UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Ndimwe Wokonzeka?
Ngati ngozi yacilengedwe ingacitike m’dela lanu, kodi ingakupezeni muli wokonzeka? Zivomezi, mphepo zamkuntho, moto wa m’nkhalango, komanso kusefukila kwa madzi zingacitike mosayembekezeleka, ndipo zingawononge kwambili. Kuwonjezela apo, kuukila kwa zigaŵenga, zipolowe, na matenda oyambukila zingayambe kulikonse, komanso mosayembekezeleka. (Mlal. 9:11) Tisaganize kuti zinthu ngati zimenezi sizingacitike kumene tikhala.
Aliyense wa ife afunika kucitapo kanthu pokonzekela ngozi yacilengedwe. (Miy. 22:3) Ngakhale kuti gulu la Yehova limapelekako thandizo pakacitika ngozi yacilengedwe, aliyense wa ife ali na udindo wokonzekelelatu.—Agal. 6:5.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi kukhala paubale wolimba na Yehova kungatithandize bwanji panthawi ya ngozi yacilengedwe?
N’cifukwa ciani m’pofunika . . .
• kupitiliza kukambilana na akulu ngozi yacilengedwe isanacitike, pamene ikucitika, kapena pambuyo pakuti yacitika?
• kukhala na cola ca zinthu zofunikila?—g17.5 6
• kukambilana mitundu ya ngozi zacilengedwe zimene zingacitike, komanso zimene mungacite pa ngozi iliyonse?
Kodi tingathandize ena m’njila zitatu ziti pamene ngozi yacilengedwe yawacitikila?