LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 April masa. 8-13
  • Kulitsani Ciyamikilo Canu pa Gulu la Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kulitsani Ciyamikilo Canu pa Gulu la Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • GULU LATHU LIMATSATILA CITSANZO CA YESU
  • PITILIZANI KUONETSA CIYAMIKILO CANU PA GULU LATHU
  • MUSALOLE ANTHU ENA KUKUPANGITSANI KUKAIKILA GULU LATHU
  • Kodi Mumacizindikila Coonadi?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Pezani Cimwemwe Coculuka Cimene Cimabwela Cifukwa Copatsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 April masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 15

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

Kulitsani Ciyamikilo Canu pa Gulu la Yehova

“Muzikumbukila amene akukutsogolelani. Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu.”—AHEB. 13:7.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene tingalimbitsile ciyamikilo cathu pa gulu la Yehova.

1. Kodi anthu a Yehova a m’zaka za zana loyamba, anali kutsatila dongosolo lotani?

YEHOVA akapatsa anthu ake utumiki, nthawi zonse amawayembekezela kuukwanilitsa mwadongosolo. (1 Akor. 14:33) Mwa citsanzo, Mulungu afuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe pa dziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Yehova anaika Yesu kuti atsogolele nchito imeneyi. Ndipo Yesu amaonetsetsa kuti nchitoyi ikugwilidwa mwadongosolo. M’zaka za zana loyamba pamene mipingo inali kukhazikitsidwa m’madela osiyana-siyana, akulu anali kusankhidwa kuti azipeleka malangizo na kuitsogolela. (Mac. 14:23) Ku Yerusalemu kunali bungwe la akulu limene linapangidwa na atumwi komanso akulu. Bungweli ndilo linali kupanga zigamulo zimene mipingo yonse inali kutsatila. (Mac. 15:2; 16:4) Cifukwa cotsatila malangizo amene anali kulandila, “anthu m’mipingo anapitiliza kukhala ndi cikhulupililo colimba ndipo ciŵelengelo cinkawonjezeka.”—Mac. 16:5.

2. Kodi Yehova wakhala akupeleka motani citsogozo na cakudya cauzimu kucokela mu 1919?

2 Yehova akupitilizabe kutsogolela anthu ake ngakhale masiku ano. Kuyambila mu 1919, Yesu wakhala akuseŵenzetsa kagulu kocepa ka amuna odzozedwa kutsogolela pa nchito yolalikila, komanso kupeleka cakudya cauzimu kwa otsatila ake.a (Luka 12:42) N’zoonekelatu kuti Yehova akudalitsa nchito ya kagulu kameneka.—Yes. 60:22; 65:​13, 14.

3-4. (a) Fotokozani mmene timapindulila cifukwa cokhala adongosolo. (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Tikanakhala opanda dongosolo, sitikanakwanitsa kugwila nchito imene Yesu anatipatsa. (Mat. 28:​19, 20) Yelekezani kuti panalibe dongosolo logaŵila magawo, ndipo aliyense amalalikila kulikonse kumene afuna. Magawo ena angamalalikidwe mobweleza-bweleza na ofalitsa osiyana-siyana, pomwe magawo ena sangamalalikidwe n’komwe. Kodi mungaganizileko njila zina zimene timapindulila cifukwa cokhala adongosolo?

4 Zimene Yesu anacita ali pa dziko lapansi zimatipatsa citsanzo ca mmene tingakhalile adongosolo masiku ano. M’nkhani ino tikambilane citsanzo cimene Yesu anapeleka komanso mmene gulu lathu limatsatilila citsanzo cimeneco. Tikambilanenso mmene tingaonetsele kuti timayamikila gulu la Yehova.

GULU LATHU LIMATSATILA CITSANZO CA YESU

5. Kodi imodzi mwa njila zimene timatsatilila citsanzo ca Yesu ni iti? (Yoh. 8:28)

5 Yesu anaphunzila kwa Atate wake wa kumwamba zimene ayenela kucita, komanso kukamba. Gulu la Yehova limazika ziphunzitso zake zokhudza makhalidwe abwino, na citsogozo cake m’Mawu a Mulungu. Mwa kutelo limatengela citsanzo ca Yesu. (Ŵelengani Yohane 8:28; 2 Tim. 3:​16, 17) Kaŵili-kaŵili, timakumbutsidwa kuti tiziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwaseŵenzetsa pa umoyo wathu. Kodi timapindula motani tikatsatila ulangizi umenewu?

6. Kodi imodzi mwa njila zofunika kwambili zimene timapindulila poŵelenga Baibo ni iti?

6 Timapindula kwambili tikamaŵelenga Baibo na kufufuza m’zofalitsa za gulu lathu. Mwa citsanzo, timatha kufananitsa ziphunzitso za m’Baibo na citsogozo cimene timalandila kucokela ku gulu lathu. Tikaona kuti citsogozo cimene timalandila n’cozikika m’Malemba, cidalilo cathu pa gulu la Yehova cimakula.—Aroma 12:2.

7. Kodi Yesu analalikila uthenga wotani? Nanga gulu la Yehova limatengela bwanji citsanzo cake?

7 Yesu analalikila “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:​43, 44) Cinanso, analamula ophunzila ake kulalikila za Ufumu. (Luka 9:​1, 2; 10:​8, 9) Masiku ano, onse m’gulu la Yehova amalalikila uthenga wa Ufumu mosasamala kanthu za kumene amakhala, komanso maudindo amene ali nawo.

8. Ni mwayi wapadela uti umene tapatsidwa?

8 Ni mwayi wapadela kugaŵilako ena coonadi ca Ufumu wa Mulungu! Si aliyense amene ali na mwayi umenewu. Mwa citsanzo, Yesu ali pa dziko lapansi, sanalole kuti ziŵanda zilalikile zokhudza iye. (Luka 4:41) Masiku ano, munthu asanayambe kulalikila pamodzi na anthu a Yehova, ayenela kukwanilitsa ziyenelezo. Timaonetsa kuti timayamikila mwayi wolalikila umenewu mwa kucitila umboni kulikonse kumene tingakhale, komanso mulimonse mmene tingathele. Mofanana na Yesu, colinga cathu ni kubyala mbewu za coonadi ca Ufumu m’mitima ya anthu na kuzithilila.—Mat. 13:​3, 23; 1 Akor. 3:6.

9. Kodi gulu lathu limawadziŵitsa motani anthu dzina la Mulungu?

9 Yesu anadziŵitsa anthu dzina la Mulungu. Yesu anapemphela kwa Atate wake wa kumwamba kuti: “Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.” (Yoh. 17:26) Potengela citsanzo ca Yesu, gulu la Yehova limacita zonse zotheka kuthandiza anthu kuti adziŵe dzina la Mulungu. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathandizila pamlingo waukulu kukwanilitsa colinga cimeneci mwa kubwezeletsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenelela. Baibo imeneyi, yathunthu kapena mbali yake cabe, imapezeka mu zinenelo zoposa 270. Mu Zakumapeto A4 komanso A5 mudzapezamo mfundo zimene anatsatila pobwezeletsa dzina la Mulungu m’Baibo. Zakumapeto C, zomwe zili m’Baibo Yophunzilila zimapeleka umboni wosatsutsika wakuti dzina la Mulungu liyenela kupezeka m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu nthawi zokwanila 237.

10. Mwaphunzilapo ciyani pa mawu amene mayi wina wa ku Myanmar ananena?

10 Potengela citsanzo ca Yesu, timafuna kuthandiza anthu ambili mmene tingathele kudziŵa dzina la Mulungu. Mayi wina wa zaka 67 wa ku Myanmar anagwetsa misozi atadziŵa kuti Mulungu ali na dzina, ndipo anati: “Mu umoyo wanga wonse, n’kuyamba kumva kuti dzina la Mulungu ni Yehova. . . . Mwaniphunzitsa cinthu cofunika kwambili mu umoyo wanga.” Cocitikaci cionetsa kuti kuphunzila dzina la Mulungu, kungakhudze anthu a maganizo abwino pamlingo waukulu.

PITILIZANI KUONETSA CIYAMIKILO CANU PA GULU LATHU

11. Kodi akulu amaonetsa bwanji kuti amayamikila gulu la Yehova? (Onaninso cithunzi.)

11 Ni njila imodzi iti imene akulu angaonetsele kuti amayamikila gulu la Mulungu? Akalandila malangizo, ayenela kuwaŵelenga mosamala na kuwaseŵenzetsa mmene angathele. Mwa citsanzo, amalandila malangizo a mmene angatsogozele mbali zina za misonkhano, mmene angapelekele mapemphelo pa mpingo, komanso mmene angasamalile nkhosa za Khristu. Akulu amene amatsatila malangizo a gulu amathandiza anthu amene akuwasamalila kumva kuti ni otetezeka, komanso okondedwa.

Cithunzi: 1. Akulu atatu akumana pa Nyumba ya Ufumu kuti akambilane za gawo la mpingo wawo. 2. Pambuyo pake, mmodzi mwa akuluwo akupeleka malangizo kwa alongo aŵili a mmene angaikile kasitandi ka ulaliki wapoyela pa malo otetezeka.

Akulu amatithandiza kutsatila citsogozo ca gulu la Yehova (Onani ndime 11)b


12. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kutsatila malangizo a amene akutitsogolela? (Aheberi 13:​7, 17) (b) N’cifukwa ciyani tiyenela kuika maganizo athu pa zimene otitsogolela amacita bwino?

12 Tikalandila malangizo kucokela kwa akulu, tiyenela kuwatsatila na mtima wonse. Tikatelo, cidzakhala cosavuta kwa iwo kugwila nchito yawo. Baibo imatilimbikitsa kukhala omvela, komanso ogonjela kwa amene akutitsogolela. (Ŵelengani Aheberi 13:​7, 17.) Koma kucita zimenezi si kopepuka nthawi zina. Cifukwa ciyani? Cifukwa iwo ni opanda ungwilo. Komabe, tikamaika maganizo athu pa zophophonya zawo m’malo mwa zimene amacita bwino, tingamathandize adani athu. Motani? Tingayambe kukaikila zakuti Mulungu akutsogolela gulu lathu. Izi n’zimene adani athu amafuna. Kodi tingacite ciyani maka-maka kuti tizindikile mabodza a adani athu na kuwakaniza?

MUSALOLE ANTHU ENA KUKUPANGITSANI KUKAIKILA GULU LATHU

13. Kodi adani a Mulungu ayesa motani kuipitsa gulu lake?

13 Adani a Mulungu amafuna kuti tiziona zinthu zimene gulu lathu limacita bwino kuti ni zolakwika. Mwa citsanzo, timaphunzila m’Malemba kuti Yehova amayembekezela alambili ake kukhala oyela kuthupi, m’makhalidwe, komanso kuuzimu. Iye amafuna kuti munthu aliyense wocita zoipa koma wosalapa acotsedwe mu mpingo. (1 Akor. 5:​11-13; 6:​9, 10) Timatsatila lamulo la m’Malemba limeneli. Koma cifukwa ca zimenezi, adani athu amanena kuti ndife anthu okhwimitsa zinthu, oweluza mopanda cilungamo, komanso opanda cikondi.

14. Kodi gwelo lenileni la mabodza okhudza gulu lathu ndani?

14 Zindikilani gwelo la mabodza amenewa. Satana Mdyelekezi ndiye amasonkhezela anthu kunena mabodza amenewa. Iye ni “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44; Gen. 3:​1-5) Conco n’zosadabwitsa kuti Satana amaseŵenzetsa anthu ake kufalitsa mabodza ponena za gulu la Yehova. Izi zinaonekela bwino m’zaka za zana loyamba.

15. N’ciyani cimene atsogoleli a cipembedzo anacita kwa Yesu na otsatila ake?

15 Ngakhale kuti Yesu Mwana wa Mulungu anali wangwilo, ndipo anali kucita zozizwitsa, adani a Mulungu anali kufalitsa mabodza ambili okhudza iye. Mwa citsanzo, atsogoleli a zipembedzo anali kuuza anthu kuti mphamvu zotulutsa ziŵanda zimene Yesu anali nazo anapatsidwa na “wolamulila ziŵanda.” (Maliko 3:22) Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu, atsogoleli a cipembedzo anamunamizila kuti ananyoza Mulungu. Iwo analimbikitsa khamu la anthu kugamula kuti Yesu aphedwe. (Mat. 27:20) Patapita nthawi, pamene otsatila a Khristu anali kulalikila uthenga wabwino, anthu otsutsa “anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo” kuti azunze Akhristuwo. (Mac. 14:​2, 19) Ponena za Machitidwe 14:​2, Nsanja ya Mlonda ya December 1, 1998, inafotokoza kuti: “Kuonjezela pa kukana uthengawo, Ayuda otsutsa anayamba kufalitsa mphekesela zoipa akumayesa kupangitsa anthu akunja kuti akhale ndi maganizo oipa ponena za Akhristu.”

16. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani tikamva nkhani zabodza?

16 Satana akupitilizabe kunena mabodza mpaka pano. Iye, “akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 12:9) Mukamva nkhani zabodza zokhudza gulu la Mulungu kapena abale amene akutsogolela, muzikumbukila mmene adani a Mulungu anacitila kwa Yesu na ophunzila ake a m’zaka za zana loyamba. Baibo inanenelatu kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa na kunamizilidwa. Ndipo n’zimene zikucitika masiku ano. (Mat. 5:​11, 12) Tikazindikila gwelo lenileni la mabodza na kucitapo kanthu mwamsanga, sitingasoceletsedwe. Kodi tiyenela kucitapo ciyani?

17. N’ciyani cingatithandize kupewa kusoceletsedwa na nkhani zabodza? (2 Timoteyo 1:13) (Onani bokosi lakuti “Mmene Tingapewele Nkhani Zabodza.”)

17 Kanizani nkhani zabodza. Mtumwi Paulo anapeleka malangizo omveka bwino a zimene tiyenela kucita tikamva nkhani zabodza. Iye anauza Timoteyo kuti: “Uletse anthu ena . . . kuti asamamvele nkhani zonama.” Anamuuzanso kuti: “Uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.” (1 Tim. 1:​3, 4; 4:7) Ganizilani izi, mwana wamng’ono angatole cinthu cadothi n’kuciika m’kamwa. Koma munthu wamkulu sangacite zimenezi cifukwa adziŵa kuti cingamudwalitse. Timakaniza nkhani zabodza cifukwa tidziŵa gwelo lake. Timagwilitsitsa “mawu olondola” a coonadi.—Ŵelengani 2 Timoteyo 1:13.

Cithunzi: njila zimene angafalitsile nkhani zabodza. 1. Mwamuna akujambula mawu. 2. Mkazi akunong’oneza. 3. Mauthenga apacipangizo opanda umboni. 4. Makalata. Mlongo akung’amba kalatayo.

Mmene Tingapewele Nkhani Zabodza

Nkhani zabodza zingacokela kwa abale na alongo amene mosadziŵa amafalitsa nkhani zopanda umboni. Angatitumizile nkhani zimenezi kupitila pa meseji. Zingacokelenso kwa anthu ampatuko amene tingakumane nawo mu ulaliki. Iwo angabise umunthu wawo mwa kuonetsa cidwi cofuna kuphunzila Baibo.

1. Nkhani zopanda umboni zocokela kwa abale na alongo:

M’funseni m’bale kapena mlongoyo kuti anatsimikiza bwanji kuti nkhaniyo inacokela ku magwelo odalilika. Ngati nkhaniyo ilibe umboni, inyalanyazeni ndipo musaifalitse.—Miy. 14:15.

2. Mauthenga abodza okamba za anthu a Yehova:

Nthawi zina tingalandile mauthenga pa cipangizo cathu ooneka ngati acokela kwa anthu amene timadziŵa. Zikatelo, m’funseni mnzanuyo ngati ndiye watumiza uthengawo, komanso ngati watsimikiza kuti wacokela ku magwelo odalilika. Ngati sindiye wautuma kapena ngati magwelo ake si odalilika, ufafanizeni.—Miy. 27:12.

3. Ampatuko amene amabisa umunthu wawo mwa kudzipanga kukhala na cidwi pa uthenga wathu:

Ngati mwaona kuti munthuyo wayamba kukamba zoipa za gulu lathu, kapena wayamba kukuuzani nkhani inayake yocokela kwa ampatuko, imitsani makambilanowo mwaulemu.—2 Yoh. 10.

18. Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila gulu la Yehova?

18 Tangokambilanako njila zitatu cabe pa njila zambili zimene gulu la Mulungu limatengela citsanzo ca Yesu. Pamene muŵelenga Baibo, pezani njila zowonjezela zimene gulu lathu limatengela citsanzo ca Yesu. Thandizani ena mu mpingo mwanu kukulitsa ciyamikilo cawo pa gulu lathu. Ndipo pitilizani kuonetsa ciyamikilo canu mwa kutumikila Yehova mokhulupilika na kumamatila gulu limene akuseŵenzetsa pokwanilitsa cifunilo cake. (Sal. 37:28) Tiyeni tisaleke kuyamikila mwayi wapadela umene tili nawo wogwilizana na anthu acikondi, komanso okhulupilika a Yehova.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi anthu a Mulungu amatengela citsanzo ca Yesu m’njila ziti?

  • Tingapitilize bwanji kuonetsa ciyamikilo cathu pa gulu la Yehova?

  • Tiyenela kutani tikamva nkhani zabodza?

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

a Onani bokosi lakuti “Why 1919?” mu buku la Cingelezi la Pure Worship of Jehovah—Restored At Last! masamba. 102-103.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Akulu atakambilana malangizo a ulaliki wapoyela, woyang’anila kagulu akuuza ofalitsa kuti ayenela kuimilila m’mbali mwa cipupa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani