LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 September tsa. 32
  • Muziphunzila Mfundo Zatsopano Mukamaŵelenga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziphunzila Mfundo Zatsopano Mukamaŵelenga
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amasamalila Anthu Ake
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Khalani na Cizoloŵezi Cabwino Coŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Pindulani Mokwanila ndi Cakudya Cakuuzimu Cimene Yehova Amapeleka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Nzelu Yeniyeni Imafuula
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 September tsa. 32

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Muziphunzila Mfundo Zatsopano Mukamaŵelenga

Tikafuna kuyamba kuŵelenga, tingadzifunse kuti, ‘Kodi nidzaphunzila ciyani?’ Tingakhale na mfundo inayake imene tikuyembekezela kupeza m’nkhani imene tikuŵelenga. Koma tizikumbukila kuti pali mfundo zina zatsopano zimene Yehova angafune kutiphunzitsa m’nkhaniyo. Tingadziŵe bwanji zimene Yehova afuna kutiphunzitsa?

Muzipempha nzelu. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa zimene akufuna kuti muphunzile panthawiyo. (Yak. 1:5) Musakhale okhutila na mfundo zimene mudziŵa kale.​—Miy. 3:5, 6.

Lolani mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito pa moyo wanu. “Mawu a Mulungu ndi amoyo.” (Aheb. 4:12) Conco, nthawi zonse tikamaŵelenga Baibo, imatiphunzitsa mfundo zatsopano komanso kutithandiza m’njila zosiyana-siyana. Koma izi zingatheke kokha ngati timavomeleza kuti pali mfundo inayake imene Mulungu afuna kutiphunzitsa.

Muziyamikila zonse zimene Yehova amatiphunzitsa. Cakudya cauzimu cimene Yehova amatipatsa cili monga “phwando la zakudya zabwino kwambili.” (Yes. 25:6) Musapewe “zakudya,” kapena kuti nkhani, zimene muona kuti simudzasangalala nazo. Mukatelo mudzapindula kwambili, ndipo mudzapeza cimwemwe pamene mukuŵelenga!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani