NKHANI YOPHUNZILA 10
NYIMBO 31 Uziyenda na Mulungu
Tengelani Kaganizidwe ka Yehova ndi Yesu
“Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu, nanunso konzekelani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo.”—1 PET. 4:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zimene mtumwi Petulo anacita kuti atengele kaganizidwe ka Khristu komanso zimene tingaphunzilepo.
1-2. Kodi Yesu anati kukonda Yehova kumaphatikizapo ciyani? Nanga anaonetsa bwanji kuti anali kukonda Atate wake ndi maganizo ake onse?
“MUZIKONDA Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.” (Luka 10:27) Yesu ponena mawuwa, anali kufuna kuonetsa kuti limeneli ndilo linali lamulo lofunika koposa m’Cilamulo ca Mose. Conco tiyenela kukonda Yehova ndi zonse tili nazo komanso umunthu wathu wonse. Izi ziphatikizapo zokhumba zathu, mmene tikumvela, mphamvu zathu, komanso mmene timaganizila. Koma monga tidziwila, n’zosatheka kumvetsa kaganizidwe konse ka Yehova. Komabe tingapitilize kukamvetsa bwino kaganizidwe ka Mulungu pophunzila “maganizo a Khristu,” cifukwa Yesu anatengela ndendende kaganizidwe ka Atate wake.—1 Akor. 2:16.
2 Yesu anali kukonda Yehova ndi maganizo ake onse. Iye anali kudziwa zimene Mulungu anali kufuna kuti acite, ndipo anali wofunitsitsa kucita zinthu mogwilizana ndi cifuniloco. Ngakhale n’conco, kucita zimenezo kukanacititsa kuti avutike cifukwa cocita zinthu zoyenela. Popeza Yesu anaika maganizo ake onse pa kucita cifunilo ca Atate wake, sanalole cina ciliconse kumulepheletsa kucita cifunilo ca Atate wake.
3. Kodi mtumwi Petulo anaphunzila ciyani kwa Yesu? Nanga analimbikitsa Akhristu anzake kucita ciyani? (1 Petulo 4:1)
3 Petulo limodzi ndi atumwi anzake anali ndi mwayi wapadela wokhalako ndi Yesu ndi kuona mmene anali kuganizila. M’kalata yoyamba youzilidwa imene Petulo analemba, anauza Akhristu kuti akonzekele mwa kukhala ndi maganizo a Khristu. (Welengani 1 Petulo 4:1.) Mawu amene Petulo anagwilitsa nchito akuti “konzekelani,” m’cilankhulo coyambilila anali kugwilitsidwa nchito pofotokoza za asilikali amene anali kukonzekela nkhondo mwa kukhala ndi zida. Conco, Akhristu akatengela kaganizidwe ka Yesu, ndiye kuti ali ndi cida camphamvu cowathandiza kulimbana ndi zilakolako za ucimo, komanso dziko lolamulidwa ndi Satana.—2 Akor. 10:3-5; Aef. 6:12.
4. Kodi nkhani ino idzatithandiza bwanji kutsatila uphungu wa Petulo?
4 Tidzasanthula kaganizidwe ka Yesu ndi kuona mmene tingakatengele. Tidzaphunzila (1) mmene tingatengele kaganizidwe ka Yehova, potithandiza kuganiza mogwilizana, (2) mmene tingakhalile odzicepetsa, ndi (3) mmene tingakhalile oganiza bwino podalila Yehova m’pemphelo.
TENGELANI KAGANIZIDWE KA YEHOVA
5. Kodi Petulo analephela bwanji kuonetsa kaganizidwe ka Yehova pa nthawi ina?
5 Ganizilani cocitika ici pamene Petulo analephela kuonetsa kaganizidwe ka Yehova. Yesu anali atauza ophunzila ake kuti iye ayenela kupita ku Yerusalemu kukapelekedwa m’manja mwa atsogoleli acipembedzo, kukazunzidwa, ndi kukaphedwa. (Mat. 16:21) Petulo anali kudziwa kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa komanso mpulumutsi wa Isiraeli. Conco, mwina zinali zovuta kwa iye kukhulupilila kuti Yehova angalole Yesu kuphedwa. (Mat. 16:16) Cotelo Petulo anatengela Yesu pambali n’kumuuza kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.” (Mat. 16:22) Popeza Petulo sanaonetse kaganizidwe ka Yehova pa nkhaniyi, maganizo ake sanali ogwilizana ndi a Yesu.
6. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuganiza ngati Yehova?
6 Kaganizidwe ka Yesu kanali kogwilizana kwambili ndi ka Atate wake wakumwamba. Yesu anauza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine cifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mat. 16:23) Petulo ayenela kuti anali ndi colinga cabwino pokamba mawuwo, koma Yesu anakana malangizo ake. Apa tiphunzilapo kuti sicinali colinga ca Yehova kuti Yesu akhale umoyo wopanda mavuto. Pa cocitikaci, Petulo anaphunzila mfundo yofunika kwambili yakuti ayenela kutengela kaganizidwe ka Mulungu.
7. N’ciyani cionetsa kuti patapita nthawi Petulo anali wokonzeka kusintha kaganizidwe kake kuti kagwilizane ndi ka Yehova? (Onani pacikuto.)
7 Patapita nthawi, Petulo anaonetsa kuti akufuna kutengela kaganizidwe ka Yehova. Nthawi inali itafika yakuti anthu amitundu ina osadulidwa alowe m’gulu la anthu a Mulungu. Petulo anatumidwa kuti akalalikile Koneliyo yemwe sanali Myuda. Munthu ameneyu ndiye anali woyamba kukhala Mkhristu pakati pa anthu osakhala Ayuda. Ayudawo sanali kugwilizana kwenikweni ndi anthu amitundu ina. Conco, Petulo anafunika kusintha kaganizidwe kake kuti akalalikile anthuwo. Petulo atazindikila cifunilo ca Mulungu pa nkhaniyi, anasintha kaganizidwe kake. Zotsatilapo zake zinali zakuti iye anapita “mosanyinyilika” ataitanidwa. (Mac. 10:28, 29) Analalikila Koneliyo ndi a m’banja lake, ndipo iwo anabatizika.—Mac. 10:21-23, 34, 35, 44-48.
Petulo akulowa m’nyumba ya Koneliyo (Onani ndime 7)
8. Kodi tingaonetse bwanji kuti kaganizidwe kathu n’kogwilizana ndi ka Yehova? (1 Petulo 3:8)
8 Patapita zaka, Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale “amaganizo amodzi.” (Welengani 1 Petulo 3:8.) Tingakhale amaganizo amodzi ndi abale komanso alongo athu tikamatengela kaganizidwe ka Yehova komwe kali m’Baibulo. Timveketse mfundoyi motele: Tiyelekeze kuti wofalitsa mu mpingo mwanu wawelenga mawu amene Yesu anakamba polimbikitsa ophunzila ake kuika Ufumu patsogolo mu umoyo wawo. (Mat. 6:33) Wofalitsayo atalimbikitsidwa ndi mfundo ya Yesu imeneyi, waganiza zoyamba utumiki wa nthawi zonse. Kodi tiyenela kucita naye motani wofalitsa wotelo? Tiyenela kukamba zabwino zokhudza colinga cakeco ndi kumuuza kuti tidzamuthandiza, m’malo momulimbikitsa kuti asankhe umoyo wawofuwofu.
KHALANI ODZICEPETSA
9-10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali wodzicepetsa kwambili?
9 Usiku wakuti mawa lake aphedwa, Yesu anaphunzitsa Petulo ndi atumwi ena phunzilo lofunika kwambili pa nkhani ya kudzicepetsa. Masana a tsikulo, Yesu anali atatuma Petulo ndi Yohane kukaika zinthu m’malo pokonzekela cakudya cothela codya nawo limodzi asanaphedwe. Mwacionekele, cimodzi mwa zinthu zimene anayenela kucita pokonzekela ndi kuonetsetsa kuti pali beseni komanso mathaulo zomwe zikanagwilitsidwa nchito posambika mapazi a opezekapo asanayambe kudya. Koma kodi ndani akanadzipeleka kugwila nchito yotsika imeneyo?
10 Yesu sanazengeleze kugwila nchito imeneyo, ndipo kucita izi kunaonetsa kuti iye anali wodzicepetsa kwambili. Atumwi ake anadabwa kwambili kuona kuti Yesu akugwila nchito imene kambili inali kugwilidwa ndi wanchito. Yesu anavula malaya ake akunja ndi kumanga thaulo m’ciuno mwake. Atatelo anathila madzi m’beseni ndi kuyamba kuwasambika mapazi. (Yoh. 13:4, 5) Ziyenela kuti zinatenga nthawi kusambika mapazi a atumwi onse 12. Yesu anasambikanso mapazi a Yudasi amene anali kudzamupeleka. Koma Yesu modzicepetsa anagwila nchitoyo. Kenako iye moleza mtima anafotokoza kuti: “Kodi mukudziwa cifukwa cake ndasambitsa mapazi anu? Inu mumandichula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, cifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye. Conco ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso mukuyenela kusambitsana mapazi.”—Yoh. 13:12-14.
Kudzicepetsa kwenikweni kumaphatikizapo . . . mmene timadzionela ife eni komanso mmene timaonela ena
11. Kodi Petulo anaonetsa bwanji kuti anaphunzila kukhala wodzicepetsa? (1 Petulo 5:5) (Onaninso cithunzi.)
11 Petulo anatengapo phunzilo pa kudzicepetsa kwa Yesu. Yesu atabwelela kumwamba, Petulo anacilitsa munthu amene anabadwa wolumala. (Mac. 1:8, 9; 3:2, 6-8) N’zosadabwitsa kuti khamu la anthu linabwela kudzaona cozizwitsaci. (Mac. 3:11) Popeza Petulo anakulila pakati pa anthu amene anali kufunitsitsa kuchuka komanso maudindo, kodi analola kulandila ulemelelo umene anapatsidwa? Ayi, Petulo modzicepetsa anakana kulandila ulemelelowo. Ndipo moyenelela anaupeleka kwa Yehova ndi Yesu mwa kunena kuti: “M’dzina [la Yesu] komanso cifukwa coti timakhulupilila dzina lakelo, munthu amene mukumuona ndiponso kumudziwayu wacila.” (Mac. 3:12-16) Patapita nthawi, Petulo analembela Akhristu kalata yowauza za kufunika kokhala odzicepetsa. Mawu amene Petulo anagwilitsa nchito amatikumbutsa pamene Yesu anamanga thaulo m’ciuno mwake ndi kusambika mapazi a ophunzila ake.—Welengani 1 Petulo 5:5.
Petulo atacita cozizwitsa, anapeleka ulemelelo kwa Yehova ndi Yesu. Ifenso tingaonetse kudzicepetsa mwa kucita zabwino popanda kuyembekezela kutamandidwa kapena kulandila mphoto (Onani ndime 11-12)
12. Potengela Petulo, kodi tingatani kuti tisaleke kukulitsa khalidwe la kudzicepetsa?
12 Ifenso tingatengele citsanzo ca Petulo ca kukhala odzicepetsa. Kudzicepetsa kwenikweni kumaonekelanso m’zocita osati m’mawu okha. Liwu limene Petulo analichula lotanthauza kudzicepetsa limaphatikizaponso mmene timadzionela ife eni komanso mmene timaonela anthu ena. Pocitila ena zinthu, colinga si kufuna kutamandidwa ayi, koma cifukwa cokonda Yehova komanso anthu. Timaonetsa kuti ndife odzicepetsa tikamatumikila Yehova komanso abale athu mmene tingathele, kaya ena akuona kapena ayi.—Mat. 6:1-4.
KHALANI “OGANIZA BWINO”
13. Kodi kukhala “oganiza bwino” kumalowetsamo ciyani?
13 Kodi kukhala “oganiza bwino” kumalowetsamo ciyani? (1 Pet. 4:7) Mkhristu woganiza bwino amadzifunsa mmene Yehova amaonela nkhani inayake asanapange cisankho. Mkhristu wotelo amadziwa kuti palibe cinthu cofunika kwambili kuposa ubale wake ndi Yehova pa umoyo wake. Sadziona mopambanitsa, koma amazindikila kuti sadziwa zonse. Amaonetsa kuti amadalila Mulungu mwa kupemphela kawilikawili kwa Yehova modzicepetsa.a
14. Kodi Petulo analephela motani kudalila Yehova pa nthawi ina?
14 Usiku wakuti mawa lake aphedwa, Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Nonsenu muthawa nʼkundisiya ndekha usiku uno.” Koma Petulo anayankha mwacidalilo kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Usiku umenewo, Yesu analimbikitsa ena mwa ophunzila ake kuti: “Khalani maso ndipo mupitilize kupemphela.” (Mat. 26:31, 33, 41) Petulo akanatsatila uphungu umenewu, akanalimba mtima n’kunena kuti anali wophunzila wa Yesu. M’malomwake, iye anakana Mbuye wake, ndipo izi zinamupweteka mtima kwambili.—Mat. 26:69-75.
15. N’ciyani cinathandiza Yesu kukhala woganiza bwino pa usiku wake wothela asanaphedwe?
15 Yesu anadalila Yehova ndi mtima wake wonse. Ngakhale kuti Yesu anali wangwilo, anapemphela mobwelezabweleza kwa Yehova usikuwo. Izi zinam’thandiza kukhala wolimba mtima kucita zimene Yehova anali kufuna. (Mat. 26:39, 42, 44; Yoh. 18:4, 5) Petulo anaona Yesu akupemphela mobwelezabweleza usikuwo, ndipo sanaiwale zimenezo kwa moyo wake wonse.
16. Kodi Petulo anaonetsa bwanji kuti anakhala woganiza bwino? (1 Petulo 4:7)
16 Patapita nthawi, Petulo anaphunzila kudalila kwambili Yehova mwa kupemphela. Yesu ataukitsidwa, anatsimikizila Petulo ndi atumwi ena kuti iwo adzalandila mzimu woyela kuti uwathandize kugwila nchito yolalikila imene anapatsidwa. Komabe, Yesu anawauza kuti akhalebe mu Yerusalemu mpaka zimenezo zitacitika. (Luka 24:49; Mac. 1:4, 5) Kodi Petulo anali kucita ciyani poyembekezela? Iye ndi Akhristu anzake “ankalimbikila kupemphela.” (Mac. 1:13, 14) Patapita nthawi, Petulo analimbikitsa Akhristu anzake m’kalata yake yoyamba kuti akhale oganiza bwino, komanso kuti azidalila Yehova mwa kupemphela. (Welengani 1 Petulo 4:7.) Petulo anaphunzila kudalila Yehova, ndipo anadzakhala mzati mu mpingo.—Agal. 2:9.
17. Kaya tili ndi maluso otani acibadwa, tisaiwale kucita ciyani? (Onaninso cithunzi.)
17 Kuti tikhale oganiza bwino, tiyenela kumapemphela kwa Yehova kawilikawili. Kaya tili ndi maluso otani acibadwa, m’pofunikabe kupitiliza kupemphela kwa Yehova. Makamaka pamene tifunika kupanga zisankho zazikulu, tisaiwale kupemphela kwa Yehova kuti atitsogolele, tili ndi cidalilo cakuti iye ndiye adziwa zimene zili zabwino koposa kwa ife.
Petulo anaphunzila kudalila Yehova mwa kupemphela. Ifenso tingakhale oganiza bwino mwa kupempha Yehova kuti atithandize makamaka popanga zisankho zikuluzikulu (Onani ndime 17)b
18. Tiyenela kucita ciyani kuti kaganizidwe kathu kakhale kofanana kwambili ndi ka Yehova?
18 Timayamikila kwambili kuti Yehova anatilenga m’njila yakuti tizitha kutengela makhalidwe ake. (Gen. 1:26) Koma sikuti tingakwanitse kutengela makhalidwe a Yehova ndendende mmene iye alili. (Yes. 55:9) Komabe monga anacitila Petulo, nafenso tingapangitse kaganizidwe kathu kuti kakhale kofanana kwambili ndi ka Yehova. Tingacite zimenezi mwa kupitiliza kutengela kaganizidwe ka Mulungu, kukhala odzicepetsa komanso oganiza bwino.
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
a Kuti mudziwe zambili pa tanthauzo la kuganiza bwino, onani mpambo wa nkhani ku Chichewa wakuti “Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo” pankhani yakuti “Kufotokoza 2 Timoteyo 1:7—‘Mulungu Sanatipatse Mzimu Wamantha,’” pansi pa kamutu kakuti “Kuganiza bwino.” Nkhanizi mungazipeze pa jw.org kapena mu JW Library®.
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akupeleka pemphelo camumtima pomwe akuyembekezela ma intavyu a nchito.