CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Funsani Mafunso
Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” amafuna kuti tizipeza cimwemwe mu ulaliki. (1 Tim. 1:11) Cimwemwe cathu cimawonjezeka ngati tikulitsa maluso athu mu ulaliki. Kufunsa mafunso kumautsa cidwi ca munthu. Komanso ni njila yabwino yoyambitsila makambilano. Mafunso amalimbikitsa anthu kuganiza. (Mat. 22:41-45) Ngati tifunsa munthu mafunso na kumumvetsela, timakhala ngati tikumuuza kuti, ‘Ndiwe wofunika kwa ine.’ (Yak. 1:19) Mayankho amene munthu angapeleke angatithandize kudziŵa mmene tingakambile naye kuti timufike pa mtima.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUFUNSA MAFUNSO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Ni makhalidwe abwino ati amene Rose anaonetsa?
Kodi mlongo Neeta anaseŵenzetsa bwanji mafunso poonetsa cidwi kwa womvetsela wake?
Kodi Neeta anaseŵenzetsa bwanji mafunso pothandiza Rose kukulitsa cidwi comvetsela uthenga wabwino?
Kodi Neeta anagwilitsila nchito bwanji mafunso pothandiza Rose kuganizilapo pa zimene anali kukambilana naye?