LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp24 na. 1 masa. 4-5
  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUDALILA MAGANIZO ATHU
  • KUYENDELA MAGANIZO A ANTHU ENA
  • KODI N’CIYANI CINGATITHANDIZE KUSANKHA ZOCITA MWANZELU?
  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Kufunika kwa Makhalidwe Abwino
    Galamuka!—2019
  • Khalani Na Cikumbumtima Cabwino Kwa Mulungu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
wp24 na. 1 masa. 4-5
Mnyamata amene taona pa cithunzi m’nkhani yapita, akuseŵenzetsa kampasi pokwela phili ndipo wafika m’mbali mwa cidzenje.

Kodi kutsatila maganizo athu kungatithandize kupanga zisankho zabwino nthawi zonse?

Mmene Ambili Amasankhila Zocita

Pafupifupi munthu aliyense amavomeleza kuti zinthu zina n’zoonekelatu kuti n’zoyenela pamene zina n’zosayenela. Mwa citsanzo, anthu ambili amaona kuti kupha munthu, kugona munthu mwacikakamizo, komanso kucitila ana nkhanza zakugonana n’kulakwa. Ndipo amaona kuti makhalidwe monga cilungamo, ubwino komanso cifundo ni abwino kwambili. Koma pa nkhani zina, monga za kugonana, kuona mtima, kapena kulela ana, anthu ambili amaona kuti aliyense ali na ufulu wocita zimene wakonda. Amaganiza kuti ciliconse cimene munthu angacite n’cabwino. Nthawi zambili anthu amapanga zisankho potengela maganizo awo komanso mmene anthu ena amaonela nkhaniyo. Kodi njila imeneyi ni yodalilika?

KUDALILA MAGANIZO ATHU

Nthawi zambili anthufe timasankha zocita malinga na kaonedwe kathu ka zinthu. Timatsatila zimene cikumbumtima cathu cikutiuza. Cikumbumtima ni liwu la mumtima limene limatiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. (Aroma 2:​14, 15) Ngakhale ana aang’ono amatha kusiyanitsa pakati pa cilungamo na kupanda cilungamo, ndipo amadziimba mlandu akalakwitsa cinacake. M’kupita kwa nthawi, cikumbumtima cathu cimayamba kutengela zimene timaphunzila kwa a m’banja lathu, anzathu, aphunzitsi, anthu a m’dela lathu, cipembedzo cathu, komanso cikhalidwe cathu. Ndipo popanga zisankho, cikumbumtimaco cimatiuza ngati cosankhaco n’cogwilizana na mfundo za makhalidwe zimene tinaphunzila kapena ayi.

Cikumbumtima cingatilimbikitse kuganizila ena, kuŵayamikila, kuŵacitila cilungamo, na kuŵaonetsa cifundo. Cingatilimbikitsenso kupewa kucita zinthu zimene zingakhumudwitse anthu amene timaŵakonda, kapena zimene zingaticotsele ulemu, kuticititsa manyazi kapena kutipangitsa kudziimba mlandu.

Kodi kudalila maganizo athu posankha zocita n’kothandiza nthawi zonse? Pofotokoza za umoyo wake ali wacinyamata, Garrick anati: “N’nali kucita ciliconse cimene naona kuti n’cabwino kwa ine.” Koma m’kupita kwa nthawi, iye anadziŵa kuti kucita zinthu zimene anali kuona kuti n’zabwino kwa iye kunali kukhala na zotulukapo zoipa. Zimenezi zinamupangitsa “kukhala munthu waciwelewele, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo, kuledzela na kukhala waciwawa.”

KUYENDELA MAGANIZO A ANTHU ENA

Kuwonjezela pa maganizo athu, nthawi zambili timacita zinthu potengela mmene anthu ena amaonela zisankho zathu. Kucita izi kungatithandize kupindula na cidziŵitso cawo komanso nzelu zawo. Timalemekezedwa na anthu a m’banja lathu, anzathu, komanso anthu a m’dela lathu tikamacita zinthu zimene iwo amaona kuti n’zoyenela.

Kodi kutsatila maganizo a anthu ena posankha zocita n’kothandiza nthawi zonse? Pamene anali mtsikana, Priscila anayamba kucita zaciwelewele potengela zimene anzake ambili anali kucita, ndipo sanali kudziimba mlandu. Anthu ena anali kuona kuti zimene anali kucita n’zabwino, ngakhale n’telo iye sanali kukhala wacimwemwe. Priscila anati: “Kutengela zimene ambili anali kucita sikunanipangitse kukhala na umoyo wabwino. M’malomwake, n’nayamba kucita zinthu mopanda nzelu, zimene zikanawonongetsa moyo wanga.”

KODI N’CIYANI CINGATITHANDIZE KUSANKHA ZOCITA MWANZELU?

Maganizo athu komanso maganizo a anthu ena angatithandize kwambili posankha coyenela na cosayenela kucita. Koma kudalila cabe maganizo athu kapena a anthu ena, nthawi zina sikukhala na zotulukapo zabwino. Cifukwa colephela kuonelatu zotulukapo za zisankho zathu, nthawi zina tingacite zinthu zimene zingatibweletsele mavuto na kuvutitsanso anthu ena. (Miyambo 14:12) Komanso ngakhale zimene ifeyo na anthu ena timaziona kuti n’zabwino zingakhale zolakwika, ndipo zingasinthe m’kupita kwa nthawi. Mwa citsanzo, makhalidwe ena amene kale anthu anali kuwaona kuti ni oipa, lomba amawaona kuti ni abwino. Ndipo makhalidwe amene kale anthu anali kuwaona kuti ni abwino, masiku ano amawaona kuti ni oipa.

Mnyamatayo waimilila pa msewu wa miyala wokhala na zikwangwani zocenjeza. Anthu ena akunyalanyaza zikwangwanizo.

Kodi kutsatila maganizo a anthu ena kungatithandize kupanga zisankho zabwino nthawi zonse?

N’kuti kumene tingapeze malangizo anzelu amene angatithandize kudziŵa coyenela na cosayenela? Kodi pali malangizo a makhalidwe abwino amene ngati tawatsatila masiku ano sangakatibweletsele mavuto m’tsogolo?

N’zokondweletsa kudziŵa kuti pali buku la malangizo a makhalidwe abwino limene lingathandize anthu onse, kulikonse padzikoli. Malangizo ake ni odalilika ndipo sasintha. Nkhani yotsatila ifotokoza kumene tingapeze malangizo odalilika otithandiza kudziŵa coyenela na cosayenela.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani