CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
Yehova ndiye amapangitsa kuti mbewu ya coonadi izike mizu mumtima mwa munthu na kukula. (1 Akor. 3:6-9) Conco kuti zinthu zitiyendele bwino mu ulaliki, tiyenela kudalila Yehova kuti atithandize na kuthandizanso ophunzila athu
Pemphani Yehova kuti athandize ophunzila anu kupilila mavuto na kugonjetsa zopinga zimene zimawalepheletsa kupita patsogolo. (Afil. 1:9, 10) Chulani zinthu mwacindunji. Pemphani mzimu woyela kuti uzitsogolela maganizo anu na zocita zanu. (Luka 11:13) Phunzitsani ophunzila Baibo anu kupemphela, ndipo alimbikitseni kucita zimenezi. Muzipemphela nawo limodzi komanso muziwapemphelela, ndipo pocita zimenezi muzichula maina awo.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—LANDILANI THANDIZO LA YEHOVA—PEMPHELO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Ni vuto lotani limene Neeta anakumana nalo pophunzila na Rose?
Kodi lemba la 1 Akorinto 3:6 linam’thandiza bwanji Neeta?
Kodi vuto limene Neeta anakumana nalo linatha bwanji?