LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 March masa. 2-7
  • Musacedwe Kubatizika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Musacedwe Kubatizika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ASAMARIYA ANABATIZIKA
  • SAULO WA KU TARISO ANABATIZIKA
  • KONELIYO ANABATIZIKA
  • AKORINTO ANABATIZIKA
  • CIKHULUPILILO CANU CINGASUNTHE MAPILI
  • Pitilizani Kutsatila Yesu Pambuyo pa Ubatizo Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kudzipatulila kwa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kubatizika?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya
    2025-2026 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woyang’anila Dela
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 March masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 9

NYIMBO 51 Tinadzipeleka kwa Mulungu

Musacedwe Kubatizika

“Ukucedwelanji? Nyamuka ubatizidwe.”​—MAC. 22:16.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Pezani mphamvu zokuthandizani kuti mubatizike mwa kuganizila citsanzo ca Asamariya, Saulo wa ku Tariso, Koneliyo, komanso Akorinto.

1. Kodi zina mwa zifukwa zabwino zimene ziyenela kupangitsa munthu kubatizika n’ziti?

KODI mumam’konda Yehova Mulungu amene anakupatsani mphatso iliyonse yabwino, kuphatikizapo moyo umene muli nawo? Kodi mumafuna kumuonetsa kuti mumam’konda? Njila yabwino kopambana imene mungacitile zimenezo ndi kudzipatulila kwa iye, ndi kuonetsa kudzipatulilako mwa kubatizika m’madzi. Masitepe amenewa amakuyenelezani kukhala m’banja la Yehova. Zotsatilapo zake zidzakhala zakuti Atate wanu komanso Bwenzi lanu, Yehova, adzakutsogolelani ndi kukusamalilani cifukwa mudzakhala wake. (Sal. 73:24; Yes. 43:​1, 2) Kuwonjezela apo, kudzipatulila ndi kubatizika kudzakupatsani ciyembekezo cokakhala ndi moyo wosatha.​—1 Pet. 3:21.

2. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Kodi pali cimene cikukulepheletsani kubatizika? Ngati n’telo, dziwani kuti si inu nokha amene muli mu mkhalidwe wa conco. Pali anthu mamiliyoni amene anayenela kusintha makhalidwe awo ndi kaganizidwe kawo kuti ayenelele ubatizo. Tsopano, iwo akutumikila Yehova mwacimwemwe komanso mokangalika. Kodi mungaphunzile ciyani kwa ena mwa anthu amene anabatizika m’nthawi ya atumwi? Tiyeni tione zopinga zimene anakumana nazo, komanso zimene tingaphunzilepo pa zitsanzo zawo.

ASAMARIYA ANABATIZIKA

3. Ndi zopinga ziti zimene ena mwa Asamariya anagonjetsa kuti abatizike?

3 Asamariya anali m’kagulu ka cipembedzo m’nthawi ya Yesu komwe kanali kupezeka kumadela a Sekemu ndi Samariya, kumpoto kwa Yudeya. Asamariya asanabatizike, anafunika kukhala ndi cidziwitso colondola ca Mawu a Mulungu mozamilapo. Iwo anali kukhulupilila kuti mabuku asanu oyambilila okha, kuyambila pa Genesis kufika pa Deuteronomo, mwinanso ndi buku la Yoswa, ndi okhawo amene anali ouzilidwa ndi Mulungu. Komabe, iwonso anali kuyembekezela kubwela kwa Mesiya mogwilizana ndi lonjezo la Mulungu la pa Deuteronomo 18:​18, 19. (Yoh. 4:25) Kuti abatizike, iwo anafunikila kuvomeleza kuti Yesu ndiye anali Mesiya wolonjezedwayo. Ndipo “Asamariya ambili” anatelodi. (Yoh. 4:39) Ena mwa iwo anagonjetsa tsankho lalikulu limene linalipo pakati pa Asamariya ndi Ayuda.​—Luka 9:​52-54.

4. Malinga ndi Machitidwe 8:​5, 6, 14, kodi Asamariya ena anaulandila motani ulaliki wa Filipo?

4 N’ciyani cinathandiza Asamariya kubatizika? Mlaliki Filipo ‘atalalikila za Khristu kwa’ Asamariya, ena a iwo ‘analandila mawu a Mulungu.’ (Welengani Machitidwe 8:​5, 6, 14.) Ngakhale kuti Filipo anali Myuda, iwo sanakane kumvetsela uthenga wake. Mwina iwo anakumbukila limodzi mwa Malemba amene anali kuwakhulupilila onena kuti Mulungu alibe tsankho. (Deut. 10:​17-19) Mulimonsemo, iwo “ankamvetsela zimene Filipo ankanena” zokhudza Khristu, ndipo anaona umboni wosatsutsika wakuti Mulungu anali naye. Iye anali kucitanso zizindikilo zambili, monga kucilitsa odwala, komanso kutulutsa ziwanda.​—Mac. 8:7.

5. Kodi mungaphunzileko ciyani kwa Asamariya?

5 Asamariya amenewo akanafuna, akanakana kumvetsela kwa Filipo cifukwa cakuti iye anali Myuda, komanso cifukwa cakuti ziphunzitso zimene anali kuwaphunzitsa zinali zacilendo kwa iwo. Koma sanatelo. Asamariyawo sanazengeleze kubatizika atatsimikiza kuti Filipo anali kuwaphunzitsa coonadi. Baibulo limafotokoza kuti: “Iwo atakhulupilila Filipo, amene ankalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso wonena za dzina la Yesu Khristu, ankabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.” (Mac. 8:12) Kodi inuyo mumakhulupilila ndi mtima wonse kuti Mawu a Mulungu ndi coonadi? Komanso kodi mumakhulupilila kuti Mboni za Yehova zilibe tsankho, komanso kuti zimaonetsana cikondi ceniceni, comwe ndi cizindikilo ca Akhristu oona? (Yoh. 13:35) Ngati n’telo, citam’poni kanthu mwa kubatizika muli ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzakudalitsani.

6. Kodi mungapindule bwanji ndi zimene zinacitikila Ruben?

6 Ruben wa ku Germany, anakulila m’banja la Mboni. Komabe, ali wacinyamata iye anali kukaikila zakuti Yehova aliko. N’ciyani cinamuthandiza kuthetsa cikaiko cimeneco? Atazindikila kuti sanali kudziwa zambili zokhudza nkhaniyo, anapanga ciganizo cakuti awonjezele cidziwitso cake. Iye anati: “Pa phunzilo langa la munthu mwini, ndinaganiza kuti ndifufuze pofuna kudziwa zoona komanso zabodza zokhudza nkhaniyo. Mobwelezabweleza ndinawelenga nkhani ya cisanduliko.” Iye anawelenga buku la Cingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Zimene anawelenga m’buku limeneli zinamukhudza kwambili. Mumtima anati: ‘Ooo! Yehova ndi weniweni.’ Ndipo Ruben atapita kukaona malo ku likulu lathu la padziko lonse, anakulitsa ciyamikilo cake pa ubale wa padziko lonse umene tili nawo. Ruben atabwelela ku Germany, anabatizika ali ndi zaka 17. Ngati muli ndi zikaiko pa zina zimene munaphunzila, thetsani zikaiko zanu mwa kufufuza m’zofalitsa zathu. Kukhala ndi cidziwitso colondola kudzakuthandizani kuthetsa zikaiko zanu. (Aef. 4:​13, 14) Kuwonjezela apo, mukamamva malipoti onena za cikondi komanso mgwilizano wa anthu a Yehova, ocokela m’mbali zina za dziko lapansi, komanso kudzionela nokha umboni umenewo mu mpingo mwanu, ciyamikilo canu pa ubale wathu wa padziko lonse cidzakulilako.

SAULO WA KU TARISO ANABATIZIKA

7. Kodi Saulo anafunika kusintha kaganizidwe kotani?

7 Ganizilani zimene zinacitikila Saulo wa ku Tariso. Iye anali kupita patsogolo bwino lomwe m’maphunzilo Aciyuda, ndiponso anali kucita bwino kwambili m’cipembedzo ca Ciyuda. (Agal. 1:​13, 14; Afil. 3:5) Saulo anali kuzunza Akhristu mwankhanza pa nthawi imene Ayuda anali kuona Akhristuwo ngati anthu ampatuko. Iye molakwa anali kuganiza kuti anali kucita cifunilo ca Mulungu pozunza Akhristuwo. (Mac. 8:3; 9:​1, 2; 26:​9-11) Kuti Saulo avomeleze Yesu ndi kukhala Mkhristu, anafunika kukhala wokonzeka kuzunzidwa.

8. (a) N’ciyani cinathandiza Saulo kubatizika? (b) Malinga ndi Machitidwe 22:​12-16, kodi Hananiya anamuthandiza motani Saulo? (Onaninso cithunzi.)

8 N’ciyani cinathandiza Saulo kubatizika? Yesu waulemeleloyo ataonekela kwa Saulo, Saulo anacita khungu. (Mac. 9:​3-9) Kwa masiku atatu, iye anasala kudya, ndipo mosakaikila anali kusinkhasinkha zimene zinali zitangomucitikila. Saulo anatsimikiza kuti Yesu ndiye anali Mesiya, komanso kuti otsatila ake ndiwo anali m’cipembedzo coona. Iye ayenela kuti anamva cisoni cifukwa covomeleza kuti Sitefano aphedwe! (Mac. 22:20) Masiku atatuwo atatha, wophunzila wina dzina lake Hananiya anayendela Saulo, ndipo anamucilitsa khungu lake ndi kumulimbikitsa kuti asacedwe kubatizika. (Welengani Machitidwe 22:​12-16.) Saulo modzicepetsa analandila thandizo la Hananiya ndipo anabatizika.​—Mac. 9:​17, 18.

Saulo akulowa m’madzi kuti abatizike. Anthu angapo akuonelela mwacisangalalo.

Kodi mudzalola kulandila thandizo kuti mubatizike monga anacitila Saulo? (Onani ndime 8)


9. Kodi mungaphunzileko ciyani kwa Saulo?

9 Pali zimene tingaphunzileko kwa Saulo. Akanafuna, akanalola kunyada kapena mantha oopa anthu kumulepheletsa kubatizika. Koma sanatelo. Modzicepetsa, anapanga masinthidwe pa umoyo wake atalandila coonadi conena za Khristu. (Mac. 26:​14, 19) Saulo anali wokonzeka kukhala Mkhristu ngakhale kuti anali kudziwa kuti adzazunzidwa. (Mac. 9:​15, 16; 20:​22, 23) Pambuyo pobatizika, iye anapitiliza kudalila Yehova kuti amuthandize kupilila mayeso osiyanasiyana. (2 Akor. 4:​7-10) Mukabatizika ndi kukhala wa Mboni za Yehova, mungakumane ndi mavuto kapena zinthu zina zoyesa cikhulupililo canu. Koma dziwani kuti thandizo lilipo. Mulungu ndi Khristu adzakupatsani thandizo lofunikila kuti mukhale wokhulupilika.​—Afil. 4:13.

10. Mungapindule bwanji ndi zimene zinacitikila Anna?

10 Anna anakulila ku Eastern Europe, m’banja la anthu olankhula cinenelo ca ci Kurdish. Amayi ake atabatizika, Anna anayamba kuphunzila Baibulo ali ndi zaka 9 atate ake atamulola. Koma acibale ake omwe anali kukhala nawo panyumba atadziwa kuti Anna wayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova, anayamba kumutsutsa. Acibalewo anali kuciona kuti ndi cinthu cocititsa manyazi munthu kusiya cipembedzo ca makolo. Anna atafika zaka 12, anapempha atate ake cilolezo cokabatizika. Atate ake anafuna kudziwa ngati Anna anali kupanga cisankho cimeneco pa iye yekha kapena ngati wina anali kumukakamiza kucita zimenezo. Iye anawayankha kuti, “Ndimamukonda Yehova.” Atate ake anamuvomeleza kuti akabatizike. Atabatizika, acibale ake anapitiliza kumunyoza komanso kumuzunza. Mmodzi wa acibale ake anamuuza kuti: “Nkhasako ukanakhalako hule kapena wosuta m’malo mokhala wa Mboni za Yehova.” N’ciyani cinathandiza Anna kupilila? Iye anati, “Yehova anandithandiza kukhala wolimba, ndipo amayi ndi atate anandithandiza kwambili.” Anna amalemba zocitika pamene waona thandizo la Yehova pa umoyo wake. Nthawi ndi nthawi amayang’anapo pa zimene amalembazo kuti asaiwale pamene Yehova anamuthandiza. Ngati mumaopa kutsutsidwa, muzikumbukila kuti inunso Yehova adzakuthandizani.​—Aheb. 13:6.

KONELIYO ANABATIZIKA

11. N’ciyani cikanalepheletsa Koneliyo kubatizika?

11 Baibulo limafotokozanso za munthu wina dzina lake Koneliyo. Iye anali “mtsogoleli” wa asilikali 100 a gulu la asilikali aciroma. (Mac. 10:​1, mawu a m’munsi.) Cifukwa ca zimenezi, n’kutheka kuti iye anali wolemekezeka kwa anthu komanso kwa asilikali. Iye “ankapatsa anthu mphatso zacifundo zambili.” (Mac. 10:2) Yehova anatuma mtumwi Petulo kuti akamulalikile uthenga wabwino. Kodi udindo wa Koneliyo unamulepheletsa kubatizika?

12. N’ciyani cinathandiza Koneliyo kubatizika?

12 N’ciyani cinathandiza Koneliyo kubatizika? Baibulo limatiuza kuti iye “ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse.” Ndipo Koneliyo anali kupemphela mocondelela kwa Mulungu nthawi zonse. (Mac. 10:2) Koneliyo atalalikidwa uthenga wabwino ndi Petulo, iye ndi a m’banja lake anakhulupilila Khristu ndipo anabatizika nthawi yomweyo. (Mac. 10:​47, 48) Koneliyo anali wokonzeka kupanga masinthidwe alionse ofunikila kuti ayambe kulambila Yehova limodzi ndi banja lake.​—Yos. 24:15; Mac. 10:​24, 33.

13. Kodi mungaphunzileko ciyani kwa Koneliyo?

13 Monga zinalili ndi Saulo, udindo wa Koneliyo ukanamulepheletsa kukhala Mkhristu. Koma sanalole zimenezo. Kodi mufunikila kusintha zinazake pa umoyo wanu kuti mubatizike? Ngati n’telo, Yehova adzakhala Mthandizi wanu. Mukamayesetsa kumutumikila motsatila mfundo za m’Baibulo, iye adzakudalitsani.

14. Mungapindule bwanji ndi zimene zinacitikila Tsuyoshi?

14 Tsuyoshi wa ku Japan anafunika kupanga masinthidwe pa nkhani ya nchito kuti ayenelele kubatizika. Iye anali waciwili kwa mphunzitsi wamkulu wa pa sukulu ya Ikenobo imene imaphunzitsa anthu moikila maluwa mwadongosolo. Mphunzitsi wamkulu akalephela kupita ku malilo, Tsuyoshi ndiye anali kupita kukamuimilako pocita miyambo ya Cibuda. Tsuyoshi ataphunzila coonadi ponena za imfa, anazindikila kuti sangayenelele kubatizika ngati angapitilize kucitako miyambo imeneyi. Conco anasankha kuleka kutengamo mbali. (2 Akor. 6:​15, 16) Tsuyoshi anakambilana nkhaniyi ndi mphunzitsi wamkulu. Zotsatilapo zake zinali zakuti Tsuyoshi anapitiliza kugwila nchito yake popanda kutengamo mbali m’miyambo ya Cibuda. Iye anabatizika patapita pafupifupi caka atayamba kuphunzila Baibulo.a Ngati mukufunikila kupanga masinthidwe pa nkhani ya nchito kuti mukondweletse Mulungu, dziwani kuti iye adzakusamalilani pa zimene inu ndi banja lanu mukufunikila.​—Sal. 127:2; Mat. 6:33.

AKORINTO ANABATIZIKA

15. Ndi zinthu ziti zikanalepheletsa Akorinto kubatizika?

15 Anthu a mumzinda wamakedzana wa Korinto anali kudziwika kuti anali kukonda kwambili zinthu zakuthupi, komanso kuti anali ndi makhalidwe oipa. Ambili anali kukhala umoyo wosakondweletsa Mulungu. N’zoonekelatu kuti kaamba ka zimenezi, zikanakhala zovuta kwambili kwa anthu amene anali kukhala mumzinda umenewu kuti ayambe kutumikila Yehova. Ngakhale n’telo, Paulo atafika mumzindawu ndi kulalikila uthenga wabwino wonena za Khristu, “anthu ambili a ku Korinto, amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupilila nʼkubatizidwa.” (Mac. 18:​7-11) Kenako Ambuye Yesu Khristu anaonekela kwa Paulo m’masomphenya ndi kumuuza kuti: “Ndili ndi anthu ambili mumzindawu.” Conco Paulo anapitiliza kulalikila mumzindawo kwa caka cimodzi ndi hafu.

16. N’ciyani cinathandiza Akorinto kugonjetsa zopinga zimene zikanawalepheletsa kubatizika? (2 Akorinto 10:​4, 5)

16 N’ciyani cinathandiza Akorinto kubatizika? (Welengani 2 Akorinto 10:​4, 5.) Mawu a Mulungu komanso mzimu woyela wamphamvu unawathandiza kupanga masinthidwe aakulu pa umoyo wawo. (Aheb. 4:12) Anthu a mumzinda wa Korinto amene analandila uthenga wabwino wonena za Khristu, anakwanitsa kusiya makhalidwe awo oipa, monga ucidakwa, umbava, komanso mathanyula.​—1 Akor. 6:​9-11.b

17. Kodi mungaphunzileko ciyani kwa Akorinto?

17 Onani kuti ngakhale kuti ena ku Korinto anali ndi makhalidwe oipa amene anali atazika mizu mwa iwo, sanaganize kuti sangakwanitse kusiya makhalidwewo n’kukhala Akhristu. Iwo anacita khama kwambili kuti alowe pa msewu wopanikiza wotsogolela ku moyo wosatha. (Mat. 7:​13, 14) Kodi muli ndi cizolowezi cimene cikukuvutani kuleka kuti muyenelele ubatizo? Ngati n’telo, musalefuke! M’pempheni Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyela kuti ukuthandizeni kukaniza cilakolako cofuna kucita zoipa.

18. Mungapindule bwanji ndi zimene zinacitikila Monika?

18 Monika wa ku dziko la Georgia anacita kulimbikila kwambili kuti asiye malankhulidwe oipa, komanso zosangalatsa zoipa kuti ayenelele kubatizika. Iye anati: “Pa citsikana canga, pemphelo linandithandiza kwambili. Yehova anali kudziwa kuti ndinali kufuna kucita zoyenela. Conco nthawi zonse anali kundithandiza komanso kunditsogolela.” Monika anabatizika ali ndi zaka 16. Nanga inu bwanji? Kodi pali zizolowezi zimene mufunikila kuleka kuti mutumikile Yehova movomelezeka? Ngati n’telo, pitilizani kumupempha kuti akupatseni mphamvu yokuthandizani kupanga masinthidwe. Yehova amapeleka mzimu wake woyela mowolowa manja.​—Yoh. 3:34.

CIKHULUPILILO CANU CINGASUNTHE MAPILI

19. N’ciyani cingakuthandizeni kugonjetsa zopinga zokhala ngati mapili? (Onaninso cithunzi.)

19 Conde, musamakaikile zakuti Yehova amakukondani komanso zakuti amafuna kuti mukhale m’banja lake. Muzikumbukila mfundoyi mosasamala kanthu za zopinga zimene mukukumana nazo zimene zikukulepheletsani kubatizika. Yesu anauza gulu la ophunzila ake kuti: “Ngati mutakhala ndi cikhulupililo cofanana ndi kanjele ka mpilu kucepa kwake, mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘Coka pano upite apo,’ ndipo lidzacokadi. Palibe cimene cidzakhale cosatheka kwa inu.” (Mat. 17:20) Amene anali kumvetsela mawuwa anali atakhala ndi Yesu zaka zocepa cabe. Conco cikhulupililo cawo cinali cikali kukula. Motelo, Yesu anawatsimikizila kuti akakhala ndi cikhulupililo cokwanila, Yehova adzawathandiza kugonjetsa zopinga zokhala ngati mapili. Yehova adzakuthandizani mmene anacitila kwa iwo!

Gulu losangalala la abale ndi alongo lili pa msonkhano, ndipo likuwomba m’manja pamene awo angobatizika kumene akudutsa.

Musakaikile kuti Yehova amakukondani, ndipo amafuna kuti mukhale m’banja lake (Onani ndime 19)c


20. Kodi zitsanzo za m’nkhani ino za Akhristu a m’nthawi ya atumwi komanso amakono, zakulimbikitsani motani?

20 Mukazindikila kuti muli ndi zopinga zimene zingakulepheletseni kubatizika, citam’poni kanthu mwamsanga kuti muzigonjetse. Lolani kuti zitsanzo za m’nthawi ya atumwi komanso zamakono, zikulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu. Pemphelo lathu n’lakuti zitsanzo zawo zikulimbikitseni ndi kukusonkhezelani kudzipatulila kwa Yehova ndi kubatizika. Cimeneci ndico cisankho cabwino koposa cimene mungapange!

MWAPHUNZILANJI KWA AKHRISTU OTSATILAWA A M’NTHAWI YA ATUMWI ZA MMENE MUNGAGONJETSELE ZOPINGA KUTI MUKABATIZIKE?

  • Asamariya

  • Saulo wa ku Tariso ndi Koneliyo

  • Akorinto

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

a Mbili ya M’bale Tsuyoshi Fujii, ili mu Galamukani! ya August 8, 2005, pa mas. 28-31.

b Onani vidiyo pa jw.org yakuti ‘N’cifukwa ciani mucedwa kubatizika?’

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Kagulu ka abale ndi alongo kakulandila amene angobatizika kumene mwansangala.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani