LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp24 na. 1 tsa. 3
  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Nkhani Zofanana
  • Khalani ndi Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
wp24 na. 1 tsa. 3
Mnyamata yemwe ali pa tsamba loyamba akupempha thandizo kwa woyang’anila malo osungilako nyama. Iye akuseŵenzetsa mapu pothandiza wacinyamatayo kuona njila imene ingamupeleke komwe akupita, kumene ni pamwamba pa phili.

Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika

Kodi mungacite ciyani ngati mufuna kupita ku malo amene n’kuyamba kupitako?

  1. 1. Kuloŵela njila imene inuyo mukuganiza kuti ndiyo yabwino.

  2. 2. Kutsatila ena poganiza kuti ndiwo akudziŵa njila yoyenela.

  3. 3. Kugwilitsa nchito cipangizo codalilika codziŵila njila monga kampasi kapena mapu, kapenanso kufunsila kwa mnzanu wodalilika amene adziŵa njila.

Mukacita zimene zili pa 1, kapena pa 2, mungasocele. Koma mukacita zimene zili pa 3, mosakayikila mungafike kumene mukufuna.

Umoyo wathu uli ngati ulendo. Pamene tili pa ulendowu, timayembekezela kudzakhala na umoyo wacimwemwe. Kuti tikafike kumene tikupita zimadalila kwambili pa malangizo amene timatsatila popanga zisankho.

Zisankho zambili zimene timapanga pa umoyo wathu zimakhala zazing’ono, koma zina zimakhala zazikulu. Zisankho zazikulu zimenezi zimaonetsa mmene timaonela zinthu pa nkhani ya coyenela na cosayenela. Zisankho zimenezi zingakhudze ifeyo komanso okondedwa athu kwa nthawi yaitali. Zisankhozi ni zokhudza nkhani monga:

  • Kugonana komanso ukwati

  • Kuona mtima, nchito, komanso ndalama

  • Molelela ana

  • Mocitila zinthu na anthu ena

Kodi mungadziŵe bwanji kuti zisankho zanu pa nkhani zimenezi zidzakuthandizani inuyo na banja lanu kukhala na tsogolo labwino?

Funso limene tonsefe tiyenela kudzifunsa ni ili: Kodi ningapeze kuti malangizo amene anganithandize kupanga zisankho zabwino pa umoyo?

Magazini ino ifotokoza cifukwa cake Baibo ni buku la malangizo odalilika komanso othandiza pa umoyo. Ifotokozanso mmene Baibo ingakuthandizileni.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani