NKHANI YOPHUNZILA 46
Inu Okwatilana Caposacedwa—Ikani Mtima Wanu pa Kutumikila Yehova
“Yehova ndiye mphamvu yanga . . . Mtima wanga umam’khulupilila.”—SAL. 28:7.
NYIMBO 131 “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”
ZIMENE TIKAMBILANEa
1-2. (a) N’cifukwa ciani amene akwatilana caposacedwa ayenela kudalila Yehova? (Salimo 37:3, 4) (b) Tikambilane ciani m’nkhani ino?
KODI mukukonzekela kuloŵa m’banja, kapena munakwatilana caposacedwa? Ngati n’conco, mosakayikila mukuyembekezela kukhala na umoyo wacimwemwe pamodzi na munthu amene mumam’konda kwambili. N’zoona kuti ukwati uli na mavuto ake, ndipo okwatilanawo amafunika kupanga zisankho zofunika kwambili. Zimene mumacita pothetsa mavuto komanso popanga zisankho, zingakhudze cimwemwe canu mu ukwati kwa zaka zambili. Mukadalila Yehova, mudzapanga zisankho zanzelu, ukwati wanu udzalimba, komanso mudzakhala acimwemwe. Koma mukanyalanyaza malangizo a Mulungu, mungakumane na mavuto amene angapangitse kuti musoŵe cimwemwe m’banja mwanu.—Ŵelengani Salimo 37:3, 4.
2 Nkhani ino analembela maka-maka amene analoŵa m’banja posacedwa, koma ifotokoza zovuta zimene onse ali pa banja angakumane nazo. Ifotokozanso zimene tingaphunzile ku zitsanzo za amuna komanso akazi okhulupilika ochulidwa m’Baibo. Zitsanzo zimenezo, n’zothandiza pa mbali zosiyana-siyana mu umoyo wathu, kuphatikizapo m’banja. Tionenso zimene tingaphunzile pa zitsanzo zamakono za anthu okwatilana.
NI ZOVUTA ZITI ZIMENE OKWATILANA CAPOSACEDWA ANGAKUMANE NAZO?
Ni zisankho zotani zimene zingalepheletse okwatilana catsopano kuwonjezela utumiki wawo kwa Yehova? (Onani ndime 3-4)
3-4. Ni zovuta ziti zimene okwatilana caposacedwa angakumane nazo?
3 Anthu ena angalimbikitse amene akwatilana posacedwa kukhala na umoyo mofanana na ena onse. Mwacitsanzo, makolo komanso acibale ena angawakakamize kuti ayambe kukhala na ŵana mwamsanga. Kapena mabwenzi awo angawalimbikitse kugula nyumba na katundu wabwino.
4 Ngati sangasamale, okwatilanawo angapange zisankho zimene zingawaloŵetse m’nkhongole. Kuti abweze nkhongoleyo, mwamuna na mkazi mwina angafunike kuseŵenza maola ambili. Nchitoyo ingayambe kuwadyela nthawi yocita phunzilo la munthu mwini, kulambila kwa pa banja, komanso kulalikila. Okwatilanawo angayambe kuphonyanso misonkhano n’colinga cakuti aseŵenze ovataimu kuti apeze ndalama zowonjezeleka, kapena kuteteza nchito yawo. Cotulukapo cake, iwo amaphonya mipata yambili yowonjezela utumiki wawo kwa Yehova.
5. Kodi muphunzilapo ciani pa citsanzo ca Klaus na mkazi wake Marisa?
5 Zitsanzo zambili zionetsa kuti kuika maganizo athu pa kufuna-funa zinthu zakuthupi sikubweletsa cimwemwe. Onani zimene Klaus na mkazi wake Marisa anaphunzilapo pa mfundo imeneyi.b Pamene anakwatilana, n’kuti onse aŵili akugwila nchito masiku onse kuti akhale na umoyo wabwino. Komabe, iwo sanali okhutila. Klaus anati: “Tinali na zinthu zambili zakuthupi kuposa zimene tinali kufunikila, koma tinalibe zolinga zauzimu. Kukamba zoona, umoyo wathu sunali waphindu, ndipo tinali a nkhawa.” Mwina inunso mwaona kuti kusumika maganizo pa zinthu zakuthupi sikunakubweletseleni cimwemwe. Koma musalefuke. Kuganizila zitsanzo zabwino za ena kungakuthandizeni pa nkhani imeneyi. Coyamba, tiyeni tikambilane zimene amuna okwatila angaphunzile pa citsanzo ca Mfumu Yehosafati.
MOFANANA NA MFUMU YEHOSAFATI, DALILANI YEHOVA
6. Malinga na malangizo apa Miyambo 3:5, 6, Kodi Mfumu Yehosafati anacitanji atakumana na vuto lalikulu?
6 Inu amuna okwatila, kodi nthawi zina mumazizila m’nkhongono mukaona kukula kwa maudindo anu? Ngati n’conco, mungalimbikitsidwe kwambili na citsanzo ca Mfumu Yehosafati. Monga mfumu, Yehosafati anali na udindo woteteza mtundu wonse! Kodi iye anausamalila bwanji udindo waukulu umenewo? Iye anacita zonse zotheka kuti ateteze anthu amene anali kuyang’anila. Analimbitsa mizinda ya Yuda, komanso kusonkhanitsa asilikali amphamvu oposa 1,160,000. (2 Mbiri 17:12-19) Patapita nthawi, Yehosafati anakumana na vuto lalikulu. Gulu la asilikali la Aamoni, Amowabu, komanso amuna a kudela la mapili la Seiri, anawopseza iye, banja lake, na anthu ake. (2 Mbiri 20:1, 2) Kodi Yehosafati anacita ciani? Iye anayang’ana kwa Yehova kuti amuthandize na kum’patsa mphamvu. Izi zinali zogwilizana na malangizo anzelu a pa Miyambo 3:5, 6. (Ŵelengani.) Pemphelo la Yehosafati la pa 2 Mbiri 20:5-12, linaonetsa kuti iye anali kudalila kwambili Atate wake wacikondi wakumwamba. Kodi Yehova anayankha bwanji pemphelo la Yehosafati?
7. Kodi Yehova analiyankha bwanji pemphelo la Yehosafati?
7 Yehova anakamba na Yehosafati kupitilila mwa Mlevi wina dzina lake Yahazieli. Yehova anati: “Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.” (2 Mbiri 20:13-17) Umu si mmene anthu anali kumenyela nkhondo. Koma malangizo amenewo anacokela kwa Yehova osati kwa munthu. Yehosafati anacita zonse zimene anauzidwa cifukwa anali kukhulupilila kwambili Mulungu wake. Iye na anthu ake atapita kuti akacite nkhondo na adani awo, Yehosafati anaika kutsogolo gulu la oimba m’malo motsogoza asilikali odziŵa kumenya nkhondo. Yehova anayankha pemphelo la Yehosafati mwa kugonjetsa gulu la asilikali la adani ake.—2 Mbiri 20:18-23.
Okwatilana catsopano angaike mtima wawo pa kutumikila Yehova mwa kupemphela na kuŵelenga Mawu ake (Onani ndime 8, 10)
8. Kodi amuna okwatila angaphunzile ciani pa citsanzo ca Yehosafati?
8 Inu amuna okwatila, phunzilani pa citsanzo ca Yehosafati. Muli na udindo woyang’anila banja lanu, n’cifukwa cake mumagwila nchito molimbika kuti muteteze na kusamalila banja lanu. Mukakumana na mavuto, mwina mungaone kuti mungakwanitse kuwathetsa pamwekha. Pewani mzimu wodzidalila. M’malo mwake, pemphani Yehova panokha kuti akuthandizeni. Cinanso, muzipemphela na mkazi wanu mocokela pansi pa mtima. Funsilani malangizo kwa Yehova mwa kuŵelenga Baibo na zofalitsa zimene gulu la Mulungu limapeleka, ndipo muziseŵenzetsa malangizo ake. Ena sangagwilizane na zisankho zanu zozikidwa pa Baibo, ndipo angafike pokuuzani kuti mukucita zinthu mopanda nzelu. Iwo angakuuzeni kuti ndalama na katundu ndizo zingateteze bwino banja lanu. Koma kumbukilani citsanzo ca Yehosafati. Iye anadalila Yehova, ndipo anaonetsa zimenezo mwa zocita zake. Yehova sanamusiye munthu wokhulupilika ameneyu, ndipo inunso sadzakusiyani. (Sal. 37:28; Aheb. 13:5) Kodi anthu okwatilana angacite ciani kuti akhale na umoyo wacimwemwe?
MOFANANA NA MNENELI YESAYA KOMANSO MKAZI WAKE, IKANI MTIMA WANU PA KUTUMIKILA YEHOVA
9. Kodi tingati ciani za mneneli Yesaya na mkazi wake?
9 Mneneli Yesaya na mkazi wake anaika patsogolo kutumikila Yehova mu umoyo wawo. Yesaya anali mneneli, ndipo n’kutheka kuti nayenso mkazi wake anali kugwila nchito ya uneneli, cifukwa amachulidwa kuti “mneneli wamkazi.” (Yes. 8:1-4) Monga banja, Yesaya na mkazi wake anasumika maganizo awo pa kulambila Yehova. Iwo ni citsanzo cabwino ngako kwa anthu okwatilana!
10. Kodi kuphunzila maulosi a m’Baibo kungathandize bwanji okwatilana kucita zambili mu utumiki wa Yehova mmene angathele?
10 Masiku anonso, anthu okwatilana angacite zonse zotheka kuti aike mtima wawo pa kutumikila Yehova. Iwo angalimbitse cikhulupililo cawo mwa Yehova, ngati aphunzila maulosi a m’Baibo capamodzi, na kuona mmene amakwanilitsidwila nthawi zonse.c (Tito 1:2) Angaganizileko zimene angacite pothandiza kukwanilitsa maulosi ena a m’Baibo. Mwacitsanzo, iwo angatengepo gawo pokwanilitsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Anthu ali pa banja akatsimikiza kuti maulosi a m’Baibo amakwanilitsikadi, adzakulitsa cifuno cawo cocita zambili mu utumiki wa Yehova mmene angathele.
MONGA PURISIKILA KOMANSO AKULA, IKANI ZINTHU ZA UFUMU PATSOGOLO
11. Kodi Purisikila na Akula anakwanitsa kucita ciani? Nanga cifukwa ciani?
11 Okwatilana catsopano angapindule na citsanzo ca Purisikila na Akula, banja laciyuda limene linali kukhala mu mzinda wa Roma. Iwo anali atamva za uthenga wabwino wonena za Yesu, ndipo anakhala Akhristu. Mosakayikila, anali okhutila na umoyo wawo. Komabe, zinthu zinasintha mwadzidzidzi pamene Mfumu Kalaudiyo analamula kuti Ayuda onse acoke m’dziko la Roma. Ganizilani mmene izi zinakhudzila Akula na Purisikila. Iwo anafunika kucoka ku malo amene anazolowela, kupeza nyumba yatsopano, na kuyambanso bizinesi yawo yosoka matenti ku malo atsopano. Kodi kusintha kwa zinthu pa umoyo wawo kunawapangitsa kuleka kuika zinthu za Ufumu patsogolo? N’kutheka kuti yankho lake mukuidziŵa. Atafika ku Korinto ku malo awo atsopano, Akula na Purisikila anagwilizana na mpingo wa kumeneko, komanso anayamba kutumikila pamodzi na mtumwi Paulo kuti alimbikitse abale. Patapita nthawi, iwo anasamukila m’matauni ena kumene alengezi a Ufumu anali ocepa kwambili. (Mac. 18:18-21; Aroma 16:3-5) Iwo ayenela kuti anasangalala kwambili na umoyo wopindulitsa umenewo!
12. N’cifukwa ciani anthu okwatilana ayenela kudziikila zolinga zauzimu?
12 Anthu amene ali pa banja angatengele citsanzo ca Purisikila na Akula, akaika zinthu za Ufumu patsogolo. Nthawi yabwino imene angakambilane zolinga zawo zauzimu, m’pamene ali pa cibwenzi. Anthu ali pa banja akamapanga zisankho pamodzi, komanso kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zina zauzimu, adzakhala na mipata yambili yoona mmene Yehova akuwathandizila. (Mlal. 4:9, 12) Ganizilani citsanzo ca Russell na Elizabeth. Russell anati, “Tisanakwatilane, tinali kukambilana zolinga zathu zauzimu.” Elizabeth anati, “Tinali kukambilana zimenezi na colinga cakuti tikakafuna kupanga zisankho mtsogolo, tikaonetsetse kuti zisankho zimenezo sizikutilepheletsa kukwanilitsa zolinga zathu zauzimu.” Malinga na mmene zinthu zinalili kwa iwo, Russell na mkazi wake Elizabeth anapita kukatumikila ku malo osoŵa ku Micronesia.
Okwatilana catsopano angaike mtima wawo pa kutumikila Yehova mwa kudziikila zolinga zauzimu (Onani ndime 13)
13. Malinga na Salimo 28:7, kodi padzakhala zotulukapo zotani tikakhulupilila Yehova?
13 Potengela citsanzo ca Russell na mkazi wake Elizabeth, okwatilana ambili asankha kutaila nthawi yawo yoculuka pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. Ngati mwamuna na mkazi wake amadziikila zolinga mu utumiki wa Yehova na kuzikwanilitsa, pamakhala zotulukapo zabwino. Iwo amaona mmene Yehova amawasamalila, cikhulupililo cawo mwa iye cimakula, ndipo amakhala na cimwemwe ceniceni.—Ŵelengani Salimo 28:7.
MONGA MTUMWI PETULO NA MKAZI WAKE, KHULUPILILANI MALONJEZO A YEHOVA
14. Kodi mtumwi Petulo na mkazi wake anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila lonjezo lopezeka pa Mateyu 6:25, 31-34?
14 Amene anali pa banja angatengenso phunzilo pa citsanzo ca mtumwi Petulo na mkazi wake. Patapita miyezi pafupi-fupi 6 pambuyo poonana na Yesu koyamba, mtumwi Petulo anafunika kupanga cisankho cacikulu. Petulo anali kugwila nchito ya usodzi kuti azisamalila banja lake. Koma Yesu atamuitana kuti azimutsatila nthawi zonse, iye anafunika kuganizila mkazi wake asanapange cisankho cimeneci. (Luka 5:1-11) Petulo anasankha kugwila nchito yolalikila pamodzi na Yesu. Ici cinali cisankho canzelu. Ndipo sitikayikila kuti mkazi wake anagwilizana na cisankho cimeneci. Baibo imaonetsa kuti pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa, Petulo anapita na mkazi wake maulendo angapo kukalalikila. (1 Akor. 9:5) Mosakayikila, citsanzo cake monga mkazi wacikhristu cinathandiza Petulo kukhala na ufulu wa kulankhula pamene anapeleka malangizo kwa amuna na akazi acikhristu. (1 Pet. 3:1-7) Mwacionekele, Petulo na mkazi wake anali kukhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzawasamalila ngati aika Ufumu wake patsogolo.—Ŵelengani Mateyu 6:25, 31-34.
15. Kodi mwaphunzila ciani pa citsanzo ca Tiago na mkazi wake Esther?
15 Ngati mwakhala m’banja zaka zocepa, mungacite ciani kuti mupitilize kukulitsa cifuno canu cowonjezela utumiki wanu? Njila imodzi ni kuphunzila pa zitsanzo za anthu ena ali pa banja. Mwacitsanzo, mungaŵelenge nkhani zakuti, “Anadzipeleka na Mtima Wonse.” Nkhani zimenezo zinathandiza Tiago na mkazi wake Esther, a ku Brazil, kukulitsa cifuno cawo cokatumikila kumalo osoŵa. Tiago anati: “Tikamaŵelenga nkhani zoonetsa mmene Yehova anathandizila atumiki ake amakono, nafenso tinafuna kuona dzanja la Yehova likutitsogolela na kutisamalila.” Posakhalitsa, iwo anasamukila ku Paraguay, ndipo akhala akutumikila m’gawo la Cipwitikizi kucokela mu 2014. Esther anati: “Lemba limene timakonda ni Aefeso 3:20. Nthawi zambili, taona kukwanilitsidwa kwa mawu amenewa mu utumiki wathu kwa Yehova.” M’kalata imeneyo yopita kwa Aefeso, Paulo anatilonjeza kuti Yehova adzatipatsa zoculuka kuposa zimene tingamupemphe. Lonjezoli limakwanilitsidwa nthawi zonse.
