LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w21 October masa. 8-13
  • Timatumikila Mulungu “Wacifundo Coculuka”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Timatumikila Mulungu “Wacifundo Coculuka”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAONETSA CIFUNDO
  • KODI N’CIFUNDO KUCOTSA MUNTHU MU MPINGO?
  • N’CIANI CINGATHANDIZE TONSEFE KUONETSA CIFUNDO?
  • Anthu Achifundo Amakhala Odala
    Imbirani Yehova
  • ‘Acifundo ni Acimwemwe!’
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
w21 October masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 41

Timatumikila Mulungu “Wacifundo Coculuka”

“Yehova amakomela mtima aliyense, ndipo nchito zake zonse amazicitila cifundo.”—SAL. 145:9.

NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika

ZIMENE TIKAMBILANEa

1. N’ciani cimabwela m’maganizo mwathu tikaganizila za munthu wacifundo?

TIKAGANIZILA za munthu wacifundo, mwina zimabwela m’maganizo mwathu ni munthu wokoma mtima, komanso wopatsa. Tingaganizilenso za Msamariya wacifundo wa m’fanizo la Yesu. Munthu wa mtundu wina ameneyu, ‘anacitila cifundo’ Myuda amene anagwa m’manja mwa acifwamba. Msamariya ameneyo “anagwidwa cifundo” poona Myuda wovulazidwa, ndipo anam’samalila mwacikondi. (Luka 10:29-37) Fanizoli litiphunzitsa khalidwe la Mulungu wathu—cifundo. Mulungu amaticitila cifundo cifukwa amatikonda, ndipo amacita zimenezi tsiku lililonse.

2. Kodi tingaonetse cifundo m’njila ina iti?

2 Pali njila inanso imene munthu angaonetsele cifundo. Njila imeneyo, ni kuleka kupatsa cilango munthu amene ayenela kulangidwa. N’zimene Yehova amacita. Iye wakhala akuticitila cifundo. Wamasalimo anati: “Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu.” (Sal. 103:10) Koma nthawi zina, Yehova amapeleka cilango cokhwima kwa munthu amene wacita chimo.

3. Tikambilane mafunso ati?

3 M’nkhani ino, tikambilane mafunso atatu aya: N’cifukwa ciani Yehova amaonetsa cifundo? Kodi n’zotheka kupeleka cilango cokhwima koma n’kuonetsabe cifundo? Nanga n’ciani cingatithandize kuonetsa cifundo? Tiyeni tione mmene Mawu a Mulungu ayankhile mafunso amenewa.

CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAONETSA CIFUNDO

4. N’cifukwa ciani Yehova amaonetsa cifundo?

4 Yehova amakonda kuonetsa cifundo. Mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba kuti Mulungu ni “wacifundo coculuka.” Iye anali kukamba za cifundo cimene Mulungu anaonetsa kwa atumiki ake odzozedwa opanda ungwilo, powapatsa ciyembekezo ca moyo wakumwamba. (Aef. 2:4-7) Koma Yehova saonetsa cifundo Akhristu odzozedwa okha. Wamasalimo Davide analemba kuti: “Yehova amakomela mtima aliyense, ndipo nchito zake zonse amazicitila cifundo.” (Sal. 145:9) Cifukwa cokonda anthu, Yehova amaonetsa cifundo ngati pali cifukwa cocitila zimenezo.

5. Kodi Yesu anafika bwanji podziŵa bwino lomwe kuti Yehova ni wacifundo?

5 Kuposa wina aliyense, Yesu amadziŵa kuti Yehova amakonda kwambili kuonetsa cifundo. Iye na Atate wake, anali pamodzi kumwamba zaka masauzande osaŵelengeka asanabwele padziko lapansi. (Miy. 8:30, 31) Pa zocitika zambili, Yesu anaona mmene Atate wake anali kucitila cifundo anthu ocimwa. (Sal. 78:37-42) Ndipo pophunzitsa anthu, anali kuchula za khalidwe labwino la Atate wake limeneli.

Tate sanacititse manyazi mwana wake woloŵelela, koma anam’landila na manja aŵili (Onani ndime 6)c

6. Kodi Yesu anapeleka fanizo lotani potiphunzitsa za cifundo ca Atate wake?

6 Monga tinaonela m’nkhani yapita, Yesu anaseŵenzetsa fanizo la mwana woloŵelela, pofuna kuonetsa kuti Yehova amakonda kwambili kuonetsa cifundo. Mwanayo anacoka panyumba, na ‘kukasakaza cuma cake conse mwa kuloŵelela m’makhalidwe oipa.’ (Luka 15:13) Patapita nthawi, iye analapa mwa kuleka makhalidwe oipawo, anadzicepetsa, ndipo anabwelela ku nyumba. Kodi atate wake anacita motani poona zimenezo? Yesu anati: “Ali capatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa cifundo. Pamenepo anamuthamangila ndi kumukumbatila ndipo anamupsompsona mwacikondi.” Tateyo sanacititse manyazi mwana wake. M’malomwake, anam’citila cifundo na kumukhululukila, ndipo anam’landila na manja aŵili. Mwana woloŵelelayo anali atacimwa kwambili. Koma cifukwa colapa, atate wake anamukhululukila. Tate wacifundo m’fanizoli aimila Yehova. Pophunzitsa mogwila mtima conco, Yesu anaonetsa kuti Yehova ni wofunitsitsa kukhululukila ocimwa amene alapa moona mtima.—Luka 15:17-24.

7. Kodi mmene Yehova amaonetsela cifundo, zimaonetsa bwanji kuti ali na nzelu zakuya?

7 Yehova amaonetsa cifundo cifukwa ni wanzelu zakuya. Nzelu za Yehova si luntha cabe la kuganiza mwakuya popanda kukhudzika mtima. M’malomwake, Baibo imati “nzelu yocokela kumwamba,” ni “yodzaza ndi cifundo ndi zipatso zabwino.” (Yak. 3:17) Monga kholo lacikondi, Yehova amadziŵa kuti cifundo cake cimapindulitsa ana ake. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Cifundo ca Mulungu cimatipatsa ciyembekezo ca zakutsogolo olo kuti ndife opanda ungwilo. Conco, popeza Yehova ali na nzelu zakuya, amaticitila cifundo pakakhala cifukwa cocitila zimenezo. Pa nthawi imodzi-modzi, iye amadziŵa pamene sangafunike kuonetsa cifundo. Pokhala wanzelu, saonetsa cifundo akaona kuti kucita zimenezo kungakhale kulekelela khalidwe loipa.

8. N’ciani cimacitika kwa anthu ocita zoipa osalapa? Nanga n’cifukwa ciani?

8 Bwanji ngati mtumiki wa Mulungu mwadala wasankha kuyamba makhalidwe oipa. Tingacite ciani? Paulo mouzilidwa analemba kuti: ‘Lekani kuyanjana’ naye. (1 Akor. 5:11) Anthu ocita zoipa osalapa amacotsedwa mu mpingo. Kucita izi n’kofunikila kuti abale na alongo athu okhulupilika atetezedwe, komanso kumaonetsa kuti njila za Yehova n’zoyela. Komabe, ena cimaŵavuta kuona kuti kucotsa munthu, ni njila imene Mulungu amaonetsela cifundo. Kodi n’zoona kuti cimeneci n’cifundo? Tiyeni tione.

KODI N’CIFUNDO KUCOTSA MUNTHU MU MPINGO?

Mbusa wapita kuli nkhosa yodwala imene aipatula ku zinzake.

Nkhosa angaipatule ku zinzake pamene ikudwala, koma m’busa amapitiliza kuisamalila (Onani ndime 9-11)

9-10. Malinga n’kunena kwa Aheberi 12:5, 6, n’cifukwa ciani tingati n’cifundo kucotsa munthu mu mpingo? Fotokozani citsanzo.

9 Tikamva cilengezo cakuti munthu amene timakonda “salinso Mboni ya Yehova,” timamvela kuipa kwambili. Mwina tingaone kuti munthuyo sanafunikile kucotsedwa. Kodi n’zoonadi kuti kucotsa munthu mu mpingo ni njila yoonetsela cifundo? Inde. Ngati wina ayenela kupatsidwa cilango koma n’kuleka osam’patsa, kungakhale kupanda nzelu, kupanda cifundo, komanso kupanda cikondi. (Miy. 13:24) Kodi kucotsa munthu wocimwa wosalapa kungam’thandize kusintha khalidwe lake? Inde. Ambili amene anacitapo macimo aakulu anakamba kuti anayeneladi kucotsedwa mu mpingo, cifukwa kunawagunduza kuti azindikile kulakwa kwawo. Kunawathandizanso kusintha khalidwe lawo, na kubwelelanso m’manja mwa Yehova.—Ŵelengani Aheberi 12:5, 6.

10 Ganizilani citsanzo ici. M’busa waona kuti nkhosa yake ina ni yodwala. Iye akudziŵa kuti, kuti athandize nkhosa yodwalayo kucila, ayenela kuicotsa pa zinzake. Monga timadziŵila, nkhosa zimayenda gulu, ndipo zimakhwinyilila ngati azipatula. M’busa akacotsa nkhosa yodwalayo pa zinzake, kodi zitanthauza kuti ni wankhanza kapena woipa mtima? Ayi. Iye amadziŵa kuti ngati angalekelele nkhosayo kukhala pamodzi na zinzake, nkhosa zinazo zingayambukilidwe. Koma akapatula nkhosa yodwalayo, amateteza gulu lonse la nkhosa.—Yelekezelani na Levitiko 13:3, 4.

11. (a) Kodi munthu wocotsedwa tingamuyelezele motani na nkhosa yodwala? (b) Kodi ocotsedwa ayenela kucita ciani? Nanga angapatsidwe thandizo lotani?

11 Mkhristu amene wacotsedwa mu mpingo tingamuyelekezele na nkhosa yodwala. Iye ni wodwala mwauzimu. (Yak. 5:14) Mofanana na matenda akuthupi, kudwala mwauzimu kumayambukila ena. Conco, nthawi zina munthu wodwala mwauzimu angafunikile kucotsedwa mu mpingo. Cilango cimeneci cimaonetsa cikondi ca Yehova pa nkhosa zake zokhulupilika, ndipo cingathandize wocimwayo kuvomeleza kuti analakwadi, komanso kuti alape. Wocotsedwayo ayenela kumapezeka ku misonkhano, kumene angalandile malangizo omuthandiza kukhalanso wolimba mwauzimu. Iye alinso na ufulu wotenga zofalitsa kuti aziŵelenga, na kutamba JW Broadcasting®. Ndipo akulu akaona kuti akupita patsogolo, angamam’patse uphungu na malangizo mwa apa na apo, omuthandiza kucila mwauzimu kuti abwezedwe mu mpingo.b

12. Kodi akulu ayenela kucita naye motani munthu wocimwa wosalapa?

12 M’pofunika kwambili kukumbukila kuti ocimwa osalapa ndiwo amacotsedwa mu mpingo. Akulu amadziŵa kuti iyi ni nkhani yaikulu, conco saitenga mopepuka. Amadziŵanso kuti Yehova amapeleka cilango “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Akulu amakonda abale awo, ndipo sangacite cinthu cimene cingawononge ubwenzi wa abalewo na Yehova. Komabe, nthawi zina wocimwa angafunikile kucotsedwa mu mpingo. Kucita zimenezi ndiko cikondi komanso cifundo.

13. N’cifukwa ciani Mkhristu wina ku Korinto anafunika kucotsedwa mu mpingo?

13 Ganizilani zimene mtumwi Paulo anacita na wocimwa wosalapa m’nthawi ya atumwi. Mkhristu wina ku Korinto anali kucita ciwelewele na mkazi wa atate wake. Izi zinali zocititsa manyazi kwambili! Paulo anali kudziŵa kuti Yehova anauza Aisiraeli kalelo kuti: “Mwamuna wogona ndi mkazi wa bambo ake, wavula bambo ake. Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu.” (Lev. 20:11) Paulo sanalamule kuti munthuyo aphedwe. Koma anauza abale ku Akorinto kuti am’cotse mu mpingo. Khalidwe lake laciwelewele linayamba kuyambukila ena mu mpingo, moti sanali kuonanso kuti kucita zimenezo ni chimo lalikulu.—1 Akor. 5:1, 2, 13.

14. Kodi Paulo anamuonetsa motani cifundo munthu wocotsedwa mu mpingo ku Korinto? Nanga n’cifukwa ciani? (2 Akorinto 2:5-8, 11)

14 Patapita nthawi, Paulo anaona kuti munthuyo wasintha kwambili. Wocimwayo analapa moona mtima. Olo kuti anabweletsa citonzo pa mpingo, zimene Paulo anauza akulu zinaonetsa kuti iye anafunabe kucita na munthuyo mwacifundo. Iye anawauza kuti: “Mukhululukileni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza.” Cifukwa ciani? Paulo anati: “Kuopela kuti mwina woteleyu angamezedwe ndi cisoni cake copitilila malile.” Paulo anacitila cifundo munthu wolapayo. Iye sanafune kuti munthuyo alefuke, kapena kukhwetemuka maganizo na zimene anacita cakuti n’kuleka kufuna-funa cikhululukilo.—Ŵelengani 2 Akorinto 2:5-8, 11.

15. Kodi akulu angaonetse motani kulimba mtima na cifundo pa nthawi imodzi?

15 Akulu amaonetsa cifundo potengela citsanzo ca Yehova. Iwo amalimba mtima ngati m’pofunika kutelo, koma amaonetsa cifundo ngati n’kotheka, pakakhala cifukwa comveka cocitila zimenezo. Ngati akulu sapeleka cilango kwa wocimwa, ndiye kuti akulekelela khalidwe loipa. Kodi ni akulu okha amene ayenela kuonetsa cifundo?

N’CIANI CINGATHANDIZE TONSEFE KUONETSA CIFUNDO?

16. Malinga na Miyambo 21:13, kodi Yehova adzacitanji kwa aja amene sacitila ena cifundo?

16 Akhristu onse ayenela kukhala acifundo potengela citsanzo ca Yehova. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi n’cakuti iye sadzamvetsela mapemphelo a anthu amene sacitila ena cifundo. (Ŵelengani Miyambo 21:13.) Palibe angafune kuti Yehova asayankhe mapemphelo ake. Conco, timayesetsa kupewa kukhala opanda cifundo. M’malo motseka makutu kuti tisamve kulila kwa Mkhristu mnzathu, nthawi zonse tiyenela kukhala okonzeka kumva “kudandaula kwa munthu wonyozeka.” Tiziyesetsa kutsatila uphungu wouzilidwa wakuti: “Wosacita cifundo adzaweluzidwa mopanda cifundo.” (Yak. 2:13) Kukumbukila kuti nafenso timafuna kucitilidwa cifundo, kudzatilimbikitsa kuonetsa ena cifundo. Conco, tizicitila cifundo maka-maka wocimwa wolapa akabwelela mu mpingo.

17. Kodi Mfumu Davide anaonetsa bwanji kuti anali wacifundo?

17 Zitsanzo za m’Baibo, zingatithandize kukhala acifundo na kupewa kukhala ouma mtima. Mwacitsanzo, ganizilani za Mfumu Davide. Kambili iye anali kuonetsa cifundo. Olo kuti Sauli anafuna kumupha, Davide anacitila cifundo mfumu yodzozedwa ya Mulungu, ndipo sanafune kubwezela kapena kumucitila cina coipa.—1 Sam. 24:9-12, 18, 19.

18-19. Ni pa zocitika ziŵili ziti pamene Davide sanaonetse cifundo?

18 Komabe, si nthawi zonse pamene Davide anali kucitila ena cifundo. Mwacitsanzo, pamene Nabala munthu woipa mtima anakamba monyoza kwa asilikali a Davide, na kukana kuwapatsa zakudya, Davide anakalipa kwambili ndipo anaganiza zakuti akaphe Nabala, na onse a m’nyumba yake. Koma Abigayeli, mkazi wa Nabala, anali woleza mtima, ndipo anacitapo kanthu mwamsanga. Izi zinathandiza Davide kupewa kupalamula mlandu wa magazi.—1 Sam. 25:9-22, 32-35.

19 Panthawi ina, mneneli Natani anauza Davide za munthu wolemela amene analanda nkhosa imodzi yokhayo ya munthu wosauka. Mwaukali Davide anati: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, munthu wocita zimenezi ayenela kufa!” (2 Sam. 12:1-6) Davide anali kulidziŵa lamulo la m’Cilamulo ca Mose, lakuti munthu akaba nkhosa imodzi, azilipila nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi imene wabayo. (Eks. 22:1) Koma safunikile kuphedwa ayi. Zimene Davide anakamba zinaonetsa kupanda cifundo. Apa Natani anali kufotokoza cabe fanizo pofuna kuthandiza Davide kuzindikila kuti anacita macimo aakulu. Yehova anamuonetsa cifundo cacikulu Davide, kuposa mmene iye akanacitila kwa munthu wa m’fanizo la Natani amene anaba nkhosa uja.—2 Sam. 12:7-13.

Mfumu Davide anaonetsa mzimu wopanda cifundo pamene Natani anamufikila (Onani ndime 19-20)d

20. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Davide?

20 Onani kuti cifukwa cokwiya, Davide anaganiza zakuti akaphe Nabala na a m’nyumba yake onse. Ndipo patapita nthawi, Davide anaweluza munthu wa m’fanizo la Natani kuti ayenela kuphedwa pa zimene anacita. Pa cocitika caciŵilici, tingadabwe kuti n’cifukwa ciani Davide anaweluza wakubayo mouma mtima conco. Ganizilani mmene anali kumvelela. Pa nthawiyo, Davide anali na cikumbumtima comuimba mlandu. Munthu akaweluza ena mopanda cifundo, zimaonetsa kuti sali pa ubale wabwino na Yehova. Yesu anacenjeza ophunzila ake mwamphamvu kuti: “Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe, pakuti ciweluzo cimene mukuweluza naco ena inunso mudzaweluzidwa naco.” (Mat. 7:1, 2) Conco, tiyeni tizipewa kucita zinthu mouma mtima, koma tiziyesetsa kukhala ‘acifundo cacikulu,’ potengela citsanzo ca Mulungu wathu.

21-22. Ni njila zina ziti zimene tingaonetsele cifundo?

21 Cifundo si mmene munthu amamvelela cabe mumtima. Munthu wacifundo amathandiza ena. Conco, tonsefe tizikhala chelu kuti tione anthu amene tingathandize, kaya ni m’banja mwathu, mu mpingo, kapena m’dela lathu. Kukamba zoona, pali njila zambili za mmene tingaonetsele cifundo. Kodi pali amene akufunikila thandizo? Mungamuthandize mwina mwa kum’patsa cakudya kapena kum’citila cinthu cina cabwino. Kodi Mkhristu amene anabwezedwa mu mpingo akufunikila anzake abwino omulimbikitsa? Kodi tingauzeko ena uthenga wabwino wotonthoza? Iyi ni njila yabwino zedi yoonetsela cifundo kwa aliyense amene tapeza.—Yobu 29:12, 13; Aroma 10:14, 15; Yak. 1:27.

22 Tikamakhala chelu kuti tione amene akufunikila thandizo, tidzaona kuti pali mipata yambili yowaonetsela cifundo. Tikamacitila anthu cifundo, timakondweletsa Atate wathu wakumwamba, amene ni Mulungu “wacifundo cacikulu.”

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Yehova amaonetsa cifundo cifukwa ciani?

  • N’cifukwa ciani n’cifundo kucotsa munthu mu mpingo?

  • N’ciani cingatithandize kukhala acifundo?

NYIMBO 43 Pemphelo la Mayamiko

a Cifundo ni khalidwe limodzi mwa makhalidwe a Yehova abwino ngako, komanso limene tonsefe tiyenela kukulitsa. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake Yehova amaonetsa cifundo, ndiponso cifukwa cake tingakambe kuti cilango cake cimaonetsa cifundo. Tikambilanenso mmene tingaonetsele acifundo monga Yehova.

b Kuti mudziŵe zimene anthu obwezeletsedwa mu mpingo angacite kuti akonzenso ubale wawo na Mulungu, komanso mmene akulu angawathandizile, onani nkhani yakuti, “Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova,” m’magazini ino.

c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Ali pa mtenje wa nyumba, tate akuona mwana wake woloŵelela akubwelela ku nyumba, ndipo akum’thamangila kuti akam’kumbatile.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pokhala na cikumbumtima comuimba mlandu, Mfumu Davide wakwiya kwambili, ndipo akukamba mwaukali kuti munthu wa m’fanizo la Natani ayenela kuphedwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani