UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Tingaseŵenzetsele Makambilano Acitsanzo
Abale amagwila nchito yaikulu pokonza makambilano acitsanzo, ndipo ofalitsa ambili aona kuti makambilano amenewa ni othandiza kwambili m’magawo awo. Koma popeza mikhalidwe imasiyana-siyana padzikoli, pocita ulaliki ofalitsa ali na ufulu wosintha funso, lemba, na ulalo, ngakhalenso kugwilitsa nchito ulaliki wina umene ungakhale wocititsa cidwi kwa anthu a m’gawo lawo. Komabe, ngati kuli kampeni ya ulaliki, ofalitsa onse ayenela kutsatila malangizo amene apelekedwa. Colinga cathu ni kukwanilitsa nchito imene Yesu anatipatsa, yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu.—Mat. 24:14.
Ofalitsa akamasamalila nkhani zawo za m’sukulu, makambilano awo atsamile (azikidwe) pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo a mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki. (Mwacitsanzo, mu July na August, mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo ni kuonetsa colinga ca Mulungu kwa anthu.) Koma ofalitsa ni omasuka kugwilitsa nchito funso lina, lemba, ulalo, kapena mtundu wina wa makambilano amene angakhale othandiza m’gawo lanu, kupatulapo ngati papelekedwa malangizo akuti asasinthe zimenezi. Izi zasintha malangizo amene ali pa tsamba 8 m’kabuku ka misonkhano ka June 2020.