LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 February tsa. 31
  • Anaona Cikondi Ceniceni

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anaona Cikondi Ceniceni
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zidindo Zimene Zimasintha Miyoyo ya Anthu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 February tsa. 31

[kucoka kulamanja kupita kumanzele] Marcelo, Yomara, na Hiver. Aliyense ali na Baibo la Dziko Latsopano la ci Spanish m’kalembedwa ka anthu osaona

Anaona Cikondi Ceniceni

YOMARA na azilongosi ake aŵili—Marcelo komanso Hiver—amakhala m’mudzi wina waung’ono ku Guatemala. Yomara anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova, ndipo posapita nthawi azilongosi ake aŵili naonso anayamba kuphunzila. Koma vuto n’lakuti onse atatu sanali kuona, ndipo sanali kudziŵa kuŵelenga kalembedwe ka anthu osaona. Conco, mphunzitsi wawo wa Baibo anali kuwaŵelengela ndime na malemba a m’phunzilo.

Cinalinso covuta kwa iwo kupezeka ku misonkhano ya mpingo. Sanali kukwanitsa pawokha kuyenda mtunda wa mphindi 40 kupita ku Nyumba ya Ufumu. Koma abale na alongo mumpingo anakonza zakuti azipita nawo ku misonkhano imeneyo. Ndipo Yomara na azilongosi ake atayamba kupeleka nkhani za m’sukulu pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, abale anali kuwathandiza kuloŵeza pamtima nkhani zawo.

Mu May 2019, misonkhano ya mpingo inayamba kucitikila m’mudzi mwawo. Nthawiyo banja lina limene linali kucita upainiya linali litasamukila m’mudzi umenewo. Iwo anadziikila colinga cakuti aziphunzitsa anthu a pacibale amenewo kudziŵa kuŵelenga na kulemba zilembo za akhungu, ngakhale kuti iwo sanali kudziŵa zilembozo. Conco, iwo anapita ku laibulale kuti akabweleke mabuku a zilembo za osaona, n’colinga cakuti adziŵe mmene angaphunzitsile ena.

Marcelo akupeleka ndemanga pa msonkhano wa mpingo

M’miyezi yocepa, Yomara na azilongosi ake anaphunzila kuŵelenga kalembedwe ka anthu osaona, ndipo izi zinawathandiza kuti apite patsogolo mwauzimu.a Pano tikamba, Yomara, Marcelo, na Hiver ni apainiya a nthawi zonse. Ndipo Marcelo ni mtumiki wothandiza. Iwo amakhala otangwanika na zinthu zauzimu mlungu wonse. Cangu cawo cayambukila ngakhale anthu ena.

Anthu atatu a pacibale amenewa amayamikila kwambili mmene mpingo umawathandizila. Yomara anati: “A Mboni akhala akutionetsa cikondi ceniceni cacikhristu kungocokela nthawi yoyamba imene tinakumana nawo.” Nayenso Marcelo: “Tili na mabwenzi abwino kwambili mumpingo, ndipo tili m’gulu logwilizana la abale padziko lonse amene amakondana.” Yomara na azilongosi ake amayembekeza mwacidwi kudzaona nthawi pamene dziko lidzasintha kukhala paradaiso.—Sal. 37:10, 11; Yes. 35:5.

a Bulosha lakuti Phunzilani Kuŵelenga Kalembedwe ka Anthu Osaona, linakonzedwa kuti lithandize anthu osaona kapena amene saona bwino-bwino kudziŵa kuŵelenga na kulemba.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani