UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Moseŵenzetsela Makambilano Acitsanzo
Kucokela mu January 2018, pacikuto ca Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki Wathu pamakhala makambilano acitsanzo. Kodi makambilano amenewa tingaŵaseŵenzetse bwanji?
Pokamba Nkhani ya M’sukulu: Muyenela kuseŵenzetsa funso, lemba, komanso ulalo, zimene zili pa makambilano acitsanzo. Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti tifunika kucita kuloŵeza mawu a mu vidiyo ya makambilano acitsanzo. Mungaseŵenzetse mtundu wina wa makambilano, mawu oyamba, njila ina ya mafotokozedwe na zina zotelo. Mungagaŵilenso cofalitsa ca mu Thuboksi yathu, olo kuti sicinachulidwe mu malangizo a mbali imeneyo.
Pamene Tili Muulaliki: Makambilano acitsanzo anakonzedwa kuti azitipatsa malingalilo otithandiza. Ngati munthu waonetsa cidwi ceni-ceni ndipo afuna kudziŵa zambili, mungapitilize kukambilana naye mwina mwa kuseŵenzetsa makambilano acitsanzo a ulendo wobwelelako. Mungasintheko makambilano acitsanzo, kapena mungaseŵenzetse makambilano ena osiyana nawo. Kodi nkhani ya mwezi watha kapena lemba lina ingakope cidwi ca anthu a m’gawo lanu? Kodi anthu a kumene mukhala amacita cidwi kwambili na zocitika za posacedwa kapena kuti nyuzi? Mulimonse mmene mwasankhila kuseŵenzetsa makambilano acitsanzo, colinga canu cizikhala ‘kucita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti tiugawilenso kwa ena.’—1 Akor. 9:22, 23.