LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 May masa. 20-25
  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Yesu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Yesu?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “INE NDACITITSA KUTI IWO ADZIWE DZINA LANU”
  • “DZINA LANU LIMENE MWANDIPATSA”
  • “ATATE LEMEKEZANI DZINA LANU”
  • “NDIKUPELEKA MOYO WANGA”
  • “NDAMALIZA KUGWILA NCHITO IMENE MUNANDIPATSA”
  • Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Ife?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • “Tamandani Dzina la Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Dipo Limatiphunzitsa Ciyani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • “Sankhani . . . Amene Mukufuna Kum’tumikila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 May masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 22

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

Kodi Dzina la Yehova Ndi Lofunika Motani kwa Yesu?

“Ine ndacititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziwitsa dzinalo.”​—YOH. 17:26.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene Yesu anadziwitsila anthu za dzina la Yehova, mmene analiyeletsela, ndi mmene analikwezela.

1-2. (a) Kodi Yesu anacita ciyani usiku wakuti mawa lake aphedwa? (b) Ndi mafunso ati omwe tikambilana m’nkhani ino?

LINALI Lacinayi madzulo, mdima uli bii pa Nisani 14 mu 33 C.E. Ndipo Yesu anali atatsala pang’ono kupelekedwa, kuweluzidwa, kutsutsidwa, kuzunzidwa, ndi kuphedwa. Pa nthawiyi n’kuti wangomaliza kumene kudya cakudya capadela m’cipinda capamwamba ndi atumwi ake okhulupilika. Atamaliza, Yesu anauza atumwi ake mawu othela acilimbikitso. Koma atatsala pang’ono kutuluka m’cipindamo, Yesu anayamba wapeleka pemphelo logwila mtima kwambili. Mtumwi Yohane analilemba pemphelo limenelo. Limapezeka mu Yohane caputala 17.

2 Kodi pemphelo la Yesu limationetsa motani zimene zinali zofunika kwambili kwa iye pa nthawiyo? Nanga pemphelo limenelo limaonetsa motani zimene zinali zofunika kwambili kwa iye pocita utumiki wake wonse wapadziko lapansi? Tiyeni tikambilane mayankho a mafunso amenewa.

“INE NDACITITSA KUTI IWO ADZIWE DZINA LANU”

3. Kodi Yesu anati ciyani za dzina la Yehova? Nanga anatanthauzanji? (Yohane 17:​6, 26)

3 Yesu m’pemphelo lake anati: “Ine ndacititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.” Kawili konse, anachula mfundo yakuti anadziwitsa ophunzila ake za dzina la Yehova. (Welengani Yohane 17:​6, 26.) Kodi anatanthauzanji pamenepa? Kodi anatanthauza kuwachulila dzina lenileni lomwe anali kulidziwa kale? Ophunzila a Yesu anali Ayuda. Conco dzina la Mulungu lakuti Yehova anali kulidziwa kale. Dzinalo linali kupezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’Malemba a Ciheberi. Conco, Yesu pokamba mawuwo sanatanthauze dzina lenileni la Mulungu. M’malomwake, anatanthauza zimene dzinalo limaimila. Iye anathandiza ophunzila ake kum’dziwa bwino Yehova. Izi zinaphatikizapo kuwathandiza kumvetsa colinga ca Yehova cokhudza dziko lapansi ndi anthu, zimene anacita kumbuyo, zimene adzacita m’tsogolo, komanso makhalidwe ake. Ndipo palibe wina aliyense amene akanatha kufotokoza za Yehova m’njila imeneyi.

4-5. (a) Pelekani citsanzo coonetsa mmene dzina la munthu lingakhalile lofunika kwa ife. (b) Kodi ophunzila a Yesu anafika podziwa dzina la Yehova m’lingalilo lotani?

4 Tinene kuti pali mkulu wina mu mpingo mwanu dzina lake David amene ndi dokotala. M’baleyo mwamudziwa kwa zaka zambili. Tsiku lina inu mukudwala mwadzidzidzi. Akukuthamangitsilani ku cipatala kumene m’baleyo amagwilila nchito. Ndipo iye akugwilitsa nchito luso lake la udokotala populumutsa moyo wanu. Apa tsopano mukuyamba kumukonda mowilikiza m’baleyo kuposa kale. Ndipo mukangomva dzina lake likuchulidwa, mukuganizilanso zimene anakucitilani. Tsopano, David si mkulu cabe mu mpingo mwanu. Wakhalanso dokotala amene anapulumutsa moyo wanu.

