NKHANI YOPHUNZILA 44
NYIMBO 138 Kukongola kwa Imvi
Khalanibe Acimwemwe mu Ukalamba Wanu
“ Ngakhale atakalamba zinthu zidzapitilizabe kuwayendela bwino.”—SAL. 92:14.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tiona cifukwa cake n’kofunika kuti acikulile akhalebe acimwemwe. Tionanso zimene angacite kuti akhalebe acimwemwe.
1-2. Kodi Yehova amawaona motani okalamba okhulupilika? (Salimo 92:12-14; onaninso cithunzi.)
ZUNGULILE dziko lapansi, anthu amauona mosiyana-siyana ukalamba. Ena amanyadila kukhala okalamba, pomwe ena amacita zonse zotheka kuti asaoneke kuti ndi okalamba. Mwacitsanzo, akangoona kaimvi amakazula. Koma mulimonse mmene angacitile, ukalamba sangaupewe.
2 Komabe, Yehova amawaona mosiyana atumiki ake omwe akukalamba. (Miy. 16:31) Iye amawayelekezela ndi mitengo yokongola. (Welengani Salimo 92:12-14.) N’cifukwa ciani kuyelekezelaku n’koyenela? Cifukwa n’cakuti nthawi zambili, mitengo imene yakhala zaka zambili-mbili imakhala ndi masamba komanso maluwa oculuka. Mwacitsanzo, ku Japan kuli mitengo ina imene imakhala zaka zambili. Ina mwa mitengoyo yakhala zaka zoposa 1,000, ndipo nthawi zambili mitengo yotelo ndi imene imakhala yokongola kwambili. Mofanana ndi mitengo imene yakhala zaka zambili, Akhristu okalamba amaonedwa kuti ndi okongola, maka-maka ndi Yehova. Yehova amaona umunthu wao wamkati, ndipo amanyadila akaona kupilila ndi kukhulupilika kwao, komanso kuculuka kwa zaka zimene akhala akum’tumikila.
Okalamba ali ngati mitengo imene yakhala zaka zambili. Ndi okongola ndipo amapitilizabe kubala zipatso (Onani ndime 2)
3. Pelekani citsanzo coonetsa kuti Yehova wakhala akugwilitsila nchito okalamba pokwanilitsa cifunilo cake.
3 Munthu akakalamba, Yehova samuona kuti wayamba kutha nchito.a Nthawi zambili, Yehova wakhala akusewenzetsa acikulile pokwanilitsa cifunilo cake. Mwacitsanzo, Sara anali wokalamba pomwe Yehova anamuuza kuti adzakhala mai wa mtundu waukulu komanso kholo la Mesiya. (Gen. 17:15-19) Mose anali wacikulile pomwe Yehova anam’patsa nchito yotulutsa Aisiraeli mu Iguputo. (Eks. 7:6, 7) Nayenso mtumwi Yohane anali wokalamba pamene Yehova anamuuzila kulemba mabuku asanu a m’Baibo.
4. Mogwilizana ndi Miyambo 15:15, n’ciani cingathandize okalamba kupilila mabvuto amene amakumana nao? (Onaninso cithunzi.)
4 Acikulile amakumana ndi mabvuto ambili obwela cifukwa ca ukalamba. Mlongo wina anati: “Ukalamba si cinthu ca masewela.” Koma kukhala acimwemweb kungathandize acikulile kupilila mabvuto a mu ukalamba wao. (Welengani Miyambo 15:15.) M’nkhani ino, tikambilana zimene acikulile angacite kuti akhalebe acimwemwe. Tikambilanenso zimene ena angacite kuti athandize okalamba mumpingo wao. Coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake kukhala acimwemwe kungakhale kobvuta tikamakalamba.
Mtima wacimwemwe ungathandize okalamba kupilila mabvuto obwela cifukwa ca ukalamba (Onani ndime 4)
CIFUKWA CAKE ZINGAKHALE ZOBVUTA KUKHALABE ACIMWEMWE MU UKALAMBA
5. N’ciani cingapangitse okalamba ena kukhala osasangalala?
5 Kodi n’ciani cingapangitse kuti musakhale acimwemwe? Mwina n’cifukwa cakuti simukwanitsanso kucita zinthu zina zimene munali kucita kale. Mungamalake-lake masiku akale pomwe munali wacinyamata ndi wathanzi. (Mlal. 7:10) Mwacitsanzo, mlongo wina wacikulile, dzina lake Ruby, anakamba kuti: “Kubvala kumandibvuta cifukwa ca kuphwanya kwa thupi, komanso cifukwa cobvutika kutambasula manja ndi miyendo. Ngakhale kunyamula phazi kuti ndibvale sokosi kumandibvuta. Manja anga amawawa kwambili ndipo zala zanga zinacita dzanzi. Conco, zimakhala zobvuta kuti ndicite zinthu ngakhale zazing’ono.” Nayenso Harold, amene anatumikilako pa Beteli, anati: “Nthawi zina ndimakhumudwa cifukwa colephela kucita zinthu zimene kale ndinali kusangalala nazo. N’nali ndi mphamvu ndili wacinyamata, ndipo n’nali kukonda kuchaya bola. Anthu anali kunena kuti, ‘Patsilani Harold bola. Mukatelo, tidzapambana.’ Koma tsopano ndiganiza kuti sindingathenso kucita zimenezo ngakhale pang’ono.”
6. (a) Ndi zinthu zina ziti zimene zingapangitse okalamba kukhala opanda cimwemwe? (b) N’ciani cingathandize acikulile kudziwa ngati afunikila kuleka kuyendetsa galimoto? (Onani nkhani m’magazini ino, ya mutu wakuti “Kodi Ndileke Kuyendetsa Galimoto?”)
6 Nthawi zina, mungataye mtima poona kuti mukulephela kucita zinthu zina panokha. Izi zingakhale telo maka-maka ngati pakufunikila wina woti azikusamalilani, kapena ngati mukufunikila kusamuka kuti mwana wanu azikakusamalilani. Mwinanso mungakhumudwe kwambili cifukwa codwala-dwala, kapena cifukwa coti simuona bwino moti simungathenso kuyenda panokha kapena kuyendetsa galimoto. Zimenezi zingakhaledi zodandaulitsa! Koma kumbukilani kuti ngakhale pamene simukuthanso kudzisamalila, kukhala panokha, kapena kuyendetsa galimoto, Yehova komanso anthu ena amakuonani kuti ndinu amtengo wapatali. Ndipo dziwani kuti Yehova amamvetsa mmene mukumvela. Cofunika kwambili kwa Yehova ndi cikondi canu pa iye komanso pa abale ndi alongo. Izi n’zimene zimapangitsa Yehova kukuonani kuti ndinu wofunika.—1 Sam. 16:7.
7. N’ciani cingathandize amene amakhumudwa poganiza kuti mapeto adzafika iwo atafa?
7 Mwinanso mungakhale wokhumudwa poganiza kuti mwina mudzamwalila mapeto a dongosolo lino la zinthu asanafike. Ngati mumamva conco, n’ciani cingakuthandizeni? Muzikumbukila kuti Yehova amafuna kuononga dziko loipali, koma pali cifukwa cabwino cimene akulezela mtima. (Yes. 30:18) Yehova akuleza mtima pofuna kupatsa anthu mamiliyoni mwai wakuti aphunzile za iye ndi kukhala mabwenzi ake. (2 Pet. 3:9) Conco, mukalefuka poganizila za mapeto, muzikumbukila kuti pali anthu ambili amene afunika kudziwa Yehova mapeto asanafike kuti akapulumuke. Adziwa ndani, mwina ena mwa iwo angakhale a m’banja lanu!
8. Kodi kudwala kungapangitse okalamba kucita ciani?
8 Mosasamala kanthu za msinkhu wathu, ngati tikudwala, n’capafupi kukamba mau kapena kucita zinthu zimene tingadziimbe nazo mlandu pambuyo pake. (Mlal. 7:7; Yak. 3:2) Mwacitsanzo, pamene munthu wokhulupilika Yobu anali kubvutika, analankhula “mosaganiza bwino.” (Yobu 6:1-3) Naonso acikulile angakambe mau kapena kucita zinthu zimene sakanatelo akanakhala kuti si odwala. Ngakhale n’telo, kudwala kapena ukalamba sikuyenela kutipangitsa kucitila ena zinthu mosakoma mtima kapena kuyembekezela kuti nthawi zonse anthu ena aziticitila zinazake. Ndipo tikazindikila kuti talankhula zinthu zimene zakhumudwitsa winawake, tiyenela kupepesa mwamsanga.—Mat. 5:23, 24.
MMENE MUNGAKHALILEBE ACIMWEMWE
Mungatani kuti mukhalebe acimwemwe ngakhale kuti mukukumana ndi mabvuto a ukalamba? (Onani ndime 9-13)
9. N’cifukwa ciani muyenela kulandila thandizo locokela kwa ena? (Onaninso zithunzi.)
9 Landilani thandizo locokela kwa ena. (Agal. 6:2) Nthawi zina, kucita izi kungakhale kobvuta. Mlongo Gretl anati: “Nthawi zina zimandibvuta kupempha thandizo kwa ena cifukwa coganiza kuti ndingakhale mtolo kwa iwo. Zinanditengela nthawi kuti ndisinthe maganizo anga ndi kubvomeleza modzicepetsa kuti ndikufunikila thandizo.” Mukalandila thandizo kwa ena, mumawapatsa mwai wokhala ndi cimwemwe cobwela cifukwa ca kupatsa. (Mac. 20:35) Ndipo mudzasangalala kudziwa kuti ena amakukondani kwambili komanso kuti amakuganizilani.
(Onani ndime 9)
10. N’cifukwa ciani muyenela kukumbukila kumayamikila thandizo la ena? (Onaninso zithunzi.)
10 Khalani oyamikila. (Akol. 3:15; 1 Ates. 5:18) Ngati ena aticitila zinthu zabwino, tingayamikile camumtima, koma nthawi zina tingaiwale kuwauza kuti tayamikila. Koma tikamwetulila n’kuwauza kuti zikomo, timawapangitsa kuona kuti ndi ofunika ndiponso kuti timayamikila thandizo lao. Leah, amene amasamalila okalamba pa Beteli, anati: “Mmodzi mwa alongo amene ndimasamalila amandilembela pa kapepala mau oyamikila. Mauwo amakhala aafupi, koma amakhala olimbikitsa kwambili. Ndimakonda kuwawelenga, ndipo ndimakondwela kudziwa kuti iye amayamikila thandizo langa.”
(Onani ndime 10)
11. Kodi mungawathandize bwanji anthu ena? (Onaninso zithunzi.)
11 Muziyesetsa kuthandiza ena. Mukamathela nthawi komanso mphamvu zanu kuthandiza ena, mudzapewa kumangoganizila za mabvuto anu. Mwambi wina wa mu Africa umayelekezela acikulile ndi laibulale yokhala ndi mabuku ambili odzala ndi nzelu. Koma mabuku omwe ali pa shelufu sangaphunzitse munthu kapena kusimba nkhani. Mofananamo, anthu ocepelapo msinkhu pa inu sangaphunzile zilizonse kwa inu ngati simuwauza kapena kuwafotokozela zinthu zina zomwe mudziwa. Conco, muziwafunsa mafunso ndi kuwamvetsela. Afotokozeleni mmene Yehova wakuthandizilani pa umoyo wanu komanso mmene kumvela Yehova kungawathandizile kukhala osangalala. Mosakaikila, mudzakhala acimwemwe mukamatonthoza mabwenzi anuwo ndi kuwalimbikitsa.—Sal. 71:18.
(Onani ndime 11)
12. Mogwilizana ndi Yesaya 46:4, kodi Yehova akulonjeza kuti adzacita ciani kwa okalamba? (Onaninso zithunzi.)
12 Pemphelani kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Nthawi zina mungalefuke. Koma muzikumbukila kuti Yehova “satopa kapena kufooka.” (Yes. 40:28) Kodi Yehova amazisewenzetsa bwanji mphamvu zake zopanda malile? Njila imodzi ndi kulimbikitsa atumiki ake okalamba okhulupilika. (Yes. 40:29-31) N’cifukwa cake iye anawalonjeza kuti adzawathandiza. (Welengani Yesaya 46:4.) Ndipo Yehova nthawi zonse amakwanilitsa malonjezo ake. (Yos. 23:14; Yes. 55:10, 11) Mukapemphela ndi kuona mmene Yehova akukuonetselani cikondi cake, mudzakhala osangalala.
(Onani ndime 12)
13. Mogwilizana ndi 2 Akorinto 4:16-18, kodi tiyenela kukumbukila ciani? (Onaninso zithunzi.)
13 Muzikumbukila kuti posacedwapa mudzakhalanso ndi thanzi labwino. Tikadziwa kuti bvuto linalake ndi lakanthawi, tingalipilile mosabvuta. Baibo imatitsimikizila kuti posacedwa anthu sadzakalambanso kapena kudwala. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) M’malo mongomaganizila masiku akale, mungakhale acimwemwe podziwa kuti zabwino zili mtsogolo. (Welengani 2 Akorinto 4:16-18.) Koma kodi ena angathandize motani?
(Onani ndime 13)
MMENE TINGAWATHANDIZILE
14. N’cifukwa ciani n’kofunika kuwayendela okalamba ndi kuwatumila foni?
14 Muziwayendela kawili-kawili ndi kuwatumila foni. (Aheb. 13:16) Nthawi zina, acikulile amakhala osungulumwa. M’bale Camille, amene sacoka panyumba, anati: “Ndimakhala m’nyumba kucokela m’mawa mpaka madzulo. Conco, ndimasungulumwa zedi. Ndipo ndimakhala ndi nkhawa komanso ndimakhumudwa podziwa kuti palibe cimene ndingacite.” Tikayendela okalamba, amadziwa kuti ndi ofunika kwa ife ndiponso kuti timawakonda. Mwacionekele, tonsefe zinaticitikilapo kuti tinafuna kutumila foni wokalamba wina wa mumpingo mwathu koma tinalephela. Izi zingacitike cifukwa timakhala ndi zocita zambili mu umoyo. Nanga mungatani kuti “muzitsimikizila zinthu zofunika kwambili,” zimene zikuphatikizapo kuyendela okalamba? (Afil. 1:10) Mungalembe maina a okalamba a mumpingo mwanu ndi tsiku limene mudzawatumila foni kapena kuwalembela meseji. Cinanso, mungacite bwino kusankhilatu tsiku lokawayendela kuti musakaiwale kupita.
15. Kodi ndi zinthu ziti zimene acinyamata ndi acikulile angacitile limodzi?
15 Ngati ndinu wacicepele, mwina mungade nkhawa posadziwa zimene mungakambe kapena kucita pamene muli ndi acikulile. Koma simuyenela kutelo. Mungokhala bwenzi labwino. (Miy. 17:17) Muzilankhula ndi acikulile misonkhano ya mpingo isanayambe kapena ikatha. Mwinanso mungawapemphe kuti akuchulilen’koni lemba lao lapamtima kapena akuuzen’koni cinacake coseketsa cimene anacita pa ubwana wao. Mungawapemphe kuti muonelele nao limodzi pulogilamu ya JW Broadcasting®. Koma palinso njila zina zimene mungawathandizile acikulile. Mwacitsanzo, mungawathandize kucita apudeti zipangizo zao kapena kucita daunilodi zofalitsa zatsopano zophunzilila. Mlongo wina, dzina lake Carol, anati: “Ngakhale kuti ndine wacikulile, ndimafuna kusangalalabe ndi moyo. Ndimakonda kukagula zinthu, kupita kokadya ndi ena, ndi kusangalala ndi cilengedwe. Conco, muzicita nao zinthu zimene mumakonda acikulile.” Mlongo wina, dzina lake Maira, anati: “Mmodzi mwa mabwenzi anga ali ndi zaka 90, koma ine ndili ndi zaka 33 cabe. Komabe, ndimaiwalako zoti ndi aakulu, cifukwa timaseka ndi kuonelela limodzi mafilimu. Ndipo tikakumana ndi mabvuto, timathandizana.”
16. N’cifukwa ciani tiyenela kupelekeza acikulile kucipatala?
16 Muziwapelekeza kucipatala. Kuonjezela pa kupeleka thandizo la mayendedwe, muyenela kuonetsetsa kuti madokotala akuwasamalila bwino acikulile komanso akuwapatsa thandizo lowayenelela. (Yes. 1:17) Mungathandizenso acikulile mwa kulemba zimene dokotala wakamba. Mlongo wina, dzina lake Ruth, anati: “Nthawi zambili ndikapita ndekha kucipatala, madokotala samakhulupilila zimene ndawauza. Iwo amanena mau monga akuti, ‘Si ndinu wodwala. Mukungoganizila kuti ndinu wodwala.’ Koma ndikapita ndi winawake, madokotala amandisamalila bwino. Ndimayamikila abale ndi alongo amene amandipelekeza kucipatala.”
17. Kodi ndi mbali ziti za utumiki zimene mungaciteko nao okalamba?
17 Muzilalikila nao. Okalamba ena sangakhale ndi mphamvu zolalikila khomo ndi khomo. Conco, bwanji osapempha mlongo wacikulile kuti akakhale nanu pa ulaliki wapoyela? Mungam’bweletsele mpando kuti akhalepo. Kapena mungapemphe m’bale wacikulile kuti mukhale naye potsogoza phunzilo lanu la Baibo. Mwinanso mungakatsogozele kunyumba kwake. Akulu angakonze zoti kukumana kokonzekela utumiki kuzicitikila kunyumba ya okalamba n’colinga coti okalambawo azitengamo mbali mosabvuta. Yehova amakondwela tikacita zonse zotheka kuti tionetse cikondi ndi ulemu kwa okalamba.—Miy. 3:27; Aroma 12:10.
18. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
18 Takumbutsidwa kuti Yehova amawakonda okalamba ndipo amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Ndi mmenenso tonse mumpingo timawaonela. Ngakhale kuti ukalamba ndi wobvuta, mwa thandizo la Yehova, mungakhalebe acimwemwe. (Sal. 37:25) N’zosangalatsa kwambili kudziwa kuti zabwino zili mtsogolo, osati kumbuyo! Koma bwanji kwa inu amene mukusamalila okalamba, mwana kapena bwenzi limene likudwala? Mungacite ciani kuti mukhalebe acimwemwe? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
a Onelelani vidiyo yakuti Acikulile—Ndinu Ofunika Kwambili, pa jw.org ndi pa JW Library®
b KUFOTOKOZELA MAU ENA: Cimwemwe ndi khalidwe limene mzimu wa Mulungu umabala. (Agal. 5:22) Kuti tikhale ndi cimwemwe ceni-ceni tifunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.