Baibo Ni Gwelo la Malangizo Odalilika
Ngati timangoyendela maganizo athu kapena a anthu ena posankha zocita, sitingakhale otsimikiza kuti zimene tikucitazo zidzakhala na zotulukapo zabwino. Baibo imafotokoza cifukwa cake zili conco. Koma ilinso na malangizo odalilika amene angatithandize kukhala na umoyo wabwino.
TIMAFUNIKILA MALANGIZO OCOKELA KWA MULUNGU
M’Baibo, Yehovaa Mulungu amatiuza kuti sanalenge anthu kuti azidzitsogolela okha, koma kuti azidalila iye kuti aŵatsogolele. (Yeremiya 10:23) Ndiye cifukwa cake anapeleka malangizo abwino opezeka m’Baibo. Iye amatikonda ife anthu, ndipo safuna kuti tipange zisankho zolakwika zimene zingatibweletsele mavuto aakulu pa umoyo wathu. (Deuteronomo 5:29; 1 Yohane 4:8) Komanso iye angatipatse malangizo abwino kwambili cifukwa ni Mlengi wathu, ndipo ali na nzelu kwambili komanso amadziŵa zambili. (Salimo 100:3; 104:24) Komabe, Mulungu sakakamiza anthu kuti azitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino.
Yehova anapatsa mwamuna na mkazi woyamba, Adamu na Hava, zonse zimene anali kufunikila kuti akhale na cimwemwe ceniceni. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 15) Anaŵapatsanso malangizo osavuta, ndipo anali kufuna kuti iwo aziwatsatila. Komabe, anaŵalola kudzisankhila okha kaya kutsatila malangizowo kapena ayi. (Genesis 2:9, 16, 17) N’zacisoni kuti Adamu na Hava anasankha kutsatila zofuna zawo m’malo motsatila miyezo ya Mulungu. (Genesis 3:6) Kodi pakhala zotulukapo zotani? Kodi anthu lomba ali na umoyo wacimwemwe cifukwa cokhala na ufulu wocita ciliconse cimene aona kuti n’cabwino? Kutalitali! M’kupita kwa zaka, zadziŵika kuti kunyalanyaza miyezo ya Mulungu sikubweletsa mtendele weniweni kapena cimwemwe.—Mlaliki 8:9.
Baibo ili na malangizo amene angatithandize kupanga zisankho mwanzelu, mosasamala kanthu za kumene tikhala. (2 Timoteyo 3:16, 17; onani bokosi lakuti “Buku la Anthu Onse.”) Onani mmene imatithandizila.
Onani cifukwa cake m’poyenela kunena kuti Baibo ni “Mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13. Tambani vidiyo yakuti Ndani Analemba Baibulo? pa jw.org.
BAIBO IMATIUZA ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI TIZICITA
Baibo imatiuza mmene Yehova wakhala akucitila zinthu na anthu kucokela pa ciyambi. Zomwe zili m’Baibo zimatithandiza kudziŵa zimene Mulungu amaona kuti n’zoyenela kapena zosayenela, zothandiza kapena zovulaza. (Salimo 19:7, 11) Mfundo zake sizikutha mphamvu, ndipo zingatithandize kusankha zinthu mwanzelu pa nkhani ya coyenela na cosayenela.
Mwacitsanzo, onani ulangizi wa pa Miyambo 13:20 umene umati: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma amene amacita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mfundo imeneyi inali yothandiza m’nthawi yakale. Ndipo masiku anonso ni yothandiza. Baibo ni yodzala na malangizo ofunika komanso othandiza ngati amenewa.—Onani bokosi lakuti “Malangizo a m’Baibo Sakutha Mphamvu.”
Mungafunse kuti, ‘Kodi ningatsimikize bwanji kuti malangizo a m’Baibo ni othandiza masiku ano?’ Nkhani yotsatila ifotokoza mmene Baibo yathandizila anthu ena.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.