UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Utumiki Wathu Wothandiza Patacitika Tsoka Wapindulitsila Abale Athu ku Caribbean
Akhristu oyambilila kalelo, anali kuonetsana cikondi wina akakumana na masoka. Masiku ano, tili na mwayi wocita cimodzi-modzi. (Yoh. 13:34, 35) Tambitsani vidiyo yakuti, Kuonetsa Cikondi M’zocita—Nchito Yothandiza Patacitika Tsoka ku Zisumbu, kuti muone mmene Akhristu anathandizila abale na alongo awo ku Caribbean, ndiyeno yankhani mafunso aya:
Kodi abale athu ku Caribbean anakhudzidwa bwanji na cimphepo coopsa cochedwa Irma, komanso ca Maria?
Kodi Yehova waŵathandiza bwanji abale athu ku Caribbean kupitila mwa Akhristu anzawo?
Kodi amene anakhudzidwa na mphepo zoopsazo anamvela bwanji ataona cikondi na kuwolowa manja kwa abale awo?
Kodi abale na alongo amene anatengako mbali m’nchito yothandiza pakacitika tsoka anali angati ku Caribbean?
Kodi tonsefe tingacite ciani kuti tizicilikiza nchito yothandiza pakacitika tsoka?
Pambuyo potamba vidiyoyi, kodi mumvela bwanji kukhala m’gulu lathu lacikondi?