LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 June tsa. 4
  • Kodi Yehova Aiona Bwanji Nkhaniyi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Yehova Aiona Bwanji Nkhaniyi?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Khalani ndi Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kodi Mumasankha Bwanji Zocita?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Pangani Zosankha Zanu Mwanzelu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 June tsa. 4

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Yehova Aiona Bwanji Nkhaniyi?

Tikafuna kupanga zosankha, zazikulu kapena zazing’ono, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova aiona bwanji nkhaniyi?’ Ngakhale kuti sitingadziŵe maganizo onse a Yehova, iye kupitilila m’Mawu ake, amatiuza zambili zimene zingatithandize kukhala “wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:16, 17; Aroma 11:33, 34) Yesu anazindikila cifunilo ca Yehova, ndipo anaciika patsogolo mu umoyo wake. (Yoh. 4:34) Mofanana na Yesu, tiyeni ticite zimene tingathe kuti tizipanga zosankha zokondweletsa Yehova.—Yoh. 8:28, 29; Aef. 5:15-17.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI PITILIZANI KUZINDIKILA CIFUNILO CA YEHOVA (LE 19:18), NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wathu?

  • Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize kusankha nyimbo zoyenela?

  • Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize pa mavalidwe na kudzikonza?

  • Ni mbali zina ziti mu umoyo wathu zimene zingafune kuti tiseŵenzetse mfundo za m’Baibo?

  • Kodi tingacite ciani kuti tikulitse luso lathu la kuzindikila cifunilo ca Yehova?

Mboni zacinyamata zocoka m’mitundu yosiyana-siyana, zavala zovala zosiyana-siyana, ndipo zikujambula pikica

Kodi zosankha zanga zimaonetsa kuti nili pa ubale wotani na Yehova?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani