LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 March masa. 26-31
  • Dzanja la Yehova Silinafupikepo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Dzanja la Yehova Silinafupikepo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TENGAM’PONI PHUNZILO PA ZIMENE ZINACITIKILA MOSE NDI AISIRAELI
  • TIKAMALIMBANA NDI MAVUTO AZACUMA
  • POKONZEKELA ZA TSOGOLO LATHU
  • Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 March masa. 26-31

NKHANI YOPHUNZILA 13

NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’

Dzanja la Yehova Silinafupikepo

“Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?”​—NUM. 11:23.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nkhani ino itithandiza kukhala ndi cidalilo cakuti Yehova adzatithandiza kuthupi. Idzatithandizanso kuwonjezela cidalilo cimene tili naco kale.

1. Kodi Mose anaonetsa bwanji cidalilo mwa Yehova pamene anali kutsogolela Aisiraeli powatulutsa mu Iguputo?

BUKU la Aheberi limachula anthu ambili omwe anali ndi cikhulupililo colimba mwa Yehova. Mmodzi wa iwo ndi Mose, amene anaonetsa cikhulupililo m’njila yapadela. (Aheb. 3:​2-5; 11:​23-25) Iye anaonetsa cikhulupililo potulutsa Aisiraeli mu Iguputo. Sanacite mantha ndi Farao komanso gulu lake la nkhondo. Iye anadalila Yehova, ndipo anatsogolela Aisiraeli kudutsa pa Nyanja Yofiila. Pambuyo pake, anawatsogolela m’cipululu. (Aheb. 11:​27-29) Cidalilo ca Aisiraeli ambili cinali citatha mwa Yehova, koma Mose anadalilabe Mulungu. Mose sanagwilitsidwe mwala cifukwa ca cikhulupililo cake. Tikutelo cifukwa mozizwitsa, Mulungu anapatsa anthuwo madzi ndi cakudya m’cipululu.a​—Eks. 15:​22-25; Sal. 78:​23-25.

2. N’ciyani cinacititsa Mulungu kufunsa Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi”? (Numeri 11:​21-23)

2 Koma ngakhale kuti Mose anali ndi cikhulupililo colimba, patapita caka cimodzi Yehova atatulutsa Aisiraeli ku Iguputo mozizwitsa, Mose anakaikila zakuti Yehova angawapatsedi nyama anthu ake. Mose anaona kuti zinali zosatheka Yehova kupatsa anthu ofika m’mamiliyoni nyama omwe anali m’cipululu mopanda anthu. Pomuyankha, Yehova anam’funsa kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?” (Welengani Numeri 11:​21-23.) Mawu akuti “Dzanja la Yehova” atanthauza mzimu woyela wa Mulungu kapena kuti mphamvu zake zimene amagwilitsa nchito. M’mawu ena, zinali ngati Yehova anali kufunsa Mose kuti, ‘Kodi zoona ukuganiza kuti ndingalephele kukwanilitsa zimene ndalonjeza?’

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kucita cidwi ndi zimene zinacitikila Mose ndi Aisiraeli?

3 Kodi munakaikilapo zakuti Yehova angasamalile zosowa zanu komanso za banja lanu? Mulimonsemo, tiyeni tikambilane cifukwa cake Mose ndi Aisiraeli anakaikila zakuti Mulungu angawasamalile. Mfundo za m’Malemba zimene tikambilane zidzatithandiza kulimbitsa cidalilo cathu cakuti dzanja la Yehova silalifupi.

TENGAM’PONI PHUNZILO PA ZIMENE ZINACITIKILA MOSE NDI AISIRAELI

4. N’ciyani ciyenela kuti n’cimene cinapangitsa anthu ambili kukaikila zakuti Yehova angawasamalile?

4 N’ciyani cinapangitsa Aisiraeli kuyamba kukaikila zakuti Yehova angawasamalile? Aisiraeli komanso “gulu la anthu amitundu yosiyanasiyana” anali atakhala m’cipululu cacikuluco kwa kanthawi paulendo wawo wocoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. (Eks. 12:38; Deut. 8:15) Gulu la anthu amitundu yosiyanasiyana anatinkhiwa nawo mana, ndipo nawonso Aisiraeli anayamba kudandaula. (Num. 11:​4-6) Anthuwo anayamba kuyewa zakudya zimene anali nazo ku Iguputo. Popeza anthu anali kudandaula kwa Mose, zioneka kuti iye anali kuganiza kuti ndiye afunika kupatsa anthuwo nyama.​—Num. 11:​13, 14.

5-6. Tiphunzilapo ciyani tikaona mmene anthu amitundu yosiyanasiyana anasonkhezela Aisiraeli ambili?

5 Mwacionekele, mzimu wosayamikila wa anthu amitundu yosiyanasiyana unayawambukila Aisiraeli. N’zotheka nafenso kutengela mzimu wosayamikila wa ena n’kukhala wosakhutila ndi zimene Yehova amatipatsa. Izi zingacitike tikamayewa zinthu zomwe tinali nazo, kapenanso ngati timasilila zimene ena ali nazo. Komabe, tingakhale acimwemwe tikamakhala okhutila kaya zinthu zili motani kwa ife.

6 Aisiraeli anafunika kukumbukila kuti Mulungu anawatsimikizila kuti adzawapatsa zinthu zambili zakuthupi akafika. Lonjezolo linali kudzakwanilitsidwa akafika m’Dziko Lolonjezedwa, osati pomwe anali pa ulendowo m’cipululu. Ifenso sitiyenela kuika maganizo athu pa zinthu zimene tilibe m’dongosolo lino la zinthu. M’malomwake, tiyenela kuganizila kwambili zimene Yehova walonjeza kutipatsa m’dziko latsopano. Tingacitenso bwino kusinkhasinkha Malemba amene angatithandize kukulitsa cidalilo cathu mwa Yehova.

7. N’cifukwa ciyani sitikaikila kuti dzanja la Yehova silalifupi?

7 Yehova pofunsa Mose funso lili pa Numeri 11:​23, n’kutheka anali kufuna kum’phunzitsa mfundo ziwili: (1) Mphamvu zake n’zopanda malile. (2) Mphamvu zake zingafike kulikonse. Mulungu anali nazo mphamvu zopatsa Aisiraeli nyama, ngakhale kuti anali m’cipululu mopanda kanthu. Mulungu anaonetsa mphamvu zake “ndi dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula.” (Sal. 136:​11, 12) Conco pamene tikukumana ndi mavuto, tisakaikile zakuti dzanja la Yehova lidzatithandiza kulikonse kumene tingakhale.​—Sal. 138:​6, 7.

8. Tingatani kuti tipewe mzimu wadyela umene anthu ambili anaonetsa m’cipululu? (Onaninso cithunzi.)

8 Posapita nthawi, Yehova anagawila anthu ake nyama. Anawatumizila zinzili zankhaninkhani. Ngakhale n’telo, Aisiraeli sanayamikile Mulungu pa cozizwitsaci. M’malomwake, ambili a iwo anakhala adyela. Iwo anagwila nchito yotola zinzili usana ndi usiku. Yehova anakwiya nawo kwambili anthu “amene anasonyeza mtima wadyela,” ndipo anawalanga. (Num. 11:​31-34) Pali phunzilo pa cocitikaci. Tiyenela kusamala kuti tisagwele mumsampha wokhala adyela. Kaya ndife olemela kapena ayi, cinthu cofunika kwambili mu umoyo wathu cizikhala kuunjika ‘cuma cathu kumwamba’ mwa kukhala pa ubale wolimba ndi Yehova komanso Yesu. (Mat. 6:​19, 20; Luka 16:9) Tikatelo, sitikaikila kuti Yehova adzatisamalila.

Aisiraeli ali m’cipululu ndipo akutola zinzili usiku.

Ndi mzimu wotani umene ambili anaonetsa m’cipululu? Ndipo tiphunzilapo ciyani? (Onani ndime 8)


9. Kodi sitikaikila za ciyani?

9 Yehova amatambasula dzanja lake kuti athandize anthu ake masiku ano. Ngakhale n’telo, izi sizitanthauza kuti sitingataikilidwe katundu kapena kusowa cakudya.b M’malomwake, zitanthauza kuti Yehova sangatitaye. Iye adzatithandiza tikakhala pa mavuto osiyanasiyana. Kodi tingaonetse bwanji cidalilo cathu cakuti Yehova adzatisamalila? Tiyeni tikambilane mbali ziwili izi: (1) tikamalimbana ndi mavuto azacuma, komanso (2) tikamakonzekela tsogolo lathu.

TIKAMALIMBANA NDI MAVUTO AZACUMA

10. Ndi mavuto azacuma ati amene tingakumane nawo?

10 Pamene dongosolo lino lifika kumapeto, tingayembekezele kuti mavuto azacuma adzawonjezeka. Cipwilikiti ca ndale za dziko, nkhondo, matsoka a zacilengedwe, kapena milili yatsopano zingapangitse kuti tigwilitse nchito ndalama m’njila imene sitinayembekezele kapena tingacotsedwe nchito, kusiya katundu wathu kapenanso nyumba yathu. Tingakakamizike kupeza nchito yatsopano m’dela limene tikukhala kapena kuganizila zosamukila ku dela lina kuti tikathe kusamalila banja lathu. Kodi n’ciyani cingatithandize kupanga zisankho zoonetsa kuti timalidalila dzanja la Yehova?

11. N’ciyani cingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto azacuma? (Luka 12:​29-31)

11 Njila yofunika kwambili komanso yothandiza ndi kuuza Yehova nkhawa zanu. (Miy. 16:3) M’pempheni kuti akupatseni nzelu zokuthandizani kupanga zisankho zabwino, komanso kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wodekha kuti ‘musavutike mumtima’ pa zimene zikukucitikilani. (Welengani Luka 12:​29-31.) M’pempheninso kuti mukhale okhutila ndi zimene muli nazo. (1 Tim. 6:​7, 8) Fufuzani m’zofalitsa zathu zokhudza zimene mungacite kuti muthane ndi mavuto azacuma. Nkhani za pa jw.org zokamba za mavuto azacuma zathandiza anthu ambili.

12. Ndi mafunso ati amene angathandize Mkhristu kupangila banja lake cisankho cabwino koposa?

12 Ena akopeka kulowa nchito yowapangitsa kukhala kutali ndi banja lawo. Koma ambili amadzazindikila atazigwilitsa kale fuwa lamoto kuti cimeneco sicinali cisankho canzelu. Musanalowe nchito yatsopano, osangoganizila pa ndalama zimene mudzapata koma muziganizilanso ngati nchitoyi idzatsamwitsa uzimu wanu. (Luka 14:28) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ukwati wanga udzakhudzidwa motani ndikakhala kutali ndi mnzanga wamuukwati? Kodi ndidzikwanitsa kupezeka pa misonkhano, kulalikila, komanso kuyanjana ndi Akhristu anzanga?’ Ngati ndinu kholo muyenelanso kudzifunsa funso lofunika kwambili lakuti: ‘Ngati sindikhala ndi ana anga, kodi ndidzakwanitsa bwanji “kuwalela powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena?”’ (Aef. 6:4) Popanga zisankho, muzipewa kutsatila a m’banja mwanu kapena anzanu amene satsatila mfundo za m’Baibulo. M’malomwake, muzitsatila kaganizidwe ka Mulungu.c Tony amene akhala kum’madzulo kwa Asia analandilapo mwayi kangapo konse wokagwila nchito ku maiko akunja. Komabe ataipemphelela nkhaniyi komanso atakambilana ndi mkazi wake, anakana kulowa nchitozo. M’malomwake, anasankha kucepetsa zinthu zimene anali kugula. Anati: “Ndathandiza anthu ambili kudziwa Yehova, ndipo ana athu amacikonda coonadi. Banja lathu laphunzila kuti tikamagwilitsa nchito mfundo ya pa Mateyo 6:​33, Yehova azitisamalila.”

POKONZEKELA ZA TSOGOLO LATHU

13. Tingacite ciyani kuti tikakhale ndi kenakake pambali tikadzakalamba?

13 Cidalilo cathu mwa Yehova cingayesedwenso tikamaganizila mmene zinthu zidzakhalila tikadzakalamba. Baibulo limatilimbikitsa kugwila nchito mwakhama kuti tikathe kudzisamalila kutsogolo. (Miy. 6:​6-11) Ngati tingakwanitse kusunga kenakake pambali kaamba ka m’tsogolo, ndi bwino kutelo. N’zoona kuti ndalama zingatiteteze. (Mlal. 7:12) Komabe, tiyenela kupewa kukhala umoyo wongofunafuna cuma.

14. Kodi Aheberi 13:5 ingatithandize bwanji pokonzekela tsogolo lathu?

14 Pogwilitsa nchito fanizo, Yesu anaonetsa kuti n’kupanda nzelu kuunjika cuma padziko lapansi popanda kukhala “wolemela kwa Mulungu.” (Luka 12:​16-21) Zamawa sizidziwika. (Miy. 23:​4, 5; Yak. 4:​13-15) Cifukwa cokhala otsatila a Yesu, timakumana ndi mavuto amene anthu ena sakumana nawo. Pa nkhaniyi, Yesu anati tiyenela kukhala okonzeka “kusiya” zinthu zathu zonse zakuthupi kuti tikhale otsatila ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolela kusiya zinthu zawo zakuthupi ali acimwemwe. (Aheb. 10:34) Masiku anonso, abale ambili alolela kutayikilidwa katundu wawo wakuthupi cifukwa cokana kukhalila mbali m’zandale. (Chiv. 13:​16, 17) Cawathandiza n’ciyani kucita zimenezi? Iwo amakhulupilila ndi mtima wonse lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Welengani Aheberi 13:5.) Timacita zonse zotheka pokonzekela tsogolo lathu. Koma ngati zinthu za mwadzidzidzi zatigwela, timadalila kuti Yehova adzatithandiza.

15. Kodi makolo sayenela kuwaona motani ana awo? (Onaninso cithunzi.)

15 Kumadela ena, makolo amakhala ndi ana n’colinga cakuti iwo akadzakalamba, anawo adzawasamalile. M’njila ina, makolowo amaona anawo ngati mbelekelo ya ukalamba wawo. Baibulo limakamba kuti makolo ayenela kusamalila zosowa za ana awo. (2 Akor. 12:14) N’zoona kuti makolo angafunikile thandizo pamene akukalamba, ndipo ana ambili amakhala okonzeka kuwathandiza. (1 Tim. 5:4) Koma makolo acikhristu amazindikila kuti cimwemwe ceniceni cimabwela cifukwa cothandiza ana awo kukhala atumiki a Yehova, osati cifukwa colela anawo kuti akawathandize kuthupi.​—3 Yoh. 4.

Mwamuna ndi mkazi wake mosangalala akukambilana ndi mwana wawo wamkazi ndi mwamuna wake pa vidiyokomfalensi. Mwana wamkaziyo ndi mwamuna wake avala zovala zakunchito.

Mabanja acikhristu odzipeleka amaganizila mfundo za m’Baibulo akamapanga zisankho zokhudza tsogolo lawo (Onani ndime 15)d


16. Kodi makolo angacite ciyani pothandiza ana awo kuti akathe kudzisamalila okha? (Aefeso 4:28)

16 Mwa citsanzo canu, phunzitsani ana anu kudalila Yehova pamene mukuwakonzekeletsa kuti akathe kudzisamalila okha. Kungoyambila ali ana, athandizeni kuona kufunika kogwila nchito molimbika. (Miy. 29:21; welengani Aefeso 4:28.) Pamene akusinkhuka, athandizeni kuti aziikako nzelu kusukulu. Makolo acikhristu angacite bwino kufufuza mfundo za m’Baibulo ndi kuzigwilitsa nchito pothandiza ana awo kuona mmene angagwilitsile nchito maphunzilo awo mwanzelu kuti akathe kudzisamalila okha, komanso kuti azitengamo mbali mokwanila m’nchito yacikhristu.

17. Kodi tingakhale otsimikiza za ciyani?

17 Atumiki a Yehova okhulupilika ayenela kumudalila kuti iye ali ndi mphamvu, komanso cikhumbo cokwanitsa kusamalila zosowa zawo zakuthupi. Cidalilo cathu mwa Yehova cidzayesedwa mokulilapo pamene tikuyandikila mapeto a dongosolo lino la zinthu. Koma mulimonse mmene zingakhalile, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kudalila kuti Yehova adzagwilitsa nchito mphamvu zake posamalila zosowa zathu. Sitikaikila kuti ndi dzanja lake lamphamvu komanso mkono wake wotambasula, Yehova adzatithandiza kulikonse kumene tili.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi maphunzilo ati omwe tingatengepo pa zimene zinacitikila Mose ndi Aisiraeli?

  • Tingaonetse bwanji cidalilo cathu mwa Yehova tikakumana ndi mavuto azacuma?

  • Tiziganizila ciyani tikamakonzekela tsogolo lathu?

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

a Onani “Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2023.

b Onani “Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi” mu Nsanja ya Mlonda ya September 15, 2014.

c Onani nkhani yakuti “Palibe Munthu Angatumikile Ambuye Aŵili” mu Nsanja ya Mlonda ya April 1, 2014.

d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Banja lodzipeleka lacikhristu likukambilana ndi mwana wawo amene akutumikila ndi mwamuna wake pa nchito yomanga Nyumba ya Ufumu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani