LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsa. 9
  • Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti ni Otani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti ni Otani?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Pewani Misampha Poceza ndi Anthu pa Intaneti
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Webu Saiti yathu—Igwilitsileni Nchito pa Phunzilo Laumwini ndi la Banja
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Sankhani Anzanu Mwanzelu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mkulu Wina wa za Umoyo Wacenjeza za Mavuto Amene Acinyamata Amakumana Nawo pa Soshomidiya—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
    Nkhani Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 March tsa. 9

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti Ni Otani?

Bwenzi ni munthu “amene amagwilizana kwambili na wina cifukwa cakuti amamukonda kapena kumulemekeza.” Mwacitsanzo, Yonatani na Davide anakhala pa ubwenzi wathithithi pambuyo pakuti Davide wapha Goliyati. (1 Sam. 18:1) Aliyense wa iwo anali na makhalidwe amene mnzake anali kukopeka nawo. Cotelo, kuti anthu akhale pa ubwenzi wolimba amafunika kudziŵana bwino. Kudziŵana na munthu wina kumatenga nthawi komanso kumafuna khama. Komabe, anthu angakhale “mabwenzi” pa masoshomidiya mwa kugodiniza batani inayake pa cipangizo cawo. Anthu pa Intaneti amakonzekela bwino zimene afuna kukamba, ndipo angathe kudzisintha. Conco zimakhala zosavuta kwa iwo kubisa umunthu wawo. N’cifukwa cake tiyenela kukhala osamala posankha mabwezi pa Intaneti. Musamaope kunyalanyaza kapena kukana, ngati anthu ena amene simuwadziŵa kwenikweni akupemphani kuti mukhale mabwenzi awo, poopa kuti mungawakhumudwitse. Podziŵilatu mavuto amene angakumane nawo, ena asankha kusaseŵenzetsa masoshomidiya. Koma kodi muyenela kukumbukila ciani mukasankha kuseŵenzetsa soshomidiya?

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZISAMALA POCEZA NA ANTHU PA INTANETI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika mu vidiyo yakuti “Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti.” Mtsikana akudabwa kuti zithunzi zake zikuonekela pa masikilini a TV.

    Kodi muyenela kuganizila ciani musanalembe ndemanga yanu kapena kuika zithunzi pa soshomidiya?

  • Cithunzi coonetsa zocitika mu vidiyo yakuti “Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti.” Pa sikelo pali cithunzi cokongola ca mtsikana ku mbali imodzi na ndalama za makoini ku mbali ina. Cithunzico cikulemela kwambili kuposa ndalamazo.

    N’cifukwa ciani muyenela kusankha mosamala mabwenzi anu pa Intaneti?

  • Cithunzi coonetsa zocitika mu vidiyo yakuti “Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti.” Anthu aŵili a maonekedwe oopsa akuonetsa mnyamata zinthu zimene zinaikidwa pa soshomidiya, koma mnyamatayo watseka maso na dzanja.

    N’cifukwa ciani muyenela kudziikila malile pa kuculuka kwa nthawi imene mumathela pa soshomidiya?—Aef. 5:15, 16

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani