LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 2 masa. 7-9
  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ONANI MFUNDO ZIŴILI ZIMENE YESU ANAKAMBA PONENA ZA MAPETO:
  • CIZINDIKILO CAKUTI MAPETO ALI PAFUPI
  • “MASIKU OTSILIZA”
  • DZIKO LA PARADAISO LILI PAFUPI
  • Kodi Tili mu “Masiku Otsiliza”?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Paladaiso Ili Pafupi!
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 2 masa. 7-9
Yesu akufotokozela atumwi ake cizindikilo ca masiku otsiliza.

Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba

Monga taonela m’nkhani yapita, Baibo ikamakamba za kutha kwa dziko, sitanthauza kutha kwa dziko lapansili kapena kutha kwa mtundu wa anthu. Koma imatanthauza kutha kwa dongosolo loipali la zinthu na onse amene amalicilikiza. Koma kodi Baibo imafotokoza nthawi pamene dongosolo loipali la zinthu lidzatha?

ONANI MFUNDO ZIŴILI ZIMENE YESU ANAKAMBA PONENA ZA MAPETO:

“Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—MATEYU 25:13.

“Khalani maso, khalani chelu, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwilatu idzafika.”—MALIKO 13:33.

Conco padziko lapansi palibe aliyense amene adziŵa nthawi imene dongosolo loipali la zinthu lidzawonongedwa. Koma Mulungu anakhazikitsa nthawi yoikidwilatu, ‘inde tsiku ndi ola’ limene mapeto adzafika. (Mateyu 24:36) Kodi izi zitanthauza kuti palibiletu njila imene tingadziŵile kuti mapeto ali pafupi? Iyai. Yesu anauza ophunzila ake kuti ayenela kukhala chelu kuti aone zocitika zoonetsa kuti mapeto ali pafupi.

CIZINDIKILO CAKUTI MAPETO ALI PAFUPI

Yesu anakamba kuti zocitika zimenezi zidzakhala cizindikilo ca “mapeto a nthawi ino.” Iye anati: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:3, 7) Anakambanso kuti kudzakhala “milili”, kutanthauza matenda ofalikila okhudza anthu ambili. (Luka 21:11) Kodi mumaziona zocitika zimene Yesu anakamba?

Masiku ano, anthu amavutika na nkhondo zoopsa, njala, zivomezi, komanso matenda osiyanasiyana. Mwacitsanzo mu 2004, civomezi coopsa cimene cinacitikila pa nyanja ya Indian Ocean cinayambitsa tsunami amene anapha anthu pafupifupi 225,000. Mʼzaka zitatu mlili wa COVID-19 unapha anthu pafupifupi 6.9 miliyoni. Yesu anakamba kuti zocitika ngati zimenezi zidzaonetsa kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.

“MASIKU OTSILIZA”

M’Baibo, nthawi imene mapeto ali pafupi kufika imachedwa “masiku otsiliza.” (2 Petulo 3:3, 4) Lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 linakambilatu kuti m’masiku otsiliza anthu adzakhala na makhalidwe oipa. (Onani bokosi lakuti “Mmene Anthu Adzakhalila Mapeto a Dzikoli Atatsala Pang’ono Kufika.”) Kodi masiku ano mumawaona anthu odzikonda, adyela, oopsa, komanso opanda cikondi? Zimenezi nazonso ni umboni wakuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili.

Kodi masiku otsiliza adzatenga utali wotani? Baibo imakamba kuti adzatenga “kanthawi kocepa” cabe. Kenako, Mulungu adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:15-18; 12:12.

Nkhondo

Asilikali ali kunkhondo ndipo akuwombela mfuti anzawo atakhala kuseli kwa cipupa codzitetezela.
  • Kuyambila mu 2007 mpaka 2017, ciŵelengelo ca anthu amene anaphedwa pa nkhondo komanso cifukwa ca zaucigaŵenga, cinakwela na 118 pelesenti

Matenda

Munthu wodwala wagona pabedi m’cipatala.
  • Matenda ena amene amapha anthu ambili ni awa: Matenda a kumtima, sitroko, matenda a m’cifuwa, zilema zobadwa nazo, matenda otsegula m’mimba, khansa, TB

Njala

Kamtsikana kamene kali na njala kwambili kanyamula mbale.
  • Mu 2021, 9.8 pelesenti ya anthu padziko lonse anali kuvutika na njala, ndipo pafupifupi mwana mmodzi pa ana atatu aliwonse osapitilila zaka 5 anali opinimbila cifukwa copeleŵela zakudya m’thupi

Nchito Yolalikila Padziko Lonse

A Mboni za Yehova ali pafupi na kasitandi ka zofalitsa, akulalikila mwamuna wina.
  • Alaliki oposa 8.6 miliyoni (Mboni za Yehova) amafalitsa mabuku ophunzilila Baibo m’zinenelo zoposa 1,000 m’maiko 240

DZIKO LA PARADAISO LILI PAFUPI

Mulungu anaika kale tsiku na ola pamene adzawononga dongosolo loipali la zinthu. (Mateyu 24:36) Koma palinso uthenga wina wabwino wakuti Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe.” (2 Petulo 3:9) Iye wapatsa anthu mwayi wophunzila za cifunilo cake na kuyamba kumumvela. Cifukwa ciani? Cifukwa afuna kuti tidzapulumuke pamene dzikoli lidzawongedwa. Afunanso kuti tikakhalemo m’dziko lake latsopano pamene lidzakhala paradaiso.

Mulungu anayambitsa nchito yapadziko lonse yophunzitsa anthu kuti adziŵe zimene angacite kuti akakhalemo m’dziko latsopano lolamulidwa na Ufumu wake. Yesu anakamba kuti Uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zimathela maola mabiliyoni polalikila na kuphunzitsa anthu za uthenga wa m’Baibo wopatsa ciyembekezo. Yesu anakamba kuti nchito yolalikila imeneyi idzacitika padziko lonse lapansi mapeto asanafike.

Nthawi yakuti ulamulilo wa anthu uthe yatsala pang’ono. Koma uthenga wabwino ni wakuti mungathe kupulumuka mapeto a dzikoli na kudzakhala m’dziko la Paradaiso limene Mulungu analonjeza. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimene mungacite kuti mudzakhalemo m’dziko latsopano limenelo.

MMENE ANTHU ADZAKHALILA MAPETO A DZIKOLI ATATSALA PANG’ONO KUFIKA

“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzawo, onenela anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe. Anthu amenewa uwapewe.”—2 TIMOTEYO 3:1-5.

Ulosi wa Yesu wokamba za masiku otsiliza umatipatsa ciyembekezo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani