UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu ambili akhungu sakhala omasuka kukamba na ŵanthu osaŵadziŵa. Conco pamafunika luso kuti tilalikile anthu amenewa. Yehova amawakonda anthu akhungu. (Lev. 19:14) Tingatengele citsanzo cake mwa kucitapo kanthu kuti tiwathandize mwauzimu.
MMENE TINGACITILE:
“Fufuzani” anthu akhungu. (Mat. 10:11) Kodi mudziŵako munthu amene wacibale wake ni wakhungu? Kodi m’gawo lanu muliko masukulu, nyumba zosungilamo anthu osaona amene angafuneko zofalitsa za anthu akhungu?
Onetsani mzimu waubwenzi. Kukhala waubwenzi komanso kuonetsa cidwi ceni-ceni kungathandize munthu wakhungu kukhala womasuka. Yesani kuyambitsa makambilano pa nkhani zimene anthu akhungu angacite nazo cidwi
Pelekani thandizo la kuuzimu. Pofuna kuthandiza anthu akhungu, gulu lathu lakonza zofalitsa m’mipangidwe yosiyana-siyana. Mungafunse wakhungu kuti afotokoze njila yophunzilila imene afuna. Woyang’anila utumiki afunika kuonetsetsa kuti mtumiki wa mabuku waitanitsa mabuku a anthu akhungu mu mpangidwe umene munthu wakhungu aliyense afuna.