m’Mau a Mulungu kuti tidziŵe zimene zingativulaze na kuzipewa.—Luka 4:4, 8, 12.
MISAMPHA YOFUNIKA KUPEWA:
Kuseŵenzetsa intaneti mopitilila malile. Kuthela maola ambili tikuceza na anthu pa intaneti kungatiwonongele nthawi yofunika yocita zinthu zauzimu.
Mfundo za m’Baibo: Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10
Kutamba zinthu zokayikitsa. Kuyang’ana mapikica outsa cilako-lako kungacititse munthu kuyamba kutamba zamalice kapena kucita zaciŵelewele. Kuŵelenga nkhani zimene anthu ampatuko amafalitsa pa intaneti, kungawononge cikhulupililo cathu.
Mfundo za m’Baibo: Mat. 5:28; Afil. 4:8
Kulemba mau osayenela kapena kuika mapikica osayenela. Cifukwa cakuti mtima ni wonyenga, munthu angayambe cizoloŵezi colemba mau osayenela kapena kuika mapikica osayenela pa intaneti. Kucita izi kungawononge mbili yake kapena kufooketsa cikhulupililo cake.
Mfundo za m’Baibo: Aroma 14:13; Aef. 4:29
TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZISAMALA POCEZA NDI ANTHU PA INTANETI, NDIYENO KAMBILANANI MMENE MUNGAPEWELE ZOCITIKA ZOTSATILAZI: