CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 16-17
Zimene Tingaphunzile pa Zocitika za pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo
16:12-15
Mkulu wa ansembe anali kuseŵenzetsa zofukiza pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa?
Mapemphelo a atumiki okhulupilika a Yehova ali ngati zofukiza. (Sal. 141:2) Mkulu wa ansembe anali kubweletsa zofukiza pamaso pa Yehova mwaulemu kwambili. Mofananamo, nafenso timaonetsa ulemu kwambili popemphela kwa Yehova
Mkulu wa ansembe asanapeleke nsembe, coyamba anali kufukiza zofukiza. Mofananamo, Yesu asanapeleke moyo wake monga nsembe, anacita zinazake zimene zinatsegula mwayi wakuti Yehova alandile nsembe yake. Anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova pa umoyo wake
Kodi ningacite ciani kuti Yehova alandile nsembe yanga?