5 Mofananamo, ophunzila a Yesu anali kulidziwa kale dzina lakuti Yehova. Koma dzinalo linakhala lofunika koposa kwa iwo pamene Yesu anawathandiza kumudziwa bwino Yehova. Tikutelo cifukwa ciyani? Cifukwa Yesu anaonetsa umunthu wa Atate wake m’zonse zimene anali kukamba ndi kucita. Conco, atumwi ake anafika ‘pomudziwa’ bwino Yehova mwa kuona mmene Yesu anali kuphunzitsila ndi kucitila zinthu ndi anthu.​—Yoh. 14:9; 17:3.

“DZINA LANU LIMENE MWANDIPATSA”

6. Kodi Yesu anatanthauza ciyani pomwe anati anapatsidwa dzina la Yehova? (Yohane 17:​11, 12)

6 Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Ayang’anileni cifukwa ca dzina lanu limene mwandipatsa.” (Welengani Yohane 17:​11, 12.) Kodi izi zikutanthauza kuti Yesu anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Yehova? Ayi. Onani kuti m’pemphelo limeneli pofotokoza za dzina la Yehova, Yesu anati “dzina lanu.” Conco sanatenge dzina la Yehova kukhala lake. Ndiye kodi Yesu anatanthauza ciyani pomwe anati dzina la Mulungu linapatsidwa kwa iye? Comwe tiyenela kudziwa n’cakuti Yesu anali Woimilako Yehova komanso Womulankhulilako. Anabwela m’dzina la Atate wake ndipo anacita zinthu zamphamvu m’dzina limenelo. (Yoh. 5:43; 10:25) Kuwonjezela apo, dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndi Cipulumutso.” Conco tanthauzo la dzina la Yesu limaphatikizapo dzina la Yehova.

7. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yesu analankhulila m’dzina la Yehova.

7 Timveketse mfundoyi motele: Kazembe wa dziko amaimilako wolamulila amene wamutumiza ku dziko lina. Ndipo amalankhula m’dzina la wolamulilayo. Conco kazembeyo akalankhula, zimakhala ngati wolamulilayo ndiye walankhula. Mofananamo, Yesu anali kuimilako Yehova ndipo anali kulankhula kwa anthu m’dzina la Yehova.​—Mat. 21:9; Luka 13:35.

8. Kodi dzina la Yehova linali “mwa” Yesu asanabwele pa dziko lapansi m’lingalilo lotani? (Ekisodo 23:​20, 21)

8 Pa udindo wake monga Mawu, Yesu watumikila Yehova monga womulankhulilako mwa kupeleka mauthenga ndi malangizo kwa ana ena auzimu a Mulungu komanso kwa anthu. (Yoh. 1:​1-3) N’kutheka Yesu ndiye mngelo amene Yehova anatuma kukasamalila Aisiraeli pomwe anali m’cipululu. Pouza Aisiraeli kuti amvele mngeloyo, Yehova anati: “Popeza dzina langa lili mwa iye.”a (Welengani Ekisodo 23:​20, 21.) Dzina la Yehova linali “mwa” Yesu m’lingalilo lakuti Yesu anali kuimilako Yehova, ndipo ndiye ali patsogolo poyeletsa dzina la Atate wake ndi kuteteza mbili yawo.

“ATATE LEMEKEZANI DZINA LANU”

9. Kodi dzina la Yehova linali lofunika motani kwa Yesu? Fotokozani.

9 Monga taonela m’ndime 8, ngakhale Yesu asanabwele pa dziko lapansi, dzina la Yehova linali lofunika koposa kwa iye. Ici ndiye cifukwa cake ali padziko lapansi, anaonetsa m’zocita zake zonse kufunika kwa dzina la Yehova. Cakumapeto kwa utumiki wake, Yesu anapempha Atate wake kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Nthawi yomweyo, Atate wake analankhula kucokela kumwamba ndi mawu omveka ngati kugunda kwa bingu kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”​—Yoh. 12:28.

10-11. (a) Kodi Yesu analilemekeza motani dzina la Yehova? (Onaninso cithunzi.) (b) N’cifukwa ciyani dzina la Yehova liyenela kuyeletsedwa ndi kukwezedwa?

10 Yesu nayenso analemekeza dzina la Atate wake. Motani? Njila imodzi anacitila zimenezo ndi kufotokozela ena makhalidwe ocititsa cidwi a Atate wake komanso zocita zake. Koma si zokhazi. Dzina la Yehova linafunikila kuyeletsedwa ndipo mbili yake inayenela kukwezedwa.b Yesu anaonetsa kufunika kwa zimenezi pomwe anaphunzitsa ophunzila ake pemphelo lacitsanzo. Anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.”​—Mat. 6:9.

