Mawu Oyamba
Kodi nthawi zina mumaona monga Mulungu sanayankhe mapemphelo anu? Ngati n’conco, dziŵani kuti si imwe mwekha. Ambili apemphelapo kwa Mulungu kuti awathandize pa vuto lawo, koma vutolo silinathe. Nkhani za m’magazini ino zifotokoza cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Mulungu amamvetsela mapemphelo athu, cifukwa cake sayankha mapemphelo ena, komanso mmene mungapemphelele kuti azimvetsela mapemphelo anu.