LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 7/1 masa. 6-8
  • Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NTHAWI YAPADELA M’MBILI YA ANTHU
  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kodi Tili mu “Masiku Otsiliza”?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko “Padzakhala Mtendele Woculuka”
    Galamuka!—2019
  • Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 7/1 masa. 6-8

NKHANI YA PACIKUTO

Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?

Kodi Mulungu adzalola kuti anthu apitilize kupondelezana ndi kucitilana nkhanza? Iyai. Monga taonela m’nkhani yapita, Mulungu adzathetsa kuvutika ndi kupondelezana kumene kwakhalapo kwa zaka zambili. Mlengi wa anthu ndi dziko lapansi afuna kuti mudziŵe kuti nthawi yakuti acitepo kanthu padzikoli yayandikila. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi?

Ganizilani citsanzo ici: Mukafuna kupita kumalo amene simunapiteko, mumayamba mwafunsa munthu kuti akuuzeni njila ndi zizindikilo zimene zingakuthandizeni kuzindikila malowo. Conco mukamaona zizindikilozo, mumatsimikiza mtima kuti mwakhala pang’ono kufika. Mofananamo, Mulungu watipatsa Mau ake amene amafotokoza zocitika za padzikoli. Tikamaona zocitikazo zikukwanilitsidwa timakhala otsimikiza kuti mapeto ali pafupi.

Baibulo limafotokoza kuti zocitika m’nthawi ya mapeto zidzakhala zapadela komanso zovuta m’mbili ya anthu. Ndipo zocitika za padziko lonse zimenezo zidzakhala zosiyanasiyana. Ganizilani zocitika zotsatilazi zimene Mau a Mulungu amakamba.

1. ZOCITIKA ZA PADZIKO: Ulosi wochulidwa m’buku la Mateyu caputala 24 ukufotokoza zocitika za padzikoli zimene zinali kudzakhala cizindikilo ca mbali zambili. Cimeneco cinali kudzakhala cizindikilo “ca mapeto a nthawi ino” kenako “mapeto adzafika.” (vesi 3, 14) Zizindikilo zimenezi zikuphatikizapo nkhondo zikuluzikulu, njala, zivomezi m’malo osiyanasiyana, kusamvela malamulo, kuzilala kwa cikondi, ndi abusa onama. (Vesi 6-26) N’zoona kuti zinthu zimenezi zakhala zikucitika kwa zaka zambili. Komabe pamene mapeto akuyandikila, zocitika zonsezi zakhala zikucitika panthawi yovuta imeneyi. Zizindikilo zimenezi zikucitikila panthawi imodzimodzi ndi zocitika zitatu zotsatilazi.

2. MAKHALIDWE A ANTHU: Baibulo limati “masiku otsiliza,” adzadziŵika ndi kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino. Timaŵelenga kuti: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale ao, osafuna kugwilizana ndi anzao, onenela anzao zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) N’zoona kuti kusalemekeza anthu sikwacilendo, koma zimenezi zacita kunyanya “masiku otsiliza” ano amene akuchulidwa kuti “nthawi yapadela komanso yovuta.” Kodi mwaona mmene makhalidwe abwino a anthu alowela pansi?

3. KUONONGEDWA KWA DZIKO: Baibulo limakamba kuti Mulungu ‘adzaononga amene akuononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Kodi anthu akuononga dziko m’njila ziti? Baibulo limati panthawi imene Nowa anali ndi moyo, “dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi ciwawa. Cotelo, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa.” Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ndiwaononga.’ (Genesis 6:11-13) Kodi mwaona umboni woonetsa kuti ciwawa cikuonjezeka padziko? Kuonjezela apo, mbili ya anthu yakhala yapadela. Iwo afika pakuti angaononge ndi kuseselatu anthu padzikoli cifukwa ca zida zankhondo zimene ali nazo. Dziko likuonongedwanso m’njila ina. Anthu aononga zinthu zimene zimacilikiza moyo padziko lapansi monga mpweya umene timapuma, nyama, zomela, ndi nyanja.

Dzifunseni kuti, kodi anthu anali ndi mphamvu zakuti angadziononge okha m’zaka 100 zapitazo? Lelolino anthu akupanga zida zankhondo zotsogola kwambili zimene zikuwacititsa kukhala ndi mphamvu zoononga dziko. Kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga kwacititsa anthu kuganiza kuti akhoza kuthetsa mavuto. Koma tsogolo la dziko silidalila pa zocita za anthu. Zinthu zonse zisanaonongedwe kothelatu padzikoli, Mulungu adzalowelelapo kuti aononge anthu amene akuonoga dziko lapansi. Izi ndi zimene walonjeza.

4. NCHITO YOLALIKILA PADZIKO LONSE: Cizindikilo cina conenedwelatu coonetsa kuti tili m’nthawi ya mapeto ndi nchito yolalikila. Baibulo limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Nchito yolalikila imeneyi ndi yofunika ndipo kuyambila kale nchitoyi yakhala yosiyana kwambili ndi zimene zipembedzo zambili zimaphunzitsa. M’kati mwa masiku otsiliza, “uthenga wabwino uwu wa ufumu” udzalalikidwa mokwanila. Kodi mudziŵako cipembedzo cililonse cimene cimakamba za uthenga wotelewu? Ngati muona kuti ena amalalikila uthenga umenewu, kodi amafalitsa m’dela lanu cabe kapena “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse”?

Mboni za Yehova ziŵili zikulalikila m’mbali mwa nyanja; akukambilana nkhani ya m’Baibulo ndi mwamuna

Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse m’zinenelo zambili

Webusaiti ya www.jw.org imakamba za “uthenga wabwino uwu wa Ufumu.” Pa webusaiti imeneyi pali zofalitsa zofotokoza uthengawu m’zinenelo zoposa 700. Kodi mudziŵako njila ina iliyonse yothandiza kuti uthenga wabwino wa Ufumu ufalikile padziko lonse lapansi? Kale kukalibe intaneti, Mboni za Yehova zinali kudziŵika kaamba ka khama lao la kulalikila uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Kuyambila mu 1939, pacikuto ca Nsanja ya Mlonda pamakhala mau akuti “Imalengeza Ufumu wa Yehova.” Buku lina lokamba pa zipembedzo linanena kuti nchito yolalikila ya Mboni za Yehova “ndi yosiyana kwambili ndi zipembedzo zina.” Nchito imeneyi imakamba za uthenga wabwino wakuti posacedwapa “mapeto adzafika” kudzela mu Ufumu wa Mulungu.

NTHAWI YAPADELA M’MBILI YA ANTHU

Kodi mwaona kuti zizindikilo zonse zinai zimene zafotokozedwa m’nkhani ino ndi umboni wooneka ndi maso? Kwa zaka zoposa 100, magazini ino yakhala ikuthandiza oŵelenga kudziŵa kuti mapeto ali pafupi. Ngakhale n’telo, anthu ena osakhulupilila sagwilizana nazo. Iwo amakamba kuti popeza dziko likupita patsogolo m’zolankhulila, zinthu padzikoli zikuoneka kuti zikuipilaipilabe. Komabe pali umboni wosatsutsika woonetsa kuti tili pamapeto penipeni pa nthawi yapadela m’mbili ya anthu.

Akatswili ena aona kuti padzikoli pacitika zinthu zina zikuluzikulu zimene zidzasintha dziko. Mwacitsanzo mu 2014 nyuzipepala ya Bulletin of the Atomic Scientists ya bungwe loona pa za sayansi ndi citetezo inacenjeza bungwe la citetezo la United Nation za zinthu zikuluzikulu zimene zikucititsa mantha anthu. Iwo anati: “Kuganizila mozama zinthu zimenezi kwaticititsa kuona kuti luso la zopangapanga laononga cikhalidwe ca anthu.” Anthu ambili ndi otsimikiza kuti tafikadi m’nthawi yapadela. Ofalitsa magazini imeneyi komanso anthu ambili amene amaiŵelenga, sakaikila zakuti nthawi yapadela imeneyi ndi masiku otsiliza ndipo mapeto ali pafupi kwambili. M’malo moopa zimene zicitike mtsogolo, mungayembekezele mapetowo mokondwela. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti inu mungapulumuke mapeto amenewa.

KODI MBONI ZA YEHOVA ZIMALOSELA ZA KUONONGEKA KWA DZIKO?

A Mboni za Yehova salosela za kuonongeka kwa dziko. Kwa zaka zambili, io akhala akulalikila uthenga wabwino wonena za tsogolo. Mwacitsanzo, nkhani ya pamsonkhano wa cigawo mu 1958 inali ndi mutu wakuti: “Ufumu wa Mulungu Ulamulila—Kodi Mapeto a Dziko Ayandikila?” Nkhaniyo inafotokoza kuti “Ufumu wa Mulungu udzabwela kudzaononga dziko la Satana osati dziko lapansili. Ufumu wa Mulungu sudzabwela kudzaocha dziko lapansili, koma kudzacita cifunilo ca Mulungu monga kumwamba cimodzimodzinso pansi pano. Pa cifukwa cimeneco, dziko lapansi lidzasungidwa monga colengedwa ca Mulungu ndipo iye adzalisunga kosatha.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani