CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 7-10
Utumiki Wathu Wothandiza Pakacitika Tsoka
Akhristufe timacita utumiki wa mbali ziŵili. Mbali yoyamba ni “utumiki wokhazikitsanso mtendele,” kapena kuti nchito yathu yolalikila na kuphunzitsa. Mbali yaciŵili ni “utumiki wothandiza” okhulupilila anzathu. (2 Akor. 5:18-20; 8:4) Conco kuthandiza Akhristu ovutika ni mbali ya utumiki wathu wopatulika. Tikamatengako mbali,
timasamalila bwino zofunika za abale na alongo athu. —2 Akor. 9:12a
timathandiza Akhristu ovutika kuyambanso kucita zinthu zauzimu, zimene ziphatikizapo kugwila nchito yolalikila modzipeleka monga njila yoonetsela ciyamikilo cawo kwa Yehova.—2 Akor. 9:12b
timalemekeza Yehova. (2 Akor. 9:13) Utumiki wathu wothandiza pakacitika tsoka umacitila umboni kwa aliyense, kuphatikizapo anthu amene amaona Mboni za Yehova m’njila yolakwika