LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 June masa. 20-25
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHAMVU
  • MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHOTO
  • KHALANIBE PAFUPI NA MULUNGU WAMOYO
  • Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Sitinakhalepo Tokha Ngakhale Pang’ono
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Mmene Tingathetsele Zikaiko Zathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 June masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 25

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”

“Yehova ndi wamoyo!”—SAL. 18:46.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Timapindula ngako tikamakumbukila kuti Mulungu amene timalambila ni “Mulungu wamoyo.”

1. N’ciyani cimathandiza anthu a Yehova kupitilizabe kumulambila ngakhale kuti amakumana na mavuto?

BAIBO imafotokoza kuti ino ni “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Kuwonjezela pa mavuto amene anthu onse amakumana nawo m’dongosolo lino la zinthu, anthu a Yehova amakumananso na citsutso komanso mazunzo. N’ciyani cimatithandiza kupitiliza kulambila Yehova ngakhale kuti timakumana na mavuto amenewa? Cinthu cacikulu cimene cimatithandiza n’cakuti timakhulupilila na mtima wathu wonse kuti Yehova ni “Mulungu wamoyo.”—Yer. 10:10; 2 Tim. 1:12.

2. Kodi Yehova ni Mulungu wamoyo m’lingalilo lotani?

2 Yehova alikodi ndipo amatisamalila tikakumana na mavuto. Iye amafuna-funa mipata yotithandizila. (2 Mbiri 16:9; Sal. 23:4) Kumuona kuti ni Mulungu wamoyo kudzatithandiza kupilila mavuto alionse amene tingakumane nawo. Tiyeni tione mmene kuona Yehova kuti ni Mulungu wamoyo kunathandizila Mfumu Davide kupilila mavuto.

3. Kodi Davide anatanthauzanji pomwe ananena kuti “Yehova ndi wamoyo?”

3 Davide anali kum’dziŵa bwino Yehova, ndipo anali kum’dalila. Pomwe Mfumu Sauli na anthu ena anali kufuna kupha Davide, iye anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. (Sal. 18:6) Mulungu atayankha pemphelo lake na kumupulumutsa, iye ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Ponena mawu amenewa, Davide sanali kungovomeleza kuti Mulungu aliko ayi. Pothilila ndemanga pa mawu amenewa, buku lina linanena kuti Davide anali kuonetsa cidalilo cake mwa Yehova “monga Mulungu wamoyo amene nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Inde, Davide anadzionela yekha pa zocitika za pa umoyo wake kuti Mulungu wake ni wamoyo, ndipo zimenezi zinam’sonkhezela kupitiliza kum’tumikila na kum’tamanda.—Sal. 18:​28, 29, 49.

4. Timapindula bwanji podziŵa kuti Yehova ni Mulungu wamoyo?

4 Kukhala otsimikiza kuti Yehova ni Mulungu wamoyo kumatithandiza kumutumikila na mtima wonse. Kumatithandizanso kupilila mavuto amene tingakumane nawo na kupitiliza kugwila nchito molimbika pom’tumikila. Cina, kumatithandiza kukhalabe naye pa ubwenzi.

MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHAMVU

5. N’ciyani cimatipatsa cidalilo tikakumana na mavuto? (Afilipi 4:13)

5 Tikamakumbukila kuti Yehova ni Mulungu wamoyo komanso kuti ni wokonzeka kutithandiza, tidzatha kupilila mayeso alionse amene tingakumane nawo, kaya akhale aakulu kapena aang’ono. Ni iko komwe, kulibe vuto limene angalephele kulithetsa. Iye ni Wamphamvuzonse, ndipo angatipatse mphamvu kuti tipilile. (Ŵelengani Afilipi 4:13.) Izi zimatithandiza kuyang’anizana na mavuto alionse mwacidalilo. Yehova akatithandiza pa mavuto aang’ono amene takumana nawo, timakhala na cidalilo cakuti adzatithandizanso tikadzakumana na mavuto aakulu.

6. Ni zocitika ziti pa unyamata wa Davide zimene zinalimbikitsa cidalilo cake mwa Yehova?

6 Ganizilani zocitika ziŵili izi pa umoyo wa Davide. Pamene iye anali m’busa wacinyamata, cimbalangondo cinagwila nkhosa ya atate ake. Pa nthawi inanso mkango unacita cimodzimodzi. Pa zocitika zonsezi, Davide molimba mtima anathamangitsa zilombozo na kupulumutsa nkhosazo. Koma iye sanaone kuti wacita zimenezi mwa mphamvu zake ayi. Anadziŵa kuti Yehova ndiye anam’patsa mphamvu. (1 Sam. 17:​34-37) Davide sanaiŵale zocitika zimenezo. Kusinkhasinkha zocitikazo kunam’patsa cidalilo cakuti Mulungu wamoyo adzam’patsanso mphamvu m’tsogolo.

7. Kodi kuona zinthu moyenela kunam’thandiza bwanji Davide?

7 Patapita nthawi Davide akali wacinyamata, mwina asanakwanitse zaka 20, anapita kumsasa wa asilikali a Isiraeli. Atafika, anapeza asilikali ali na mantha cifukwa ca ngwazi ya Cifilisiti dzina lake Goliyati amene anali ‘kunyoza asilikali a Isiraeli.’ (1 Sam. 17:​10, 11) Asilikaliwo anacita mantha cifukwa anali kuganizila kwambili za maonekedwe a Goliyati komanso mawu onyoza amene iye anali kukamba. (1 Sam. 17:​24, 25) Koma Davide anaona nkhaniyo m’njila ina. Anali kuona kuti Goliyati sanali kulimbana na asilikali wamba a Isiraeli, koma anali kulimbana na “Mulungu wamoyo.” (1 Sam. 17:26) Davide anali kuganizila za Yehova. Ndipo anali na cidalilo cakuti Mulungu amene anam’thandiza pamene anali m’busa, adzam’thandizanso pa cocitika cimeneci. Ali na cidalilo cimeneci, iye anapita kukamenyana na Goliyati, ndipo anapambana!—1 Sam. 17:​45-51.

8. N’ciyani cingalimbikitse cidalilo cathu mwa Yehova tikakumana na mavuto? (Onaninso cithunzi.)

8 Nafenso tingathe kupilila mayeso ngati timakumbukila kuti Mulungu wamoyo ni wokonzeka kutithandiza. (Sal. 118:6) Tingalimbikitse cidalilo cathu cakuti Yehova adzatithandiza mwa kusinkhasinkha zimene iye anacita kalelo. Muziŵelenga zocitika za m’Baibo zimene zingakukumbutseni mmene Yehova anapulumutsila alambili ake. (Yes. 37:​17, 33-37) Komanso, muziŵelenga na kuonelela malipoti a pa jw.org okamba za mmene Yehova akuthandizila abale na alongo athu masiku ano. Kuwonjezela apo, muzikumbukila nthawi pamene Yehova anakuthandizani. Mwina mumaona kuti Yehova sanakucitilemponi cinthu cacikulu pa umoyo wanu, monga kukupulumutsani ku mkango kapena ku cimbalangondo. Koma zoona zake n’zakuti Yehova wakucitilani zinthu zambili pa umoyo wanu. Anakukokelani kwa iye kuti mukhale naye pa ubwenzi. (Yoh. 6:44) Ngakhale panopa mukali m’coonadi cifukwa ca thandizo lake. Mungacite bwino kum’pempha kuti akuthandizeni kukumbukila nthawi pamene iye anayankha mapemphelo anu, kukuthandizani pamene munafunikila thandizo, kapena kukusamalilani m’nthawi zovuta. Kusinkhasinkha zocitika ngati zimenezi kudzalimbikitsa cidalilo canu cakuti Yehova sadzaleka kukuthandizani.

Abale aŵili ali m’ndende, ndipo akuceza atakhala pa bedi. Kumbuyo kwawo kuli ma khadi, makalata, komanso cithunzi cojambula.

Mmene timacitila tikakumana na mavuto zimakhudza mmene Yehova amamvela (Onani ndime 8-9)


9. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani tikakumana na mavuto? (Miyambo 27:11)

9 Kuona Yehova kuti ni Mulungu wamoyo kumatithandiza kuona mavuto athu moyenela. Motani? Timayamba kuona mavuto athu monga mbali ya nkhani yaikulu ya pakati pa Yehova na Satana. Mdyelekezi amanena kuti tikakumana na mavuto aakulu, tikhoza kusiya kulambila Yehova. (Yobu 1:​10, 11; ŵelengani Miyambo 27:11.) Koma tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova pa mavuto, timaonetsa kuti timamukonda komanso kuti Mdyelekezi ni wabodza. Kodi anthu salabadila uthenga wanu kapena mukuyang’anizana na citsutso ca boma, mavuto a zacuma, kapena mavuto ena? Ngati n’telo, kumbukilani kuti zocitikazo zikukupatsani mwayi wokondweletsa mtima wa Yehova. Muzikumbukilanso kuti iye sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungathe kupilila. (1 Akor. 10:13) Adzakupatsani mphamvu kuti mupilile.

MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHOTO

10. Kodi Mulungu wamoyo adzacita ciyani kwa amene amam’lambila?

10 Yehova nthawi zonse amapeleka mphoto kwa amene amam’lambila. (Aheb. 11:6) Pali pano amatithandiza kukhala na mtendele komanso kukhala acimwemwe, ndipo m’tsogolo adzatipatsa moyo wosatha. Tili na ciyembekezo cakuti adzatifupa cifukwa ali na cifuno komanso mphamvu zocitila zimenezi. Ndipo izi zimatisonkhezela kukangalika pa kulambila kwathu monga mmene atumiki okhulupilika a Mulungu a m’nthawi zakumbuyo anacitila. Izi n’zimene Timoteyo wa m’zaka za zana loyamba anacita.—Aheb. 6:​10-12.

11. N’ciyani cinasonkhezela Timoteyo kutumikila molimbika mumpingo? (1 Timoteyo 4:10)

11 Ŵelengani 1 Timoteyo 4:10. Timoteyo anaika ciyembekezo cake mwa Mulungu wamoyo. Conco anali na zifukwa zabwino zotumikilila Mulungu molimbika na kudzipeleka na mtima wonse. Anacita bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo anamulimbikitsa kuti anole maluso ake a kuphunzitsa mumpingo komanso mu ulaliki. Anam’limbikitsanso kuti akhale citsanzo cabwino kwa okhulupilila anzake, acinyamata na acikulile omwe. Anapatsidwanso nchito zina zovuta zomwe zinaphatikizapo kupeleka uphungu wamphamvu koma wacikondi kwa amene anali kuufunikila. (1 Tim. 4:​11-16; 2 Tim. 4:​1-5) Timoteyo sanakaikile kuti Yehova adzamupatsa mphoto cifukwa ca nchito imene anali kugwila, ngakhale kuti nthawi zina ena sanali kuona nchitoyo kapena kumuyamikila.—Aroma 2:​6, 7.

12. N’ciyani cimalimbikitsa akulu kugwila nchito yawo mwakhama? (Onaninso cithunzi.)

12 Nawonso akulu masiku ano ayenela kukhala otsimikiza kuti Yehova amaona na kuyamikila nchito zawo zabwino. Kuwonjezela pa kucita ubusa, kuphunzitsa, komanso kulalikila, akulu ena amathandizila pa nchito za mamangidwe komanso makomiti othandiza pakagwa tsoka. Akulu enanso amatumikila m’Magulu Oyendela Odwala kapena m’Makomiti Okambilana na Azacipatala. Akulu amene amadzipeleka pa nchito ngati zimenezi, amadziŵa kuti mpingo ni wa Yehova osati wa munthu. Conco, amacita mautumiki amenewa na mtima wawo wonse podziŵa kuti Mulungu sadzalephela kuwafupa pa zimene amacita.—Akol. 3:​23, 24.

Akulu aŵili akucita ulendo waubusa pa vidiyokomfalensi kwa mlongo usiku. Mmodzi wa abalewo akuŵelenga Baibo. Pa cipupa pakuonekela zovala zimene amaseŵenzetsa pa nchito ya mamangidwe a gulu, ndipo pakuonekanso kalenda yodzala na zocita zambili.

Mulungu wamoyo adzakufupani mukamam’tumikila molimbika pothandiza mpingo (Onani ndime 12-13)


13. Kodi Yehova amamva bwanji pa zimene timacita pom’tumikila?

13 Si onse angakhale akulu mumpingo. Komabe, tonsefe tili na cina cake cimene tingam’patse Yehova. Mulungu wathu amayamikila tikamacita zonse zimene tingathe pom’tumikila. Iye amaona zopeleka zathu pa nchito ya padziko lonse ngakhale zitakhala zocepa. Amakondwela tikamayetsetsa mwamphamvu kuti tigonjetse mantha athu na kuimika dzanja kuti tipelekepo ndemanga pa misonkhano. Amakondwelanso tikanyalanyaza zimene munthu watilakwila na kumukhululukila. Ngakhale kuti nthawi zina mungaone kuti zimene mumapatsa Yehova n’zocepa, musakaikile kuti iye amayamikila zimene mumam’patsazo. Amakukondani cifukwa ca zimenezo, ndipo adzakupatsani mphoto.—Luka 21:​1-4.

KHALANIBE PAFUPI NA MULUNGU WAMOYO

14. Kodi kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova, kumatithandiza bwanji kukhala okhulupilika kwa iye? (Onaninso cithunzi.)

14 Tikamaona kuti Yehova ni weniweni, cidzakhala capafupi kukhala okhulupilika kwa iye. Umu ni mmene zinalili na Yosefe. Iye anakana molimba mtima kucita ciwelewele cifukwa anali kuona kuti Mulungu ni weniweni, ndipo sanafune kucita zinthu zomukhumudwitsa. (Gen. 39:9) Kuti tiziona Yehova kukhala weniweni, tiyenela kumapatula nthawi yopemphela kwa iye na kuŵelenga Mawu ake. Tikatelo, ubwenzi wathu na iye udzalimba. Ngati nafenso tili pa ubwenzi wolimba na Yehova monga mmene zinalili kwa Yosefe, tidzapewa kucita ciliconse cimene cingamukhumudwitse.—Yak. 4:8.

M’bale wacinyamata akucoka pali anzake a m’kalasi pomwe iwo ayamba kuona zinazake pa foni.

Kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu wamoyo kudzakuthandizani kukhalabe wokhulupilika kwa Iye (Onani ndime 14-15)


15. Ni cenjezo lotani limene tingatengepo pa nkhani ya Aisiraeli m’cipululu? (Aheberi 3:12)

15 Munthu akaiŵala kuti Yehova ni Mulungu wamoyo, cimakhala cosavuta kuti akhale osakhulupilika kwa iye. Ganizilani zimene zinacitikila Aisiraeli pomwe anali m’cipululu. Iwo anali kudziŵa kuti Yehova aliko, koma anakaikila zakuti angawasamalile pa zosoŵa zawo. Iwo anafika pofunsa kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?” (Eks. 17:​2, 7) Zotsatilapo zake zinali zakuti anapandukila Mulungu. Tiyenela kupewelatu kutsatila citsanzo cawo coipa ca kusamvela.—Ŵelengani Aheberi 3:12.

16. N’ciyani cingaike cikhulupililo cathu pamayeso?

16 Dziko limapangitsa kuti cikhale covuta kwa ife kuyandikila Yehova. Pali anthu ambili amene amakana zakuti kuli Mulungu. Ndipo nthawi zina anthu amene amakana mfundoyi zinthu zimaoneka kuti zikuwayendela bwino pa umoyo. Tikaona zimenezi, cikhulupililo cathu cingayesedwe. N’zoona kuti sitingayambe kukayikila zakuti kuli Mulungu, koma tingayambe kukaikila zakuti iye angatithandize. Izi zinacitikapo kwa amene analemba Salimo 73. Iye anaona kuti anthu amene anali kuphwanya malamulo a Mulungu anali kusangalala na umoyo. Cifukwa ca zimenezi, iye anayamba kukaikila ngati kutumikila Mulungu kunalidi kwaphindu.—Sal. 73:​11-13.

17. N’ciyani cidzatithandiza kukhalabe pa ubwenzi na Yehova?

17 N’ciyani cinathandiza wolemba Salimo ameneyu kusintha kaganizidwe kake? Anasinkhasinkha zimene zidzacitikila onse amene amaleka kukhulupilila Yehova. (Sal. 73:​18, 19, 27) Anaganizilanso za mapindu amene munthu amapeza akamatumikila Mulungu. (Sal. 73:24). Nafenso tingacite bwino kumasinkhasinkha za madalitso amene Yehova watipatsa. Kenako n’kuyelekezela mmene umoyo wathu ulili na mmene ukanakhalila tikanakhala kuti sitikutumikila Yehova. Kucita zimenezi, kudzatithandiza kuti tikhalebe okhulupilika. Ndipo na mtima wonse tidzakamba monga mmene wamasalimo anakambila kuti, “Koma kwa ine kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.”—Sal. 73:28.

18. N’cifukwa ciyani sitiyenela kuopa zimene zidzacitika m’tsogolo?

18 Tingakhalebe olimba mtima pokumana na mavuto alionse amene angabwele masiku ano otsiliza cifukwa ‘timatumikila Mulungu wamoyo ndi woona.’(1 Ates. 1:9) Mulungu wathu ni weniweni ndipo amasamala za ife. Iye nthawi zonse amatithandiza. Anathandizapo atumiki ake a m’nthawi za kumbuyo, ndipo adzacitanso cimodzimodzi kwa ife masiku ano. Posacedwapa, tidzayang’anizana na cisautso cacikulu cimene sicinacikepo n’kale lonse. Koma sitidzakhala tokha, Yehova adzakhala nafe. (Yes. 41:10) Pemphelo lathu n’lakuti tonsefe “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.’”—Aheb. 13:​5, 6.

KODI KUKUMBUKILA KUTI YEHOVA NI “MULUNGU WAMOYO” KUDZAKUTHANDIZANI MOTANI . . .

  • kupeza mphamvu?

  • kutsimikiza kuti adzakupatsani mphoto?

  • kukhalabe naye pa ubwenzi?

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani