NKHANI YOPHUNZILA 16
NYIMBO 87 Bwelani Mutsitsimulidwe!
Kuyandikila Abale ndi Alongo Athu n’Kwabwino kwa Ife!
“Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!”—SAL. 133:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tikambilane zimene tingacite kuti tiwayandikile kwambili abale ndi alongo athu. Tikambilanenso madalitso amene timakhala nawo tikakhala pa ubwenzi ndi alambili anzathu.
1-2. Kodi cinthu cimodzi cofunika kwambili kwa Yehova n’citi? Nanga iye amafuna kuti tizicita ciyani?
KWA Yehova, mmene timacitila ndi alambili anzathu ndi nkhani yaikulu. Yesu anatiphunzitsa kuti tizikonda anzathu mmene timadzikondela ife eni. (Mat. 22:37-39) Izi ziphatikizapo kukhala okoma mtima ngakhale kwa anthu amene ndi osakhulupilila anzathu. Tikakhala okoma mtima, timakhala kuti tikutengela Yehova Mulungu amene “amawalitsila dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsela mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mat. 5:45.
2 N’zoona kuti Yehova amakonda anthu onse, koma makamaka amakonda amene amacita zoyenela. (Yoh. 14:21) Iye amafuna kuti tizitengela citsanzo cake. Conco amatilimbikitsa kuti ‘tiziwakonda kwambili’ abale ndi alongo athu komanso kuti tiziwaonetsa “cikondi ceniceni.” (1 Pet. 4:8; Aroma 12:10) Cikondi ca mtundu uwu n’cimene timaonetsa kwa wacibale amene timamukonda kapena bwenzi lathu lapamtima.
3. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani ponena za cikondi?
3 Cikondi cili ngati mtengo. Cimafuna kucisamalila kuti cikule. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Pitilizani kukonda abale.” (Aheb. 13:1) Yehova amafuna kuti tisaleke kukulitsa cikondi cathu pa ena. Nkhani ino idzafotokoza cifukwa cake tiyenela kuwayandikila kwambili alambili anzathu. Idzafotokozanso mmene tingapitilizile kucita zimenezo.
CIFUKWA CAKE TIYENELA KUYANDIKILANA KWAMBILI
4. Malinga ndi Salimo 133:1, kodi tingapitilize bwanji kuonetsa kuyamikila mgwilizano umene tili nawo? (Onaninso zithunzi.)
4 Welengani Salimo 133:1. Tigwilizana ndi zimene wamasalimo analemba kuti ndi “zabwino” komanso “zosangalatsa” kukhala pa ubwenzi weniweni ndi anthu okonda Yehova. Koma monga mmene munthu angalekele kunyadila mtengo waukulu wocititsa cidwi umene amauona tsiku lililonse, ifenso tingaleke kunyadila mgwilizano wathu wacikhristu. Zili conco cifukwa cakuti abale ndi alongo athu timawaona kawilikawili, mwinanso kangapo pa mlungu. Conco, kodi tingatani kuti tiziwaonabe kuti ndi amtengo wapatali? Tingakulitse cikondi pa abale ndi alongo athu mwa kupatula nthawi yoganizila kufunika kwa aliyense wa iwo mu mpingo komanso kwa ife.
Musaleke kunyadila mgwilizano wathu wokongola wacikhristu (Onani ndime 4)a
5. Kodi cikondi cimene timaonetsana cimawakhudza bwanji anthu ena?
5 Anthu amene amabwela kudzasonkhana nafe kwa nthawi yoyamba, amacita cidwi kwambili akaona cikondi cimene timaonetsana wina ndi mnzake. Akaona cikondi cimeneci, iwo amazindikila kuti apezadi coonadi. Yesu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Ganizilani zinacitikila mtsikana wina dzina lake Chaithra. Iye anali kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo anavomela ciitano cokapezeka pa msonkhano wa cigawo. Tsiku loyamba la msonkhano litatha, iye anauza amene anali kum’phunzitsa Baibulo kuti: “Makolo anga sanayambe andikumbatilapo. Koma pa msonkhano wanu, anthu andikumbatila maulendo 52 pa tsiku limodzi cabe! Ndinaona cikondi ca Yehova kudzela m’banja lake lauzimu. Ndikufuna kukhala m’banjali.” Chaithra anapitabe patsogolo ndipo anabatizika mu 2024. Inde, acatsopano akaona nchito zathu zabwino kuphatikizapo cikondi cimene timaonetsana, amasonkhezeleka kuyamba kutumikila Yehova.—Mat. 5:16.
6. Kodi kuyandikila kwambili abale ndi alongo athu kungatiteteze motani?
6 Kuyandikila kwambili abale ndi alongo kungatiteteze. Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitilizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku . . . kuti cinyengo camphamvu ca ucimo cisaumitse mtima wa aliyense wa inu.” (Aheb. 3:13) Tikalefuka kwambili moti tayamba kusocela, Yehova angagwilitse nchito wokhulupilila mnzathu amene wazindikila vuto lathu kuti atithandize. (Sal. 73:2, 17, 23) Kunena zoona, thandizo limene angatipatse ndi labwino kwa ife.
7. Pali kugwilizana kotani pakati pa cikondi ndi mgwilizano? (Akolose 3:13, 14)
7 Tili m’gulu la anthu amene amacita khama poonetsana cikondi. Conco timasangalala ndi madalitso oculuka. (1 Yoh. 4:11) Mwacitsanzo, cikondi cimatisonkhezela ‘kupitiliza kulolelana.’ Kuteloko kumalimbikitsa mgwilizano wathu wacikhristu. (Welengani Akolose 3:13, 14; Aef. 4:2-6) Conco, pa misonkhano yathu timasangalala ndi mtendele woculuka umene sungapezeke m’gulu lina lililonse pa dziko lapansi.
MUZICITILANA ULEMU
8. Kodi Yehova amacita ciyani potithandiza kuti tikhale ogwilizana?
8 Mgwilizano wapadziko lonse umene tili nawo ndi cozizwitsa. Zimenezi zimatheka ndi thandizo la Yehova ngakhale kuti ndife opanda ungwilo. (1 Akor. 12:25) Baibulo limakamba kuti ‘Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana.’ (1 Ates. 4:9) M’mawu ena tingati Yehova amagwilitsa nchito Malemba potiuza ndendende zimene tiyenela kucita kuti tiyandikilane. Tingaphunzitsidwe ndi Mulungu mwa kusanthula mosamala ziphunzitso zake komanso kuzigwilitsa nchito. (Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Izi n’zimene Mboni za Yehova zimayesetsa kucita.
9. Kodi tiphunzilapo ciyani pa Aroma 12:9-13 pa nkhani yoonetsana ulemu?
9 Kodi Mawu a Mulungu amatiphunzitsa ciyani kuti tithe kuyandikilana? Ganizilani zimene Paulo anakamba pa nkhaniyi pa Aroma 12:9-13. (Welengani.) Onani kuti pa lembali pali mawu akuti “pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.” Kodi izi zitanthauza ciyani? Tiyenela kuyamba ndi ifeyo kuonetsa ena “cikondi ceniceni” mwa kucita zinthu monga kukhululuka, kuceleza, komanso kukhala owolowa manja. (Aef. 4:32) Musayembekezele m’bale kapena mlongo wanu kuti akhale woyamba kukuyandikilani. “Muziyamba ndi inuyo.” Mukatelo, mudzaona kukwanilitsika kwa mawu amene Yesu anakamba akuti: “Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.
10. Kodi tingakhale bwanji akhama “pa nkhani yosonyezana ulemu”? (Onaninso cithunzi.)
10 N’zocititsa cidwi kuti Paulo atangotiuza kuti tiziyamba ndife pa nkhani yoonetsana ulemu, anatilimbikitsa kuti ‘tikhale akhama osati aulesi.’ Munthu wakhama amakhala wokangalika ndipo amagwila nchito molimbika. Akapatsidwa nchito, amaigwila moikilapo mtima. Miyambo 3:27, 28 imatilimbikitsa kuti: “Usalephele kucitila zabwino anthu amene ukuyenela kucitila zabwinozo, ngati ungathe kuwathandiza.” Ndipo ngati winawake akufunikila thandizo, timacita zimene tingathe kuti timuthandize. Sitizengeleza kapena kuganiza kuti winawake adzam’thandiza.—1 Yoh. 3:17, 18.
Tifunika kukhala patsogolo pothandiza abale ndi alongo athu amene akufunikila thandizo (Onani ndime 10)
11. N’ciyani cingatithandize kuyandikilana?
11 Njila inanso tingaonetsele ulemu kwa ena ndi kuwakhululukila mwamsanga akatilakwila. Aefeso 4:26 imati: “Dzuwa lisalowe mudakali okwiya.” N’cifukwa ciyani? Vesi 27 lionetsa kuti kukhala cikwiyile ‘kungam’patse mpata Mdyelekezi.’ Kudzela m’Mawu ake, Yehova amatiuza mobwelezabweleza kuti tizikhululukilana. Akolose 3:13 imatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kupitiliza . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.’ Kunyalanyaza zophophonya za ena komanso zolakwa zawo, ndi imodzi mwa njila zabwino koposa zotithandiza kuwayandikila. Tikamatelo, timathandiza “kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela, pokhala mwamtendele umene uli ngati comangila cimene cimatigwilizanitsa.” (Aef. 4:3) Mwacidule, tingati kukhululukila ena kumalimbitsa mgwilizano ndi mtendele wathu.
12. Kodi Yehova amatithandiza motani kukhala okhululuka?
12 N’zoona kuti zingakhale zovuta kukhululukila anthu amene atilakwila. Koma tingakwanitse mwa thandizo la mzimu wa Mulungu. Pambuyo potilimbikitsa kuti ‘tizikhala ndi cikondi ceniceni’ komanso “akhama,” Baibulo limatilimbikitsanso kuti: “Yakani ndi mzimu.” Munthu amene ‘akuyaka’ amakhala wokangalika kwambili komanso wodzipeleka cifukwa cosonkhezeledwa ndi mzimu woyela. (Aroma 12:11) Conco mzimu wa Mulungu ungatithandize kuonetsa cikondi ceniceni komanso kukhululukila ena ndi mtima wonse. Ndiye cifukwa cake timacondelela Yehova kuti atithandize.—Luka 11:13.
“PAKATI PANU PASAKHALE KUGAWANIKA”
13. N’ciyani cingabweletse magawano pakati pathu?
13 Mpingo umapangidwa ndi “anthu osiyanasiyana” a zikhalidwe zosiyanasiyana. (1 Tim. 2:3, 4) Tikapanda kusamala, kusiyanasiyana kumeneku kungabweletse magawano pa nkhani za munthu mwini monga kavalidwe ndi kudzikongoletsa, cithandizo ca mankhwala, kapena zosangalatsa. (Aroma 14:4; 1 Akor. 1:10) Popeza Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana, tiyenela kusamala kuti tisaumilize ena kuona kuti zisankho zathu ndizo zabwino kuposa za ena.—Afil. 2:3.
14. Kodi tiyenela kuyesetsa kukhala otani? Ndipo n’cifukwa ciyani?
14 Tingapewe kubweletsa magawano mu mpingo mwa kuyesetsa kukhala otsitsimula komanso olimbikitsa kwa ena nthawi zonse. (1 Ates. 5:11) Anthu ambili amene anali ozilala kapena ocotsedwa, abwezeletsedwa mu mpingo m’nthawi zaposacedwapa. Amenewa tikuwalandila ndi manja awili! (2 Akor. 2:8) Onani zinacitikila mlongo amene anapita ku Nyumba ya Ufumu pambuyo pokhala wozilala kwa zaka 10. Iye anati, “Onse anali kumwetulila ndipo anandipatsa moni wakumanja.” (Mac. 3:19) Kodi kukomeledwa mtima m’njila zosavuta zimenezo kunam’khudza motani? Iye anati, “N’namva dzanja la Yehova likunditsogolela kuti ndikhalenso wacimwemwe.” Tikakhala olimbikitsa kwa onse, Khristu angatigwilitsile nchito kuti tikhale otsitsimula kwa ‘amene akugwila nchito yotopetsa ndi yolemetsa.’—Mat. 11:28, 29.
15. Kodi tingalimbikitse mgwilizano m’njila ina iti? (Onaninso cithunzi.)
15 Njila ina tingalimbikitsile mgwilizano ndi m’zokamba zathu. Yobu 12:11 imati: “Kodi si paja khutu limasiyanitsa mawu ngati mmene lilime limasiyanitsila kakomedwe ka cakudya?” Wophika wabwino amalawa cakudya asanagawile ena pofuna kutsimikiza kuti n’cokoma. Ifenso tiyenela kuziganizila kaye zokamba zathu tisanazikambe kwa ena. (Sal. 141:3) Colinga cathu nthawi zonse ndi kutsimikiza kuti mawu athu akhale olimbikitsa, otsitsimula, komanso kuti “athandize anthu amene akumvetsela.”—Aef. 4:29.
Muziyamba mwaziganizila kaye zimene mufuna kukamba (Onani ndime 15)
16. Ndani makamaka ayenela kuyesetsa kukamba mawu olimbikitsa?
16 Makamaka amuna okwatila ndi makolo ayenela kukhala chelu kuti akhale olimbikitsa m’zokamba zawo. (Akol. 3:19, 21; Tito 2:4) Akulu naonso ayenela kukhala gwelo la citsitsimutso komanso citonthozo monga abusa a nkhosa za Yehova. (Yes. 32:1, 2; Agal. 6:1) Mwambi wina wa m’Baibulo umatikumbutsa kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili.”—Miy. 15:23.
“TIZISONYEZANA CIKONDI CENICENI M’ZOCITA ZATHU”
17. Tingatani kuti cikondi cathu pa abale ndi alongo cizicokela mu mtima?
17 Mtumwi Yohane anatilimbikitsa kuti “tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceniceni m’zocita zathu.” (1 Yoh. 3:18) Timafuna kuti cikondi cathu pa abale ndi alongo cizicokela mu mtima. Kodi tingacite motani zimenezo? Tikamaceza kawilikawili ndi abale komanso alongo athu, tidzayandikilana nawo kwambili, ndipo cikondi pakati pathu cidzakula. Conco muzipeza mipata yocezako ndi ena pa misonkhano komanso mu ulaliki. Muzipatula nthawi yoyendelako ena. Tikatelo, timaonetsa kuti ‘Mulungu akutiphunzitsa kuti tizikondana.’ (1 Ates. 4:9) Ndipo tidzapitiliza kudzionela tokha kuti “ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!”—Sal. 133:1.
NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake
a MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Monyadila, mlongo akuyangana mtengo waukulu. Pambuyo pake, akukumbatila mlongo wina pa msonkhano wa cigawo. Pa msonkhanowo, ena akukambilana mwacimwemwe.