11 N’cifukwa ciyani dzina la Yehova liyenela kuyeletsedwa ndi kukwezedwa? Cifukwa n’cakuti kalelo m’munda wa Edeni, Satana ananena mabodza ponena za Yehova Mulungu. Satana anati Yehova ndi wabodza komanso kuti anali kumana zabwino Adamu ndi Hava. (Gen. 3:​1-5) Satana ananenanso kuti Yehova samacita zinthu mwacilungamo. Mabodza a Satana anawononga mbili ya Yehova, kapena kuti dzina lake. Patapita nthawi m’masiku a Yobu, Satana ananenanso kuti atumiki a Yehova amam’tumikila, cabe cifukwa cofuna kupindulapo kenakake kwa iye. Munthu wabodza ameneyo anakambanso kuti anthu angasiye kutumikila Yehova akakumana ndi mavuto cifukwa samukonda kwenikweni Mulungu. (Yobu 1:​9-11; 2:4) Panafunika nthawi yokwanila yakuti wabodza aonekele pakati pa Yehova ndi Satana.

Yesu akucita ulaliki wake wa pa Phili ku khamu lalikulu la anthu.

Yesu anaphunzitsa otsatila ake kufunika koyeletsa dzina la Mulungu (Onani ndime 10)


“NDIKUPELEKA MOYO WANGA”

12. Kodi Yesu anali wokonzeka kucita ciyani cifukwa cokonda dzina la Yehova?

12 Cifukwa cakuti Yesu anali kukonda kwambili Yehova, anali kufuna kucita zonse zotheka kuti ayeletse ndi kukweza dzina la Yehova. Anati: “Ndikupeleka moyo wanga.” (Yoh. 10:​17, 18) Zoonadi, iye anali wokonzeka ngakhale kufa kaamba ka dzina la Yehova.c Anthu angwilo oyambilila, Adamu ndi Hava, anafulatila Yehova n’kukhala kumbali ya Satana. Koma mosiyana ndi zimenezi, Yesu anali wokonzeka kubwela padziko lapansi ndi kuonetsa kuti anali kum’kondadi Yehova. Yesu anacita zimenezi mwa kumvela Yehova pa ciliconse. (Aheb. 4:15; 5:​7-10) Iye anakhalabe wokhulupilika mpaka pamene anafa pa mtengo wozunzikilapo. (Aheb. 12:2) Mwa kutelo, iye anaonetsa kuti amakonda Yehova ndi dzina Lake.

13. N’cifukwa ciyani tingati Yesu anali pa malo abwino oonetsa kuti Satana ndi wabodza? (Onaninso cithunzi.)

13 Pa umoyo wake wonse, Yesu anaonetsa poyela kuti Satana ndiye wabodza osati Yehova. (Yoh. 8:44) Yesu anali kum’dziwa bwino Yehova kuposa aliyense. Ngati zimene Satana ananena zokhudza Yehova zinalidi zoona, Yesu akanatha kudziwa zimenezi. Yesu sanasunthike pokhalila kumbuyo mbili ya Yehova, kapena kuti dzina lake. Ngakhale pamene zinaoneka ngati Yehova wamusiya, Yesu anali wokonzeka kufa m’malo mofulatila Atate wake wacikondi.​—Mat. 27:46.d

Yesu ali pamtengo wozunzikilapo.

Umoyo wa Yesu unatsimikizila kothelatu kuti Satana ndiye wabodza, osati Yehova! (Onani ndime 13)


“NDAMALIZA KUGWILA NCHITO IMENE MUNANDIPATSA”

14. Kodi Yehova anamufupa motani Yesu cifukwa ca kukhulupilika kwake?

14 M’pemphelo limene Yesu anapeleka usiku woti mawa lake aphedwa, iye anati: “Ndamaliza kugwila nchito imene munandipatsa.” Iye anali ndi cidalilo cakuti Yehova adzam’fupa akakhalabe wokhulupilika. (Yoh. 17:​4, 5) Cidalilo ca Yesu mwa Atate wake sicinamugwilitse mwala. Yehova sanalole kuti Yesu akhalebe m’manda. (Mac. 2:​23, 24) Anamuukitsa ndi kum’patsa udindo wapamwamba kumwamba. (Afil. 2:​8, 9) Pambuyo pake, Yesu anayamba kulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kodi Ufumuwo unali kudzacita zotani? Mbali yaciwili ya pemphelo lake lacitsanzo imati: “Ufumu wanu ubwele, zofuna zanu [Yehova] zicitike pa dziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.”​—Mat. 6:10.

15. Kodi n’ciyaninso cina cimene Yesu adzacita?

15 Posacedwapa, Yesu adzawononga adani a Mulungu pa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:​14, 16; 19:​11-16) Posapita nthawi, Satana adzaponyedwa “m’phompho” mmene sadzatha kucita kena kalikonse. (Chiv. 20:​1-3) Yesu adzabwezeletsa mtendele ndi ungwilo ku mtundu wa anthu mu Ulamulilo wake wa Zaka 1,000. Adzaukitsa akufa. Adzacititsa dziko lonse kukhala paradaiso. Colinga ca Yehova cidzakwanilitsika!​—Chiv. 21:​1-4.

16. Kodi umoyo udzakhala bwanji kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000?

16 Kodi n’ciyani cidzacitika kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000. Ucimo ndi kupanda ungwilo zidzakhala zitatha. Anthu sadzafunikilanso kupempha kuti akhululukidwe pa maziko a dipo. Sadzafunikilanso mkhalapakati kapena ansembe. Ndipo “imfa nayonso, yomwe ndi mdani womaliza, idzawonongedwa.” Manda adzakhala opanda kanthu. Akufa adzakhala ataukitsidwa. Anthu onse padziko lapansi adzakhala angwilo.​—1 Akor. 15:​25, 26.

17-18. (a) N’ciyani cidzacitika kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000? (b) Kodi Yesu adzacita ciyani nthawi yake yolamulila ikadzatha? (1 Akorinto 15:​24, 28) (Onaninso cithunzi.)

17 N’ciyaninso cidzacitika kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000? Panthawiyo, cinthu cinacake capadela cidzacitika. Nkhani yokhudza kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova idzatha. Motani? M’munda wa Edeni, Satana anakamba kuti Yehova ndi wabodza komanso kuti salamulila anthu mwacilungamo. Kungocokela nthawiyo, dzina la Yehova lakhala likuyeletsedwa mobwelezabweleza ndi anthu amene amamulemekeza. Conco, kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000, mbili yake idzakwezedwa kothelatu. Adzakhala atatsimikizila mofikapo kuti ndi Tate wacikondi.

18 Zonse zimene Satana anakamba zidzaonekela poyela kuti n’zabodza. Kodi Yesu adzacita ciyani akadzamaliza kulamulila? Kodi adzatengela citsanzo ca Satana ndi kupandukila Yehova? Ayi! (Welengani 1 Akorinto 15:​24, 28.) Yesu adzabweza Ufumu kwa Atate wake. Adzakhala pansi pa ulamulilo wa Yehova. Inde, mosiyana ndi Satana, Yesu ndi wokonzeka kutula pansi udindo wake wonse cifukwa cokonda Yehova.

Yesu ali kumwamba akupeleka cisoti cacifumu kwa Yehova.

Yesu akubweza Ufumu kwa Atate wake kumapeto kwa Ulamulilo wake wa Zaka 1,000 (Onani ndime 18)


19. Kodi dzina la Yehova ndi lofunika motani kwa Yesu?

19 M’pake kuti Yehova anapatsa Yesu dzina lake. Yesu waonetsa kuti ndi woimilako wabwino koposa wa Atate wake. Conco kodi dzina la Yehova ndi lofunika motani kwa Yesu? Ndi lofunika kwambili kuposa cina ciliconse. Anali wokonzeka kufa cifukwa ca dzinalo ndipo mofunitsitsa adzabweza zonse kwa Yehova kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka Cikwi. Kodi tingatengele bwanji citsanzo cake? Tidzakambilana funso limeneli m’nkhani yotsatila.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yesu analidziwikitsa motani dzina la Yehova kwa ophunzila ake?

  • Kodi Yesu anapatsidwa dzina la Yehova m’lingalilo lotani?

  • Kodi Yesu anali wokonzeka kucita ciyani cifukwa ca dzina la Yehova? Nanga n’cifukwa ciyani?

NYIMBO 16 Tamandani Ya Kaamba ka Mwana Wake Wodzozedwayo

a Nthawi zina, angelo naonso anali kuimilako Yehova popeleka mauthenga m’dzina lake. Ici ndiye cifukwa cake nthawi zina Baibo imanena kuti Yehova ndiye anali kulankhula pomwe m’ceniceni mngelo womuimilako ndiye anali kulankhula. (Gen. 18:​1-33) Ngakhale kuti Malemba amanena kuti Mose analandila Cilamulo kucokela kwa Yehova, mavesi ena amaonetsa kuti Yehova anagwilitsa nchito angelo popeleka Cilamuloco m’dzina lake.​—Lev. 27:34; Mac. 7:​38, 53; Agal. 3:19; Aheb. 2:​2-4.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Kuyeletsa” kumatanthauza kupangitsa cinthu kukhala cosadetsedwa kapena kuciona kuti n’copatulika. “Kukweza” kungatanthauze kutsimikizila kuti zimene munthu anacita n’zoyenela ndi kupeleka umboni wakuti alibe mlandu.

c Imfa ya Yesu inatsegulila khomo mtundu wa anthu wokakhala ndi moyo wosatha.

d Onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Mlonda ya April 2021, mas. 30-31.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani