LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 May tsa. 7
  • Kodi Mwakonzekela Kukumana na Zacipolowe?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mwakonzekela Kukumana na Zacipolowe?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Khalanibe Wokonzeka m’Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki Kuthandiza Maphunzilo Athu a Baibo Kukonzekela
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 May tsa. 7
Banja likumvetsela nkhani yokamba za cipolowe pa TV. Pafupi na iwo, pali vyola vothaŵa navo pakagwa tsoka.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mwakonzekela Kukumana na Zacipolowe?

Pamene mapeto a dongosolo lino ayandikila, timayembekezela kuti zacipolowe, zaucigawenga, komanso nkhondo zidzawonjezeka. (Chiv. 6:4) Kodi tingakonzekele bwanji mavuto a kutsogolo?

  • Konzekelani kuuzimu: Pezani mfundo kapena nkhani za m’Baibo zimene zingalimbitse cidalilo canu mwa Yehova na gulu lake, komanso zimene zingakuthandizeni kusakhalila mbali pa zandale. (Miy. 12:5; jr 125-126 ¶23-24) Ino ndiyo nthawi yolimbitsa ubwenzi wathu na abale na alongo mumpingo.—1 Pet. 4:7, 8

  • Konzekelani kuthupi: Khalani na pulani ya mmene mungadzitetezele ngati n’zosatheka kucoka panyumba, komanso sungankoni zinthu zina zofunikila. Cina, khalani na pulani ya mmene mungathaŵile kucoka panyumba kupita ku malo otetezeka. Nthawi na nthawi, muziona ngati m’cola canu cothaŵa naco pakagwa tsoka muli zinthu zofunikila, kuphatikizapo zinthu zodzitetezela monga mamaski na magulovesi, komanso ndalama. Dziŵani mmene mungakambile na akulu, komanso tsimikizani kuti iwonso akudziŵa njila imene angakambile nanu.—Yes. 32:2; g17.5 3-7

Pamene cipolowe cili mkati, musaleke kucita zinthu zauzimu. (Afil. 1:10) Musamacoke panyumba, pokhapo ngati mukuthaŵila ku dela lina. (Mat. 10:16) Gaŵanani na ena cakudya canu na zofunikila zina.—Aroma 12:13.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi ya matsoka?

  • Kodi tingacite ciyani kuti tikhale okonzeka?

  • Tingacite ciyani kuti tithandize amene akhudzidwa na matsoka a zacilengedwe?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani