LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp23 na. 1 masa. 6-7
  • 1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Kucita Zimenezi Kungatithandizile
  • Tulilani Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Mmene Tingathanilane Nazo Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
wp23 na. 1 masa. 6-7
Mnyamata wopanikizika maganizo waika dzanja pa cifuwa pamene akupemphela.

1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”

BAIBO IMATI: ‘Mutulileni Mulungu, nkhawa zanu zonse. Pakuti amakudelani nkhawa.’—1 PETULO 5:7.

Tanthauzo Lake

Yehova Mulungu akutipempha kuti tizimuuza nkhawa zilizonse zimene tili nazo. (Salimo 55:22) Palibe vuto lalikulu kwambili kapena laling’ono kwambili limene sitingamuuze m’pemphelo. Ngati ife tiona kuti ni vuto, ndiye kuti nayenso Yehova amaona kuti ni vuto cifukwa amasamala za ife. Kupemphela kwa iye n’kofunika cifukwa kumatithandiza kukhala na mtendele wa mumtima.—Afilipi 4:6, 7.

Mmene Kucita Zimenezi Kungatithandizile

Tikamadwala matenda a maganizo, tingaone monga kuti palibe aliyense amene akuona zimene tikupitamo. Zili conco cifukwa nthawi zina anthu sangamvetse vuto lathu. (Miyambo 14:10) Koma tikamuuza Mulungu mocokela pansi pa mtima mmene tikumvela, iye adzatimvetsela mokoma mtima. Yehova amationa. Amadziŵa zimene zimatipweteka mtima komanso mavuto amene timakumana nawo. Ndipo amafuna kuti tizimuuza m’pemphelo zilizonse zimene zimatidetsa nkhawa.—2 Mbiri 6:29, 30.

Kupemphela kwa Yehova kungalimbitse cidalilo cathu cakuti iye amasamala za ife. Tingamve mmene wamasalimo anamvela pamene anapemphela kuti: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwela.” (Salimo 31:7) Kungodziŵa kuti Yehova amaona mavuto amene timapitamo, kungatithandize kupitiliza kupilila mavutowo. Koma sikuti Mulungu amangowaona mavutowo. Amacitapo kanthu. Kuposa munthu wina aliyense, Yehova amamvetsetsa mavuto amene timakumana nawo, ndipo amatithandiza kupeza cilimbikitso m’Baibo.

Mmene Baibo Imathandizila Julian

Mmene Nimavutikila na Nkhawa

Julian.

“Nimavutika na nkhawa komanso matenda a maganizo amene amapangitsa kuti nizicita zinthu mobweleza-bweleza. Nkhawa imangonibwelela mosayembekezeleka. Pa nthawi ina, nimakhala bwino-bwino. Koma posakhalitsa nimakhala na nkhawa kwambili popanda cifukwa comveka. Nkhawa imakula maka-maka nikakhala pa anthu, cifukwa sinidziŵa mmene amanionela.

“Anzanga amene adziŵa za vuto langa, amayesetsa kunithandiza. N’zoona kuti nthawi zina iwo amakamba zinthu zosathandiza kwenikweni. Koma nimayamikila kuyesayesa kwawo pofuna kunithandiza.

“Nthawi zina, nkhawa komanso matenda anga a maganizo zimapangitsa kuti kupemphela kukhale kovuta. Pamafunika khama kuti maganizo anga asamayendeyende pamene nifuna kukamba na Yehova m’pemphelo. Maganizo anga amayendayenda kwambili moti nthawi zambili nimasokonezeka. Zikakhala conco, zimanivuta kum’fotokozela Yehova maganizo anga komanso mmene nikumvela.”

Mmene Baibo Imanithandizila

“M’Baibo n’naphunzila kuti pemphelo silifunika kucita kukhala lalitali, kapena lokambidwa mwaluso kuti Mulungu alimve. Nthawi zina zikanivuta kufotokoza mmene nikumvela, nimangopemphela kuti: ‘Yehova, conde nithandizeni.’ Ngakhale nipemphele mwacidule conco, nimadziŵa kuti Yehova wanimvetsetsa, ndipo anipatsa zimene nikufunikila panthawiyo. Kuwonjezela pa kupemphela, nimalandilanso thandizo la kucipatala. Ndine wokondwa kuti cifukwa ca zinthu ziŵilizi, vuto langa tsopano linacepako. Nimafunika kuyesetsa mwamphamvu kuti nipemphe thandizo kwa Atate wanga wakumwamba. Koma nimacitabe zimenezi cifukwa nimadziŵa kuti iye amanikonda ndiponso amafuna kunithandiza.”

Mfundo Zothandiza kwa Acinyamata

Vidiyo yakuti “Khala Bwenzi la Yehova—Muzipemphela Nthawi Zonse.”

Pitani pa webusaiti ya jw.org, kuti muone cifukwa cake mungakhale wotsimikiza kuti Yehova amamva na kuyankha mapemphelo anu.

Onelelani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Muzipemphela Nthawi Zonse

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani