CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Pitilizani Kuonetsa Cikondi Cosasintha
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Rute.]
Naomi anacondelela Olipa na Rute kuti abwelele ku Mowabu (Rute 1:8-13; w16.02 10 ¶5)
Rute anakana kusiya Naomi komanso Yehova. (Rute 1:16, 17; w16.02 10 ¶6)
Munthu amaonetsa cikondi cosasintha cifukwa ca mtima wodzipeleka, kukhulupilika, na cikondi cozama. Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa atumiki ake okhulupilika. (Sal. 63:3) Ifenso tiyenela kuonetsa cikondi cosasintha kwa ena.—Miy. 21:21.