Okwatilana catsopano angaike mtima wawo pa kutumikila Yehova mwa kufunsila malangizo kwa Akhristu okhwima kuuzimu (Onani ndime 16)
16. Kodi mabanja acinyamata angafunsile malangizo kwa ndani akamaganizila zodziikila zolinga?
16 Mabanja acinyamata angapindule na zitsanzo za anthu ena amene anaphunzila kudalila Yehova. Mabanja ena akhala mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka zambili. Bwanji osafunsila malangizo kwa iwo ngati mukuganizila zodziikila zolinga. Iyi ni njila ina imene mungaonetsele kuti mumadalila Yehova. (Miy. 22:17, 19) Naonso akulu angathandize mabanja acinyamata kudziikila zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa.
17. N’ciani cinacitika kwa Klaus na mkazi wake Marisa? Nanga tiphunzilapo ciani kwa iwo?
17 Koma nthawi zina, colinga cathu cofuna kuwonjezela utumiki sicingakwanilitsike mmene tinali kufunila. Ganizilani citsanzo ca Klaus na mkazi wake Marisa, amene tachula kumayambililo. Atakhala mu ukwati zaka zitatu, iwo anasiya nyumba yawo na kudzipeleka kuti akathandize kumanga nthambi ya ku Finland. Komabe, anauzidwa kuti sangaloledwe kukhala kumeneko kupitilila miyezi 6. Poyamba, iwo sanakondwele. Koma posakhalitsa, anaitanidwa kuti akaloŵe sukulu yophunzitsa ci Arabic. Tsopano, iwo akutumikila mwacimwemwe m’gawo la anthu okamba ci Arabic ku dziko lina. Pokumbukila zinacitika, Marisa anati: “N’nali kudodoma kucita zinthu zimene sin’nacitepo, ndipo n’nafunika kudalila Yehova na mtima wonse. Koma naona mmene Yehova wakhala akutithandizila m’njila zimene sitinali kuyembekezela. Izi zitacitika, cidalilo canga mwa Yehova calimbilako.” Monga mmene citsanzo ici cionetsela, mungakhale na cidalilo cakuti Yehova adzakufupani nthawi zonse ngati mumam’khulupilila na mtima wonse.
18. Kodi anthu okwatilana angacite ciani kuti apitilize kudalila Yehova?
18 Ukwati ni mphatso yocokela kwa Yehova. (Mat. 19:5, 6) Iye amafuna kuti okwatilana azikondwela na mphatso imeneyi. (Miy. 5:18) Inu mabanja acinyamata, bwanji osapenda mmene mukuseŵenzetsela umoyo wanu. Kodi mukucita zonse zotheka kuti muonetse Yehova kuti mukuyamikila mphatso imene anakupatsani? Kambilanani na Yehova m’pemphelo. Fufuzani mfundo zothandiza m’Mawu ake zogwilizana na mmene zinthu zilili kwa imwe. Kenaka, tsatilani malangizo amene Yehova amakupatsani. Dziŵani kuti mudzakhala na umoyo wacimwemwe komanso wopindulitsa, mukaika mtima wanu pa kutumikila Yehova.
NYIMBO 132 Lomba Ndise Thupi Limodzi
a Zisankho zina zimene timapanga zingakhudze nthawi na mphamvu zathu potumikila Yehova. Amene akwatilana posacedwa angafunike kupanga zisankho zimene zingakhudze umoyo wawo kwa nthawi yaitali. Nkhani ino, idzawalimbikitsa kupanga zisankho zimene zingawathandize kukhala na umoyo wopindulila.
b Maina ena asinthidwa
c Monga citsanzo cabe, mungaŵelenge macaputala 6, 7, komanso 19 m’buku la Cizungu lakuti, Pure Worship of Jehovah—Restored At Last!