LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsa. 13
  • Kodi Zolinga Zanu za Caka Cautumiki Catsopano n’Zotani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Zolinga Zanu za Caka Cautumiki Catsopano n’Zotani?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Khalani na Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Mlengi Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2004
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • “Muzicita Zimene Mawu Amanena”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 July tsa. 13
Msewu wokhotakhota woonetsa zolinga zauzimu zimene tingadziikile. Zikwangwani zimene zili m’mbali mwa msewu umenewu ziimila phunzilo la munthu mwini, kulalikila, makhalidwe acikhristu, na luso la kuphunzitsa.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Zolinga Zanu za Caka Cautumiki Catsopano N’zotani?

Zolinga zauzimu ni ciliconse cimene timayesetsa kukwanilitsa kuti titumikile Yehova mofikapo na kum’kondweletsa. Zolingazo zimatithandiza kukhala Akhristu okhwima mwauzimu. Conco, mpake kutailapo nthawi na mphamvu zathu kuti tizikwanilitse. (1 Tim. 4:15) N’cifukwa ciyani tiyenela kumasanthula zolinga zathu nthawi na nthawi? Cifukwa zinthu zimasintha pa umoyo. N’kutheka kuti colinga cimene tinali naco sitingacikwanilitse tsopano cifukwa zinthu zinasintha pa umoyo wathu. N’kuthekanso kuti colinga cimene tinali naco tinacikwanilitsa, ndipo tingafunike kudziikila cina.

Nthawi yabwino yosanthula zolinga zauzimu ni pamene tatsala pang’ono kuloŵa m’caka cautumiki catsopano. Bwanji osakambilana nkhaniyi pa kulambila kwanu kwa pabanja na kudziikila zolinga aliyense payekha-payenkha, komanso za banja lonse?

Kodi zolinga zanu ni zotani pa mbali zotsatilazi? Nanga mwakonza zotani zimene zingakuthandizeni kukwanilitsa zolingazo?

Kuŵelenga Baibo, kucita phunzilo la munthu mwini, kupezeka pa misonkhano, kupelekapo ndemanga.—w02 6/15 15 ¶14-15

Ulaliki.—w23.05 27 ¶4-5

Makhalidwe acikhristu.—w22.04 23 ¶5-6

Zina:

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani